< ישעה 43 >

ועתה כה אמר יהוה בראך יעקב ויצרך ישראל אל תירא כי גאלתיך קראתי בשמך לי אתה׃ 1
Koma tsopano, Yehova amene anakulenga, iwe Yakobo, amene anakuwumba, iwe Israeli akuti, “Usaope, pakuti ndakuwombola; Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.
כי תעבר במים אתך אני ובנהרות לא ישטפוך כי תלך במו אש לא תכוה ולהבה לא תבער בך׃ 2
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe; ndipo pamene ukuwoloka mitsinje, sidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto, sudzapsa; lawi la moto silidzakutentha.
כי אני יהוה אלהיך קדוש ישראל מושיעך נתתי כפרך מצרים כוש וסבא תחתיך׃ 3
Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako, Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako. Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe, ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe.
מאשר יקרת בעיני נכבדת ואני אהבתיך ואתן אדם תחתיך ולאמים תחת נפשך׃ 4
Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga, ndipo chifukwa ndimakukonda, ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
אל תירא כי אתך אני ממזרח אביא זרעך וממערב אקבצך׃ 5
Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe; ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa, ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo.
אמר לצפון תני ולתימן אל תכלאי הביאי בני מרחוק ובנותי מקצה הארץ׃ 6
Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’ ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’ Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali, ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi;
כל הנקרא בשמי ולכבודי בראתיו יצרתיו אף עשיתיו׃ 7
onsewo amadziwika ndi dzina langa; ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga, ndinawawumba, inde ndinawapanga.”
הוציא עם עור ועינים יש וחרשים ואזנים למו׃ 8
Tulutsa anthu amene ali nawo maso koma sakupenya, anthu amene ali nawo makutu koma sakumva.
כל הגוים נקבצו יחדו ויאספו לאמים מי בהם יגיד זאת וראשנות ישמיענו יתנו עדיהם ויצדקו וישמעו ויאמרו אמת׃ 9
Mitundu yonse ya anthu isonkhane pamodzi, anthu a mitundu ina akhale pamodzi pabwalo la milandu. Ndani wa iwo amene ananeneratu zimenezi? Ndani wa iwo anatifotokozerapo zinthu zakalekale? Abweretu ndi mboni zawo kuti adzatsimikizire kuti ananena zoona, kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, “Ndi zoona.”
אתם עדי נאם יהוה ועבדי אשר בחרתי למען תדעו ותאמינו לי ותבינו כי אני הוא לפני לא נוצר אל ואחרי לא יהיה׃ 10
Yehova akunena kuti, “Inu Aisraeli ndinu mboni zanga, ndi mtumiki wanga amene ndinakusankha, kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, ndipo mudzamvetsa kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipanapangidwepo mulungu wina, ngakhale pambuyo panga sipadzakhalaponso wina.”
אנכי אנכי יהוה ואין מבלעדי מושיע׃ 11
Akutero Yehova, “Ine, Inetu ndine Yehova, ndipo palibe Mpulumutsi wina koma Ine ndekha.
אנכי הגדתי והושעתי והשמעתי ואין בכם זר ואתם עדי נאם יהוה ואני אל׃ 12
Ndine amene ndinaneneratu, amene ndinakupulumutsa; ndine, osati mulungu wina wachilendo pakati panu amene ndinalengezeratu. Inu ndinu mboni zanga, kuti Ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.
גם מיום אני הוא ואין מידי מציל אפעל ומי ישיבנה׃ 13
“Ine ndine Mulungu kuyambira nthawi yamakedzana, ndipo ndidzakhalabe Mulungu ku nthawi zonse. Palibe amene angathe kuthawa mʼmanja mwanga, ndipo chimene ndachita palibe angathe kuchisintha.”
כה אמר יהוה גאלכם קדוש ישראל למענכם שלחתי בבלה והורדתי בריחים כלם וכשדים באניות רנתם׃ 14
Yehova akuti, Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti, “Chifukwa cha inu ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babuloni ndi kukupulumutsani. Ndidzagwetsa zitseko zonse za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.
