< ישעה 57 >
הצדיק אבד ואין איש שם על לב ואנשי חסד נאספים באין מבין כי מפני הרעה נאסף הצדיק׃ | 1 |
Anthu olungama amafa, ndipo palibe amene amalingalira mu mtima mwake; anthu odzipereka amatengedwa, ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake. Anthu olungama amatengedwa kuti tsoka lisawagwere.
יבוא שלום ינוחו על משכבותם הלך נכחו׃ | 2 |
Iwo amene amakhala moyo wolungama amafa mwamtendere; amapeza mpumulo pamene agona mu imfa.
ואתם קרבו הנה בני עננה זרע מנאף ותזנה׃ | 3 |
“Bwerani kuno, anthu ochita zoyipa, inu muli ngati zidzukulu za mkazi wachigololo ndi wadama!
על מי תתענגו על מי תרחיבו פה תאריכו לשון הלוא אתם ילדי פשע זרע שקר׃ | 4 |
Kodi inu mukuseka yani? Kodi mukumunena ndani ndi kupotoza pakamwa panu? Kodi inu si ana owukira, zidzukulu za anthu abodza?
הנחמים באלים תחת כל עץ רענן שחטי הילדים בנחלים תחת סעפי הסלעים׃ | 5 |
Inu mumapembedza mafano pamene mumalobodoka ndi zilakolako zanu pakati pa mitengo ya thundu, ndiponso pa tsinde pa mtengo uliwonse wa nthambi zambiri. Mumapereka ana anu ngati nsembe mu zigwa ndiponso mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.
בחלקי נחל חלקך הם הם גורלך גם להם שפכת נסך העלית מנחה העל אלה אנחם׃ | 6 |
Mafano a pakati pa miyala yosalala ya mu zigwa ndiye chuma chanu. Inde, ndiye gawo lanu. Mumapereka chopereka cha chakumwa kwa mafanowo, ndipo mumaperekanso chopereka cha chakudya. Kodi zimenezi zingandichititse kuti ndikukomereni mtima?
על הר גבה ונשא שמת משכבך גם שם עלית לזבח זבח׃ | 7 |
Inu munayiwala bedi lanu pa phiri lalitali ndi looneka kutali. Mumapita kumeneko kukapereka nsembe zanu.
ואחר הדלת והמזוזה שמת זכרונך כי מאתי גלית ותעלי הרחבת משכבך ותכרת לך מהם אהבת משכבם יד חזית׃ | 8 |
Mʼnyumba mwanu mwayika mafano kuseri kwa zitseko ndiponso pa mphuthu. Mwandisiya Ine, mwavula zovala zanu. Bedi lanu mwalikulitsa ndipo mwakwera ndi zibwenzi zanu, ndiye mwazilipira kuti mugone nazo. Kumene mwakwaniritsa zilakolako zanu zoyipa.
ותשרי למלך בשמן ותרבי רקחיך ותשלחי צריך עד מרחק ותשפילי עד שאול׃ (Sheol ) | 9 |
Mumapita kukapembedza fano la Moleki mutatenga mafuta ndi zonunkhira zochuluka. Munachita kutumiza akazembe anu kutali; inu ngakhale munapita ku manda kwenikweniko! (Sheol )
ברב דרכך יגעת לא אמרת נואש חית ידך מצאת על כן לא חלית׃ | 10 |
Inu mumatopa ndi maulendo anu, koma simunathe kunena kuti, ‘Nʼzopanda phindu.’ Munapezako kumeneko zokhumba zanu nʼchifukwa chake simunalefuke.
ואת מי דאגת ותיראי כי תכזבי ואותי לא זכרת לא שמת על לבך הלא אני מחשה ומעלם ואותי לא תיראי׃ | 11 |
“Kodi ndani amene mwachita naye mantha ndi kumuopa, kotero kuti mwakhala mukundinamiza, ndipo Ine simundikumbukira nʼkomwe, kapena kuganizirapo mʼmitima yanu za Ine? Kodi mwaleka kundiopa chifukwa choti ndakhala chete nthawi yayitali?
אני אגיד צדקתך ואת מעשיך ולא יועילוך׃ | 12 |
Koma ndaonetsa poyera ntchito zanu zomwe mumati nʼzolungama, ndi mafano anu kuti nʼzosathandiza.
בזעקך יצילך קבוציך ואת כלם ישא רוח יקח הבל והחוסה בי ינחל ארץ ויירש הר קדשי׃ | 13 |
Pamene mufuwula kupempha thandizo, mafano anu amene munasonkhanitsawo ndiyetu akupulumutseni! Mphepo idzanyamula mafano anu onsewo, mpweya chabe udzawulutsa mafanowo. Koma munthu amene amadalira ine adzalandira dziko lokhalamo. Phiri langa lopatulika lidzakhala lakelake.”
ואמר סלו סלו פנו דרך הרימו מכשול מדרך עמי׃ | 14 |
Ndipo panamveka mawu akuti, “Undani, undani, konzani msewu! Chotsani zotchinga pa njira yoyendamo anthu anga.”
כי כה אמר רם ונשא שכן עד וקדוש שמו מרום וקדוש אשכון ואת דכא ושפל רוח להחיות רוח שפלים ולהחיות לב נדכאים׃ | 15 |
Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.
כי לא לעולם אריב ולא לנצח אקצוף כי רוח מלפני יעטוף ונשמות אני עשיתי׃ | 16 |
Sindidzawatsutsa anthu mpaka muyaya kapena kuwapsera mtima nthawi zonse, popeza kuti ndinalenga anthu anga ndi kuwapatsa mpweya wamoyo.
בעון בצעו קצפתי ואכהו הסתר ואקצף וילך שובב בדרך לבו׃ | 17 |
Ine ndinakwiya kwambiri chifukwa cha tchimo lawo ladyera; ndinawalanga ndi kuwafulatira mokwiya, koma iwo anapitirirabe kuchita ntchito zawo zoyipa.
דרכיו ראיתי וארפאהו ואנחהו ואשלם נחמים לו ולאבליו׃ | 18 |
Ndaona zochita zawo, komabe ndidzawachiritsa; kuwapumulitsa ndi kuwapatsa mtendere,
בורא נוב שפתים שלום שלום לרחוק ולקרוב אמר יהוה ורפאתיו׃ | 19 |
anthu olira a mu Israeli adzanditamanda ndi milomo yawo. Anthu amene ali kutali ndi apafupi pomwe ndidzawapatsa mtendere,” “Ndipo ndidzawachiritsa.” Akutero Yehova.
והרשעים כים נגרש כי השקט לא יוכל ויגרשו מימיו רפש וטיט׃ | 20 |
Koma anthu oyipa ali ngati nyanja yowinduka, yosatha kukhala bata, mafunde ake amaponya matope ndi ndere.
אין שלום אמר אלהי לרשעים׃ | 21 |
“Palibe mtendere kwa oyipa,” akutero Mulungu wanga.