< ישעה 41 >
החרישו אלי איים ולאמים יחליפו כח יגשו אז ידברו יחדו למשפט נקרבה׃ | 1 |
“Khalani chete pamaso panga, inu mayiko a mʼmbali mwa nyanja! Alekeni ayandikire ndi kuyankhula; tiyeni tikhale pamodzi kuti atiweruze.
מי העיר ממזרח צדק יקראהו לרגלו יתן לפניו גוים ומלכים ירד יתן כעפר חרבו כקש נדף קשתו׃ | 2 |
“Ndani anadzutsa wochokera kummawa uja amene ananka napambana kulikonse kumene ankapita? Iye amapereka anthu a mitundu ina mʼmanja mwake ndipo ndi lupanga lake anagonjetsa ndi kusandutsa mafumu kukhala ngati fumbi nawamwaza ngati mankhusu ndi uta wake.
ירדפם יעבור שלום ארח ברגליו לא יבוא׃ | 3 |
Amawalondola namayenda mosavutika, mʼnjira imene mapazi ake sanayendemo kale.
מי פעל ועשה קרא הדרות מראש אני יהוה ראשון ואת אחרנים אני הוא׃ | 4 |
Ndani anachita zimenezi ndi kuzitsiriza, si uja amene anayambitsa mitundu ya anthu? Ine Yehova, ndine chiyambi ndipo potsiriza pake ndidzakhalapo.”
ראו איים וייראו קצות הארץ יחרדו קרבו ויאתיון׃ | 5 |
Mayiko amʼmbali mwa nyanja aona zimenezi ndipo akuopa; anthu a ku mathero a dziko lapansi akunjenjemera. Akuyandikira pafupi, akubwera;
איש את רעהו יעזרו ולאחיו יאמר חזק׃ | 6 |
aliyense akuthandiza mnzake ndipo akuwuza mʼbale wake kuti, “Limba mtima!”
ויחזק חרש את צרף מחליק פטיש את הולם פעם אמר לדבק טוב הוא ויחזקהו במסמרים לא ימוט׃ | 7 |
Mʼmisiri wa matabwa amalimbikitsa mʼmisiri wa golide, ndipo iye amene amasalaza fano ndi nyundo amalimbikitsa amene amalisanja pa chipala. Ponena za kuwotcherera iye amati, “Zili bwino.” Iye amalikhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwe.
ואתה ישראל עבדי יעקב אשר בחרתיך זרע אברהם אהבי׃ | 8 |
“Koma Iwe Israeli mtumiki wanga, Yakobo amene ndakusankha, Ndiwe chidzukulu cha Abrahamu bwenzi langa.
אשר החזקתיך מקצות הארץ ומאציליה קראתיך ואמר לך עבדי אתה בחרתיך ולא מאסתיך׃ | 9 |
Ndinakutengani kuchokera ku mapeto a dziko lapansi, ndinakuyitanani kuchokera ku mbali za kutali za dziko lapansi. Ine ndinati, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga;’ Ndinakusankha ndipo sindinakutaye.
אל תירא כי עמך אני אל תשתע כי אני אלהיך אמצתיך אף עזרתיך אף תמכתיך בימין צדקי׃ | 10 |
Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
הן יבשו ויכלמו כל הנחרים בך יהיו כאין ויאבדו אנשי ריבך׃ | 11 |
“Onse amene akupsera mtima adzachita manyazi ndithu ndi kunyazitsidwa; onse amene akukangana nawe sadzakhalanso kanthu, adzawonongeka.
תבקשם ולא תמצאם אנשי מצתך יהיו כאין וכאפס אנשי מלחמתך׃ | 12 |
Udzafunafuna adani ako, koma sadzapezeka. Iwo amene akuchita nawe nkhondo sadzakhalanso kanthu.
כי אני יהוה אלהיך מחזיק ימינך האמר לך אל תירא אני עזרתיך׃ | 13 |
Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako, amene ndikukugwira dzanja lako lamanja ndipo ndikuti, usaope; ndidzakuthandiza.
אל תיראי תולעת יעקב מתי ישראל אני עזרתיך נאם יהוה וגאלך קדוש ישראל׃ | 14 |
Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi, iwe wochepa mphamvu Israeli, chifukwa Ine ndidzakuthandiza,” akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.
הנה שמתיך למורג חרוץ חדש בעל פיפיות תדוש הרים ותדק וגבעות כמץ תשים׃ | 15 |
“Taona, ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu chatsopano, chakunthwa ndi cha mano ambiri. Udzanyenya mapiri ndi kuwaphwanyaphwanya, ndipo zitunda adzazisandutsa ngati mankhusu.
