< ישעה 55 >

הוי כל צמא לכו למים ואשר אין לו כסף לכו שברו ואכלו ולכו שברו בלוא כסף ובלוא מחיר יין וחלב׃ 1
“Bwerani, inu nonse amene muli ndi ludzu, bwerani madzi alipo; ndipo inu amene mulibe ndalama bwerani, mudzagule chakudya kuti mudye! Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka osalipira ndalama, osalipira chilichonse.
למה תשקלו כסף בלוא לחם ויגיעכם בלוא לשבעה שמעו שמוע אלי ואכלו טוב ותתענג בדשן נפשכם׃ 2
Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene samadya, ndipo mukuwononga malipiro anu pa zinthu zimene sizikhutitsa? Tamverani, mvetsetsani zimene ndikunena kuti mudye zimene zili zabwino; ndipo mudzisangalatse.
הטו אזנכם ולכו אלי שמעו ותחי נפשכם ואכרתה לכם ברית עולם חסדי דוד הנאמנים׃ 3
Tcherani makutu ndipo mubwere kwa Ine; mvereni Ine, kuti mukhale ndi moyo. Ndidzachita nanu pangano losatha, chikondi changa chija chosasinthika ndi chodalirika ndinalonjeza Davide.
הן עד לאומים נתתיו נגיד ומצוה לאמים׃ 4
Taonani, ine ndamusankha kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu, kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira mitundu ya anthu.
הן גוי לא תדע תקרא וגוי לא ידעוך אליך ירוצו למען יהוה אלהיך ולקדוש ישראל כי פארך׃ 5
Ndithu inu mudzayitanitsa mitundu ya anthu imene simuyidziwa, ndipo mitundu ya anthu imene sikudziwani idzabwera ndi liwiro kwa inu. Izi zidzatero chifukwa Yehova Mulungu wanu, Woyerayo wa Israeli, wakuvekani ulemerero.”
דרשו יהוה בהמצאו קראהו בהיותו קרוב׃ 6
Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka. Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.
יעזב רשע דרכו ואיש און מחשבתיו וישב אל יהוה וירחמהו ואל אלהינו כי ירבה לסלוח׃ 7
Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa, ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa. Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo, ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.
כי לא מחשבותי מחשבותיכם ולא דרכיכם דרכי נאם יהוה׃ 8
“Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu, ngakhale njira zanu si njira zanga,” akutero Yehova.
כי גבהו שמים מארץ כן גבהו דרכי מדרכיכם ומחשבתי ממחשבתיכם׃ 9
“Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
כי כאשר ירד הגשם והשלג מן השמים ושמה לא ישוב כי אם הרוה את הארץ והולידה והצמיחה ונתן זרע לזרע ולחם לאכל׃ 10
Monga mvula ndi chisanu chowundana zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko koma zimathirira dziko lapansi. Ndipo zimameretsa ndi kukulitsa zomera kenaka nʼkupatsa mlimi mbewu ndi chakudya.
כן יהיה דברי אשר יצא מפי לא ישוב אלי ריקם כי אם עשה את אשר חפצתי והצליח אשר שלחתיו׃ 11
Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.
כי בשמחה תצאו ובשלום תובלון ההרים והגבעות יפצחו לפניכם רנה וכל עצי השדה ימחאו כף׃ 12
Inu mudzatuluka mu mzindawo mwachimwemwe ndipo adzakutsogolerani mwamtendere; mapiri ndi zitunda zidzakuyimbirani nyimbo, ndipo mitengo yonse yamʼthengo idzakuwombereni mʼmanja.
תחת הנעצוץ יעלה ברוש תחת הסרפד יעלה הדס והיה ליהוה לשם לאות עולם לא יכרת׃ 13
Mʼmalo mʼmene tsopano muli mitengo ya minga mudzamera mitengo ya payini, ndipo kumene kuli mkandankhuku kudzamera mchisu. Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Yehova, ngati chizindikiro chamuyaya, chimene sichidzafafanizika konse.”

< ישעה 55 >