< ישעה 45 >
כה אמר יהוה למשיחו לכורש אשר החזקתי בימינו לרד לפניו גוים ומתני מלכים אפתח לפתח לפניו דלתים ושערים לא יסגרו׃ | 1 |
Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wake Koresi amene anamugwira dzanja lamanja kuti agonjetse mitundu ya anthu ndi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo, ndi kutsekula zitseko kuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi:
אני לפניך אלך והדורים אושר דלתות נחושה אשבר ובריחי ברזל אגדע׃ | 2 |
Ine ndidzayenda patsogolo pako, ndi kusalaza mapiri; ndidzaphwanya zitseko za mkuwa ndi kuthyola mipiringidzo ya chitsulo.
ונתתי לך אוצרות חשך ומטמני מסתרים למען תדע כי אני יהוה הקורא בשמך אלהי ישראל׃ | 3 |
Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima, katundu wa pamalo obisika, kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina.
למען עבדי יעקב וישראל בחירי ואקרא לך בשמך אכנך ולא ידעתני׃ | 4 |
Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo, chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli, Ine ndakuyitana pokutchula dzina ndipo ndakupatsa dzina laulemu ngakhale iwe sukundidziwa Ine.
אני יהוה ואין עוד זולתי אין אלהים אאזרך ולא ידעתני׃ | 5 |
Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina; kupatula Ine palibenso Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu, ngakhale sukundidziwa Ine,
למען ידעו ממזרח שמש וממערבה כי אפס בלעדי אני יהוה ואין עוד׃ | 6 |
kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzulo anthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha. Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.
יוצר אור ובורא חשך עשה שלום ובורא רע אני יהוה עשה כל אלה׃ | 7 |
Ndimalenga kuwala ndi mdima, ndimabweretsa madalitso ndi tsoka; ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.
הרעיפו שמים ממעל ושחקים יזלו צדק תפתח ארץ ויפרו ישע וצדקה תצמיח יחד אני יהוה בראתיו׃ | 8 |
“Iwe thambo gwetsa mvula kuchokera kumwamba; mitambo ivumbwe mivumbi ya chilungamo. Dziko lapansi litsekuke, ndipo chipulumutso chiphuke kuti chilungamo chimereponso; Ine Yehova, ndine ndalenga zimenezi.
הוי רב את יצרו חרש את חרשי אדמה היאמר חמר ליצרו מה תעשה ופעלך אין ידים לו׃ | 9 |
“Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake, ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake. Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti, ‘Kodi ukuwumba chiyani?’ Kodi ntchito yako inganene kuti, ‘Ulibe luso?’
הוי אמר לאב מה תוליד ולאשה מה תחילין׃ | 10 |
Tsoka kwa wofunsa abambo ake kuti, ‘Kodi munabereka chiyani?’ Kapena amayi ake kuti, ‘Kodi mufuna kubereka chiyani?’
כה אמר יהוה קדוש ישראל ויצרו האתיות שאלוני על בני ועל פעל ידי תצוני׃ | 11 |
“Yehova Woyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena, zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi: Kodi iwe ukundifunsa za ana anga, kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga?
אנכי עשיתי ארץ ואדם עליה בראתי אני ידי נטו שמים וכל צבאם צויתי׃ | 12 |
Ndine amene ndinapanga dziko lapansi ndikulenga munthu kuti akhalemo. Ine ndi manja anga ndinayalika thambo; ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.
אנכי העירתהו בצדק וכל דרכיו אישר הוא יבנה עירי וגלותי ישלח לא במחיר ולא בשחד אמר יהוה צבאות׃ | 13 |
Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe: ndipo ndidzawongolera njira zake zonse. Iye adzamanganso mzinda wanga ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo, wopanda kupereka ndalama kapena mphotho, akutero Yehova Wamphamvuzonse.”
כה אמר יהוה יגיע מצרים וסחר כוש וסבאים אנשי מדה עליך יעברו ולך יהיו אחריך ילכו בזקים יעברו ואליך ישתחוו אליך יתפללו אך בך אל ואין עוד אפס אלהים׃ | 14 |
Yehova akuti, “Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu. Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Seba adzabwera kwa inu ndipo adzakhala anthu anu; iwo adzidzakutsatani pambuyo panu ali mʼmaunyolo. Adzakugwadirani ndi kukupemphani, ponena kuti, ‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina; palibenso mulungu wina.’”
אכן אתה אל מסתתר אלהי ישראל מושיע׃ | 15 |
Zoonadi inu muli ndi Mulungu wobisika amene ali Mulungu ndi Mpulumutsi wa Israeli.
בושו וגם נכלמו כלם יחדו הלכו בכלמה חרשי צירים׃ | 16 |
Onse amene amapanga mafano adzawachititsa manyazi ndi kuwanyozetsa. Adzakhala osokonezeka maganizo.
ישראל נושע ביהוה תשועת עולמים לא תבשו ולא תכלמו עד עולמי עד׃ | 17 |
Koma Yehova adzapulumutsa Israeli ndi chipulumutso chamuyaya; simudzachitanso manyazi kapena kunyozeka mpaka kalekale.
כי כה אמר יהוה בורא השמים הוא האלהים יצר הארץ ועשה הוא כוננה לא תהו בראה לשבת יצרה אני יהוה ואין עוד׃ | 18 |
Yehova analenga zinthu zakumwamba, Iye ndiye Mulungu; amene akulenga dziko lapansi, ndi kulikhazikitsa, sanalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma analipanga kuti anthu akhalemo. Iyeyu akunena kuti: Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.
לא בסתר דברתי במקום ארץ חשך לא אמרתי לזרע יעקב תהו בקשוני אני יהוה דבר צדק מגיד מישרים׃ | 19 |
Ine sindinayankhule mwachinsinsi, pamalo ena a mdima; Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti, “Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.” Ine Yehova, ndimayankhula zoona; ndikunena zolungama.
הקבצו ובאו התנגשו יחדו פליטי הגוים לא ידעו הנשאים את עץ פסלם ומתפללים אל אל לא יושיע׃ | 20 |
Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere; yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina. Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo, amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa.
הגידו והגישו אף יועצו יחדו מי השמיע זאת מקדם מאז הגידה הלוא אני יהוה ואין עוד אלהים מבלעדי אל צדיק ומושיע אין זולתי׃ | 21 |
Fotokozani mlandu wanu, mupatsane nzeru nonse pamodzi. Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale? Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana? Kodi si Ineyo Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine, Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa, palibenso wina kupatula Ine.
פנו אלי והושעו כל אפסי ארץ כי אני אל ואין עוד׃ | 22 |
“Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke, inu anthu onse a pa dziko lapansi, pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.
בי נשבעתי יצא מפי צדקה דבר ולא ישוב כי לי תכרע כל ברך תשבע כל לשון׃ | 23 |
Ndalumbira ndekha, pakamwa panga patulutsa mawu owona, mawu amene sadzasinthika konse akuti, bondo lililonse lidzagwada pamaso panga; anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.
אך ביהוה לי אמר צדקות ועז עדיו יבוא ויבשו כל הנחרים בו׃ | 24 |
Iwo adzanene kwa Ine kuti, ‘Chilungamo ndi mphamvu zimapezeka mwa Yehova yekha.’” Onse amene anamuwukira Iye adzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi.
ביהוה יצדקו ויתהללו כל זרע ישראל׃ | 25 |
Koma mwa Yehova zidzukulu zonse za Israeli zidzapambana ndi kupeza ulemerero.