תזרם ורוח תשאם וסערה תפיץ אותם ואתה תגיל ביהוה בקדוש ישראל תתהלל׃ | 16 |
Udzawapeta ndipo adzawuluka ndi mphepo komanso adzamwazika ndi kamvuluvulu. Koma iwe udzakondwera chifukwa Ine ndine Mulungu wako, ndipo udzanyadira chifukwa cha Ine Woyerayo wa Israeli:
העניים והאביונים מבקשים מים ואין לשונם בצמא נשתה אני יהוה אענם אלהי ישראל לא אעזבם׃ | 17 |
“Pamene amphawi ndi osauka akufunafuna madzi, koma sakuwapeza; ndipo kummero kwawo kwawuma ndi ludzu. Ine Yehova ndidzayankha pemphero lawo; Ine, Mulungu wa Israeli, sindidzawasiya.
אפתח על שפיים נהרות ובתוך בקעות מעינות אשים מדבר לאגם מים וארץ ציה למוצאי מים׃ | 18 |
Ndidzayendetsa mitsinje mʼmalo owuma, ndi akasupe adzatumphuka mu zigwa. Ndidzasandutsa chipululu kukhala dziwe la madzi ndipo dziko lowuma kukhala akasupe a madzi.
אתן במדבר ארז שטה והדס ועץ שמן אשים בערבה ברוש תדהר ותאשור יחדו׃ | 19 |
Mʼchipululu ndidzameretsa mkungudza, kasiya mchisu ndi mtengo wa Olivi. Mʼdziko lowuma ndidzaza mitengo ya payini, ya mkuyu ndi ya mlombwa,
למען יראו וידעו וישימו וישכילו יחדו כי יד יהוה עשתה זאת וקדוש ישראל בראה׃ | 20 |
kuti anthu aone ndi kudziwa; inde, alingalire ndi kumvetsa, kuti Yehova ndiye wachita zimenezi; kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.
קרבו ריבכם יאמר יהוה הגישו עצמותיכם יאמר מלך יעקב׃ | 21 |
“Yehova akuwuza milungu ina kuti, ‘Fotokozani mlandu wanu.’ Mfumu ya Yakobo ikuti, ‘Perekani umboni wanu.’
יגישו ויגידו לנו את אשר תקרינה הראשנות מה הנה הגידו ונשימה לבנו ונדעה אחריתן או הבאות השמיענו׃ | 22 |
Bwerani ndi milungu yanu kuti idzatiwuze zomwe zidzachitike mʼtsogolo. Tifotokozereni zinthu zamakedzana tiziganizire ndi kudziwa zotsatira zake. Kapena tiwuzeni zimene zidzachitike mʼtsogolo,
הגידו האתיות לאחור ונדעה כי אלהים אתם אף תיטיבו ותרעו ונשתעה ונרא יחדו׃ | 23 |
tiwuzeni kuti kutsogolo kuli zotani, ndipo ife tidziwa kuti ndinu milungu. Chitani chinthu chabwino kapena choyipa, ndipo mutidabwitsa ndi kutichititsa mantha.
הן אתם מאין ופעלכם מאפע תועבה יבחר בכם׃ | 24 |
Koma inu sindinu kanthu ndipo zochita zanu nʼzopandapake; amene amapembedza inu ali ngati chinthu chokanidwa chifukwa ndi choyipa.
העירותי מצפון ויאת ממזרח שמש יקרא בשמי ויבא סגנים כמו חמר וכמו יוצר ירמס טיט׃ | 25 |
“Ndinawutsa munthu wina kumpoto ndipo anabwera, munthu wochokera kummawa amene ndinamuyitana. Amapondaponda olamulira ngati matope, ngati ndi wowumba mbiya amene akuponda dongo.
מי הגיד מראש ונדעה ומלפנים ונאמר צדיק אף אין מגיד אף אין משמיע אף אין שמע אמריכם׃ | 26 |
Ndani anawululiratu zimenezi poyamba pomwe, kuti ife tidziwe, kapena kutiwuziratu zisanachitike kuti ife tinene kuti, ‘Analondola?’ Palibe amene ananena, palibe analengeza zimenezi, palibe anamva mawu anu.
ראשון לציון הנה הנם ולירושלם מבשר אתן׃ | 27 |
Ine ndinali woyamba kumuwuza Ziyoni kuti, ‘Taona, si awa akubwera apawa!’ Ndinatumiza mthenga wa nkhani yabwino ku Yerusalemu.
וארא ואין איש ומאלה ואין יועץ ואשאלם וישיבו דבר׃ | 28 |
Koma ndikayangʼana palibe ndi mmodzi yemwe, palibe ndi mmodzi yemwe pakati pawo wotha kupereka uphungu, palibe woti ayankhe pamene ine ndawafunsa.
הן כלם און אפס מעשיהם רוח ותהו נסכיהם׃ | 29 |
Taonani, milungu yonseyi ndi yachinyengo! Zochita zawo si kanthu konse; mafano awo ali ngati mphepo yachabechabe.