< ישעה 5 >

אשירה נא לידידי שירת דודי לכרמו כרם היה לידידי בקרן בן שמן׃ 1
Ndidzamuyimbira bwenzi langa nyimbo yokamba za munda wake wa mpesa: Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa pa phiri la nthaka yachonde.
ויעזקהו ויסקלהו ויטעהו שרק ויבן מגדל בתוכו וגם יקב חצב בו ויקו לעשות ענבים ויעש באשים׃ 2
Anatipula nachotsa miyala yonse ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri. Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo. Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino, koma ayi, unabala mphesa zosadya.
ועתה יושב ירושלם ואיש יהודה שפטו נא ביני ובין כרמי׃ 3
“Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda, weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu.
מה לעשות עוד לכרמי ולא עשיתי בו מדוע קויתי לעשות ענבים ויעש באשים׃ 4
Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesa kupambana chomwe ndawuchitira kale? Pamene ndinkayembekezera kuti udzabala mphesa zabwino, bwanji unabala mphesa zosadya?
ועתה אודיעה נא אתכם את אשר אני עשה לכרמי הסר משוכתו והיה לבער פרץ גדרו והיה למרמס׃ 5
Tsopano ndikuwuzani chimene ndidzawuchitire munda wanga wa mpesa: ndidzachotsa mpanda wake, ndipo mundawo udzawonongeka; ndidzagwetsa khoma lake, ndipo nyama zidzapondapondamo.
ואשיתהו בתה לא יזמר ולא יעדר ועלה שמיר ושית ועל העבים אצוה מהמטיר עליו מטר׃ 6
Ndidzawusandutsa tsala, udzakhala wosatengulira ndi wosalimira ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina. Ndidzalamula mitambo kuti isagwetse mvula pa mundapo.”
כי כרם יהוה צבאות בית ישראל ואיש יהודה נטע שעשועיו ויקו למשפט והנה משפח לצדקה והנה צעקה׃ 7
Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonse ndi Aisraeli, ndipo anthu a ku Yuda ndiwo minda yake yomukondweretsa. Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana; mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika.
הוי מגיעי בית בבית שדה בשדה יקריבו עד אפס מקום והושבתם לבדכם בקרב הארץ׃ 8
Tsoka kwa inu amene mumangokhalira kulumikiza nyumba, ndipo mumangokhalira kuwonjezera minda, mpaka mutalanda malo onse kuti muzikhalamo nokha mʼdzikomo.
באזני יהוה צבאות אם לא בתים רבים לשמה יהיו גדלים וטובים מאין יושב׃ 9
Yehova Wamphamvuzonse wayankhula ine ndikumva kuti, “Ndithudi nyumba zambirizo zidzasanduka mabwinja, nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu.
כי עשרת צמדי כרם יעשו בת אחת וזרע חמר יעשה איפה׃ 10
Munda wamphesa wa maekala khumi udzatulutsa vinyo wodzaza mbiya imodzi, kufesa madengu khumi a mbewu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.”
הוי משכימי בבקר שכר ירדפו מאחרי בנשף יין ידליקם׃ 11
Tsoka kwa iwo amene amadzuka mmamawa nathamangira chakumwa choledzeretsa, amene amamwa mpaka usiku kufikira ataledzera kotheratu.
והיה כנור ונבל תף וחליל ויין משתיהם ואת פעל יהוה לא יביטו ומעשה ידיו לא ראו׃ 12
Pa maphwando awo pamakhala azeze, apangwe, matambolini, zitoliro ndi vinyo, ndipo sasamala ntchito za Yehova, salemekeza ntchito za manja ake.
לכן גלה עמי מבלי דעת וכבודו מתי רעב והמונו צחה צמא׃ 13
Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo chifukwa cha kusamvetsa zinthu; atsogoleri awo olemekezeka adzafa ndi njala, ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu.
לכן הרחיבה שאול נפשה ופערה פיה לבלי חק וירד הדרה והמונה ושאונה ועלז בה׃ (Sheol h7585) 14
Nʼchifukwa chake ku manda sikukhuta ndipo kwayasama kwambiri kukamwa kwake; mʼmandamo mudzagweranso anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka; adzagweramo ali wowowo, nʼkuledzera kwawoko. (Sheol h7585)
וישח אדם וישפל איש ועיני גבהים תשפלנה׃ 15
Ndipo munthu aliyense adzatsitsidwa, anthu onse adzachepetsedwa, anthu odzikuza adzachita manyazi.
