< ישעה 27 >
ביום ההוא יפקד יהוה בחרבו הקשה והגדולה והחזקה על לויתן נחש ברח ועל לויתן נחש עקלתון והרג את התנין אשר בים׃ | 1 |
Tsiku limenelo, Yehova ndi lupanga lake lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu, adzalanga Leviyatani chinjoka chothawa chija, Leviyatani chinjoka chodzikulunga; adzapha chirombo choopsa cha mʼnyanja.
ביום ההוא כרם חמד ענו לה׃ | 2 |
Tsiku limenelo Yehova adzati, “Tidzayimba nyimbo ya munda wamphesa wobereka bwino:
אני יהוה נצרה לרגעים אשקנה פן יפקד עליה לילה ויום אצרנה׃ | 3 |
Ine, Yehova, ndimawuyangʼanira; ndimawuthirira nthawi zonse. Ndimawulondera usana ndi usiku kuti wina angawononge.
חמה אין לי מי יתנני שמיר שית במלחמה אפשעה בה אציתנה יחד׃ | 4 |
Ine sindinakwiye. Ngati mkandankhuku ndi minga zikanaoneka ndikanalimbana nazo! Ndikachita nazo nkhondo; ndikanazitentha zonse ndi moto.
או יחזק במעוזי יעשה שלום לי שלום יעשה לי׃ | 5 |
Koma ngati apo ayi, abweretu kwa Ine adani angawo kuti ndidzawateteze; apangane nane za mtendere, ndithu, apangane nane za mtendere.”
הבאים ישרש יעקב יציץ ופרח ישראל ומלאו פני תבל תנובה׃ | 6 |
Masiku akubwerawo Yakobo adzazika mizu, Israeli adzaphukira ndi kuchita maluwa, ndipo adzadzaza dziko lonse lapansi ndi zipatso.
הכמכת מכהו הכהו אם כהרג הרגיו הרג׃ | 7 |
Kodi Yehova anakantha Israeli ngati momwe anakanthira anthu amene anazunza Israeli? Kapena kodi Yehova anapha Israeli ngati mmene anthu ena anaphera Israeli?
בסאסאה בשלחה תריבנה הגה ברוחו הקשה ביום קדים׃ | 8 |
Yehova mwawalanga powapirikitsa ndi kuwatumiza ku ukapolo, mwawachotsa ndi mpweya wanu woopsa, monga zimachitikira pa tsiku la mkuntho wochokera kummawa.
לכן בזאת יכפר עון יעקב וזה כל פרי הסר חטאתו בשומו כל אבני מזבח כאבני גר מנפצות לא יקמו אשרים וחמנים׃ | 9 |
Yehova adzakhululuka kulakwa kwa Yakobo. Iwo adzaonetsa kuti alapadi pamene adzaphwanya miyala yonse ya guwa lachikunja, ngati mmene anthu amaphwanyira miyala yanjereza mpaka kukhala ngati fumbi lokhalokha. Sipadzapezekanso mafano a Asera kapena maguwa ofukiza lubani.
כי עיר בצורה בדד נוה משלח ונעזב כמדבר שם ירעה עגל ושם ירבץ וכלה סעפיה׃ | 10 |
Mzinda wamalinga uja wasanduka bwinja, wasanduka malo osiyidwa, ndi kutayidwa ngati chipululu; kumeneko amadyetselako ana angʼombe kumeneko zimapumulako ziweto ndi kumwetula nthambi za mitengo kotheratu.
ביבש קצירה תשברנה נשים באות מאירות אותה כי לא עם בינות הוא על כן לא ירחמנו עשהו ויצרו לא יחננו׃ | 11 |
Pamene nthambi za mitengoyo zauma, zimathyoka ndipo amayi amabwera nazitola ndi kuzisandutsa nkhuni. Pakuti awa ndi anthu opanda nzeru; kotero Mulungu amene anawapanga sadzachitira chisoni, ndipo Mlengi wawo sawakomera mtima.
והיה ביום ההוא יחבט יהוה משבלת הנהר עד נחל מצרים ואתם תלקטו לאחד אחד בני ישראל׃ | 12 |
Tsiku limenelo Yehova adzasonkhanitsa pamodzi anthu ake mmodzimmodzi kumalo opunthira tirigu, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Igupto.
והיה ביום ההוא יתקע בשופר גדול ובאו האבדים בארץ אשור והנדחים בארץ מצרים והשתחוו ליהוה בהר הקדש בירושלם׃ | 13 |
Ndipo tsiku limenelo lipenga lalikulu lidzalira. Amene akuzunzika ku Asiriya iwo amene ali ku ukapolo ku Igupto adzabwera ndi kudzalambira Yehova pa phiri lopatulika mu Yerusalemu.