< ישעה 56 >

כה אמר יהוה שמרו משפט ועשו צדקה כי קרובה ישועתי לבוא וצדקתי להגלות׃ 1
Yehova akuti, “Chitani chilungamo ndi zinthu zabwino, chifukwa chipulumutso changa chili pafupi ndipo ndidzakuwombolani posachedwapa.
אשרי אנוש יעשה זאת ובן אדם יחזיק בה שמר שבת מחללו ושמר ידו מעשות כל רע׃ 2
Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi, munthu amene amalimbika kuzichita, amene amasunga Sabata osaliyipitsa, ndipo amadziletsa kuchita zoyipa.”
ואל יאמר בן הנכר הנלוה אל יהוה לאמר הבדל יבדילני יהוה מעל עמו ואל יאמר הסריס הן אני עץ יבש׃ 3
Mlendo amene waphatikana ndi Yehova asanene kuti, “Ndithu Yehova wandichotsa pakati pa anthu ake.” Ndipo munthu wofulidwa asanene kuti, “Ine ndine mtengo wowuma basi.”
כי כה אמר יהוה לסריסים אשר ישמרו את שבתותי ובחרו באשר חפצתי ומחזיקים בבריתי׃ 4
Popeza Yehova akuti, “Wofulidwa amene amasunga masabata anga, nachita zokomera Ine ndi kusunga pangano langa,
ונתתי להם בביתי ובחומתי יד ושם טוב מבנים ומבנות שם עולם אתן לו אשר לא יכרת׃ 5
ndidzawapatsa dzina ndi mbiri yabwino mʼkati mwa Nyumba yanga ndi makoma ake, kuposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi. Ndidzawapatsa dzina labwino, losatha ndi losayiwalika.”
ובני הנכר הנלוים על יהוה לשרתו ולאהבה את שם יהוה להיות לו לעבדים כל שמר שבת מחללו ומחזיקים בבריתי׃ 6
Yehova akuti, “Alendo amene amadziphatika kwa Yehova, motero kuti amamutumikira Iye, amakonda dzina la Yehova, amamugwirira ntchito, komanso kusunga Sabata osaliyipitsa ndi kusunga bwino pangano langa,
והביאותים אל הר קדשי ושמחתים בבית תפלתי עולתיהם וזבחיהם לרצון על מזבחי כי ביתי בית תפלה יקרא לכל העמים׃ 7
amenewa Ine ndidzawafikitsa ku phiri langa lopatulika, ndidzawapatsa chimwemwe mʼnyumba yanga ya mapemphero. Zopereka zawo zopsereza ndi nsembe zawo ndidzazilandira pa guwa langa la nsembe. Paja nyumba yanga idzatchedwa nyumba ya mapemphero ya anthu a mitundu yonse.”
נאם אדני יהוה מקבץ נדחי ישראל עוד אקבץ עליו לנקבציו׃ 8
Ambuye Yehova, amene amasonkhanitsa Aisraeli onse ali ku ukapolo akunena kuti, “Ndidzasonkhanitsano anthu ena kuwonjezera amene anasonkhana kale.”
כל חיתו שדי אתיו לאכל כל חיתו ביער׃ 9
Bwerani, inu zirombo zonse zakuthengo, inu nonse zirombo zamʼnkhalango bwerani mudzadye!
צפו עורים כלם לא ידעו כלם כלבים אלמים לא יוכלו לנבח הזים שכבים אהבי לנום׃ 10
Atsogoleri onse a Israeli ndi akhungu, onse ndi opanda nzeru; onse ndi agalu opanda mawu, samatha kuwuwa: amagona pansi nʼkumalota amakonda kugona tulo.
והכלבים עזי נפש לא ידעו שבעה והמה רעים לא ידעו הבין כלם לדרכם פנו איש לבצעו מקצהו׃ 11
Ali ngati agalu amene ali ndi njala yayikulu; sakhuta konse. Abusa nawonso samvetsa zinthu; onse amachita monga akufunira, aliyense amafunafuna zomupindulitsa iye mwini.
אתיו אקחה יין ונסבאה שכר והיה כזה יום מחר גדול יתר מאד׃ 12
Aliyense amafuwulira mnzake kuti, “Bwera, tiye timwe vinyo! Tiyeni timwe mowa mpaka kukhuta! Mawa lidzakhala ngati leroli, kapena kuposa lero lino.”

< ישעה 56 >