ויגבה יהוה צבאות במשפט והאל הקדוש נקדש בצדקה׃ 16
Koma Yehova Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chiweruzo chake cholungama. Ndipo Mulungu woyera adzadzionetsa kuti ndi woyera pochita chilungamo chake.
ורעו כבשים כדברם וחרבות מחים גרים יאכלו׃ 17
Tsono nkhosa zidzadya pamenepo ngati pabusa pawo; ana ankhosa adzadya mʼmabwinja a anthu olemera.
הוי משכי העון בחבלי השוא וכעבות העגלה חטאה׃ 18
Tsoka kwa amene amadzikokera tchimo ndi zingwe zachinyengo, ndipo amadzikokera zoyipa ndi zingwe zokokera ngolo,
האמרים ימהר יחישה מעשהו למען נראה ותקרב ותבואה עצת קדוש ישראל ונדעה׃ 19
amene amanena kuti, “Yehova afulumire, agwire ntchito yake mwamsanga kuti ntchitoyo tiyione. Ntchito zionekere, zimene Woyerayo wa Israeli akufuna kuchita, zichitike kuti tizione.”
הוי האמרים לרע טוב ולטוב רע שמים חשך לאור ואור לחשך שמים מר למתוק ומתוק למר׃ 20
Tsoka kwa amene zoyipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoyipa, amene mdima amawuyesa kuwala ndipo kuwala amakuyesa mdima, amene zowawasa amaziyesa zotsekemera ndipo zotsekemera amaziyesa zowawasa.
הוי חכמים בעיניהם ונגד פניהם נבנים׃ 21
Tsoka kwa amene amadziona ngati anzeru ndipo amadziyesa ochenjera.
הוי גבורים לשתות יין ואנשי חיל למסך שכר׃ 22
Tsoka kwa zidakwa zimene zimayika mtima pa vinyo ndipo ndi akatswiri posakaniza zakumwa,
מצדיקי רשע עקב שחד וצדקת צדיקים יסירו ממנו׃ 23
amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphu koma amayipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.
לכן כאכל קש לשון אש וחשש להבה ירפה שרשם כמק יהיה ופרחם כאבק יעלה כי מאסו את תורת יהוה צבאות ואת אמרת קדוש ישראל נאצו׃ 24
Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputu ndipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto, momwemonso mizu yawo idzawola ndipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi; chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse, ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli.
על כן חרה אף יהוה בעמו ויט ידו עליו ויכהו וירגזו ההרים ותהי נבלתם כסוחה בקרב חוצות בכל זאת לא שב אפו ועוד ידו נטויה׃ 25
Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake; watambasula dzanja lake pa anthuwo ndipo akuwakantha Mapiri akugwedezeka, ndipo mitembo ya anthu yangoti mbwee mʼmisewu ngati zinyalala. Komabe ngakhale watero, mkwiyo wake sunaleke, dzanja lake likanali chitambasulire;
ונשא נס לגוים מרחוק ושרק לו מקצה הארץ והנה מהרה קל יבוא׃ 26
Yehova wakweza mbendera kuyitana mtundu wa anthu akutali, akuyitana anthuwo ndi likhweru kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi. Awo akubwera, akubweradi mofulumira kwambiri!
אין עיף ואין כושל בו לא ינום ולא יישן ולא נפתח אזור חלציו ולא נתק שרוך נעליו׃ 27
Palibe ndi mmodzi yemwe amene akutopa kapena kupunthwa, palibe amene akusinza kapena kugona; palibe lamba wa mʼchiwuno amene akumasuka, palibe chingwe cha nsapato chimene chaduka.
אשר חציו שנונים וכל קשתתיו דרכות פרסות סוסיו כצר נחשבו וגלגליו כסופה׃ 28
Mivi yawo ndi yakuthwa, mauta awo onse ndi okoka, ziboda za akavalo awo nʼzolimba ngati mwala wansagalabwi, magaleta awo ndi aliwiro ngati kamvuluvulu.
שאגה לו כלביא ושאג ככפירים וינהם ויאחז טרף ויפליט ואין מציל׃ 29
Kufuwula kwawo kuli ngati kubangula kwa mkango, amabangula ngati misona ya mkango; imadzuma pamene ikugwira nyama ndipo imapita nayo popanda ndi mmodzi yemwe woyipulumutsa.
וינהם עליו ביום ההוא כנהמת ים ונבט לארץ והנה חשך צר ואור חשך בעריפיה׃ 30
Tsiku limenelo mitundu ya anthu idzabangula ngati mkokomo wa madzi a mʼnyanja. Ndipo wina akakayangʼana dzikolo adzangoona mdima ndi zovuta; ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.

< ישעה 5 >