< ישעה 16 >
שלחו כר משל ארץ מסלע מדברה אל הר בת ציון׃ | 1 |
Anthu a ku Mowabu atumiza mphatso za ana ankhosa onenepa, kuchokera ku Sela kudutsa chipululu mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
והיה כעוף נודד קן משלח תהיינה בנות מואב מעברת לארנון׃ | 2 |
Monga momwe mbalame zimawulukira uku ndi uku akazimwaza mʼchisa, momwemonso akazi a ku Mowabu akuyendayenda ku madooko a Arinoni.
הביאו עצה עשו פלילה שיתי כליל צלך בתוך צהרים סתרי נדחים נדד אל תגלי׃ | 3 |
Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti, “Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite. Inu mutiteteze kwa adani anthu. Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo. Mutibise, musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.
יגורו בך נדחי מואב הוי סתר למו מפני שודד כי אפס המץ כלה שד תמו רמס מן הארץ׃ | 4 |
Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu; mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.” Nthawi idzafika ndipo wozunzayo sadzakhalaponso, kuwononga kudzaleka; waukaliyo adzachoka mʼdzikomo.
והוכן בחסד כסא וישב עליו באמת באהל דוד שפט ודרש משפט ומהר צדק׃ | 5 |
Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi; mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika. Iyeyo poweruza adzatsata chilungamo ndipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.
שמענו גאון מואב גא מאד גאותו וגאונו ועברתו לא כן בדיו׃ | 6 |
Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri. Kunyada kwawo ndi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo, zonse ndi zopanda phindu.
לכן ייליל מואב למואב כלה ייליל לאשישי קיר חרשת תהגו אך נכאים׃ | 7 |
Nʼchifukwa chake Amowabu akulira kwambiri; iwo akulirira dziko lawo. Akubuma momvetsa chisoni chifukwa cha makeke a mphesa a ku Kiri Hareseti.
כי שדמות חשבון אמלל גפן שבמה בעלי גוים הלמו שרוקיה עד יעזר נגעו תעו מדבר שלחותיה נטשו עברו ים׃ | 8 |
Minda ya ku Hesiboni yauma, minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga. Atsogoleri a mitundu ina anapondaponda minda ya mpesa wabwino, imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri, mpaka kutambalalira ku chipululu. Mizu yake inakafika mpaka ku tsidya la nyanja.
על כן אבכה בבכי יעזר גפן שבמה אריוך דמעתי חשבון ואלעלה כי על קיצך ועל קצירך הידד נפל׃ | 9 |
Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri, chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima. Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali, ndikukunyowetsani ndi misozi! Mwalephera kupeza zokolola, chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.
ונאסף שמחה וגיל מן הכרמל ובכרמים לא ירנן לא ירעע יין ביקבים לא ידרך הדרך הידד השבתי׃ | 10 |
Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso; palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa; palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa, pakuti ndathetsa kufuwula.
על כן מעי למואב ככנור יהמו וקרבי לקיר חרש׃ | 11 |
Chifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe kulirira Mowabu, mtima wanga ukubuwula chifukwa cha Kiri Hareseti.
והיה כי נראה כי נלאה מואב על הבמה ובא אל מקדשו להתפלל ולא יוכל׃ | 12 |
Ngakhale anthu a ku Mowabu apite ku malo awo achipembedzo koma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabe chifukwa sizidzatheka.
זה הדבר אשר דבר יהוה אל מואב מאז׃ | 13 |
Awa ndi mawu amene Yehova wayankhula kale zokhudza Mowabu.
ועתה דבר יהוה לאמר בשלש שנים כשני שכיר ונקלה כבוד מואב בכל ההמון הרב ושאר מעט מזער לוא כביר׃ | 14 |
Koma tsopano Yehova akuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata mʼmene munthu waganyu amawerengera, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu ndipo anthu ake ambiri adzakhala atawonongeka, ndipo opulumuka ake adzakhala ochepa ndi ofowoka.”