אני יהוה קדושכם בורא ישראל מלככם׃ 15
Ine ndine Yehova, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israeli. Ine ndine Mfumu yanu.”
כה אמר יהוה הנותן בים דרך ובמים עזים נתיבה׃ 16
Yehova anapanga njira pa nyanja, anapanga njira pakati pa madzi amphamvu.
המוציא רכב וסוס חיל ועזוז יחדו ישכבו בל יקומו דעכו כפשתה כבו׃ 17
Iye anasonkhanitsa magaleta, akavalo, gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu, ndipo onse anagwa pamenepo, osadzukanso anazimitsidwa kutheratu ngati chingwe cha nyale. Yehova ameneyu akuti,
אל תזכרו ראשנות וקדמניות אל תתבננו׃ 18
“Iwalani zinthu zakale; ndipo musaganizirenso zinthu zimene zinachitika kale.
הנני עשה חדשה עתה תצמח הלוא תדעוה אף אשים במדבר דרך בישמון נהרות׃ 19
Taonani, Ine ndikuchita zinthu zatsopano! Tsopano zayamba kale kuoneka; kodi simukuziona? Ine ndikulambula msewu mʼchipululu ndi kupanga mitsinje mʼdziko lowuma.
תכבדני חית השדה תנים ובנות יענה כי נתתי במדבר מים נהרות בישימן להשקות עמי בחירי׃ 20
Nyama zakuthengo, nkhandwe ndi akadzidzi zinandilemekeza. Ndidzayendetsa mitsinje mʼdziko lowuma kuti ndiwapatse madzi anthu anga osankhidwa.
עם זו יצרתי לי תהלתי יספרו׃ 21
Anthu amene ndinadziwumbira ndekha kuti aziyimba nyimbo yotamanda Ine.
ולא אתי קראת יעקב כי יגעת בי ישראל׃ 22
“Komatu simunapemphera kwa Ine, Inu a mʼbanja la Yakobo, munatopa nane, Inu Aisraeli.
לא הביאת לי שה עלתיך וזבחיך לא כבדתני לא העבדתיך במנחה ולא הוגעתיך בלבונה׃ 23
Simunabweretse kwa Ine nkhosa za nsembe zopsereza, kapena kundilemekeza ndi nsembe zanu. Ine sindinakulemetseni pomakupemphani zopereka za chakudya kapena kukutopetsani pomakupemphani nsembe zofukiza.
לא קנית לי בכסף קנה וחלב זבחיך לא הרויתני אך העבדתני בחטאותיך הוגעתני בעונתיך׃ 24
Simunandigulire bango lonunkhira kapena kundipatsa Ine mafuta okwanira a nsembe zanu. Koma inu mwandilemetsa Ine ndi machimo anu ndipo mwanditopetsa Ine ndi zolakwa zanu.
אנכי אנכי הוא מחה פשעיך למעני וחטאתיך לא אזכר׃ 25
“Ine, Inetu, ndi amene ndimafafaniza zolakwa zanu, chifukwa cha Ine mwini, ndipo sindidzakumbukiranso machimo anu.
הזכירני נשפטה יחד ספר אתה למען תצדק׃ 26
Mundikumbutse zakale, ndipo titsutsane nkhaniyi pamodzi; fotokozani mlandu wanu kuti muonetse kuti ndinu osalakwa.
אביך הראשון חטא ומליציך פשעו בי׃ 27
Kholo lanu loyamba linachimwa; ndipo Atsogoleri anu achipembedzo anandiwukira.
ואחלל שרי קדש ואתנה לחרם יעקב וישראל לגדופים׃ 28
Chifukwa chake Ine ndidzanyazitsa akuluakulu a Nyumba yanu ya mapemphero, ndipo ndidzapereka Yakobo kuti awonongedwe ndi Israeli kuti achitidwe chipongwe.”

< ישעה 43 >