< ישעה 11 >
ויצא חטר מגזע ישי ונצר משרשיו יפרה׃ | 1 |
Padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese ndipo nthambi idzaphukira kuchokera ku mizu yake.
ונחה עליו רוח יהוה רוח חכמה ובינה רוח עצה וגבורה רוח דעת ויראת יהוה׃ | 2 |
Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu, Mzimu wauphungu ndi wamphamvu, Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova.
והריחו ביראת יהוה ולא למראה עיניו ישפוט ולא למשמע אזניו יוכיח׃ | 3 |
Ndipo kuopa Yehova ndiye chidzakhale chinthu chomukondweretsa. Iye sadzaweruza potsata zooneka pamaso, kapena kugamula mlandu potsata zakumva;
ושפט בצדק דלים והוכיח במישור לענוי ארץ והכה ארץ בשבט פיו וברוח שפתיו ימית רשע׃ | 4 |
koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo, adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi. Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake; atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa.
והיה צדק אזור מתניו והאמונה אזור חלציו׃ | 5 |
Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake ndipo kukhulupirika kudzakhala ngati chomangira mʼchiwuno mwake.
וגר זאב עם כבש ונמר עם גדי ירבץ ועגל וכפיר ומריא יחדו ונער קטן נהג בם׃ | 6 |
Mʼmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwana wambuzi, mwana wangʼombe ndi mwana wa mkango adzadyera limodzi ndipo mwana wamngʼono adzaziweta.
ופרה ודב תרעינה יחדו ירבצו ילדיהן ואריה כבקר יאכל תבן׃ | 7 |
Ngʼombe yayikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi, ana awo adzagona pamodzi, ndipo mkango udzadya udzu ngati ngʼombe.
ושעשע יונק על חר פתן ועל מאורת צפעוני גמול ידו הדה׃ | 8 |
Mwana wakhanda adzasewera pa dzenje la mamba, ndipo mwana wamngʼono adzapisa dzanja lake ku phanga la mphiri osalumidwa.
לא ירעו ולא ישחיתו בכל הר קדשי כי מלאה הארץ דעה את יהוה כמים לים מכסים׃ | 9 |
Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga pa phiri lopatulika la Yehova, pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.
והיה ביום ההוא שרש ישי אשר עמד לנס עמים אליו גוים ידרשו והיתה מנחתו כבוד׃ | 10 |
Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera pa Muzu wa Yese idzakhala ngati chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Mitundu ya anthu idzasonkhana kwa Iye, ndipo malo awo okhalapo adzakhala aulemerero.
והיה ביום ההוא יוסיף אדני שנית ידו לקנות את שאר עמו אשר ישאר מאשור וממצרים ומפתרוס ומכוש ומעילם ומשנער ומחמת ומאיי הים׃ | 11 |
Tsiku limenelo Ambuye adzatambasula dzanja lake kachiwiri kuti awombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Igupto, ku Patirosi, Kusi, ku Elamu, ku Sinana, ku Hamati ndi pa zilumba za nyanja yamchere.
ונשא נס לגוים ואסף נדחי ישראל ונפצות יהודה יקבץ מארבע כנפות הארץ׃ | 12 |
Adzakwezera mitundu ya anthu mbendera, ndipo adzasonkhanitsa otayika a ku Israeli; Iye adzasonkhanitsa anthu obalalika a ku Yuda kuchokera ku mbali zonse zinayi za dziko lapansi.
וסרה קנאת אפרים וצררי יהודה יכרתו אפרים לא יקנא את יהודה ויהודה לא יצר את אפרים׃ | 13 |
Nsanje ya Efereimu idzatha, ndipo adani a Yuda adzatha; Efereimu sadzachitira nsanje Yuda, ngakhale Yuda sadzamuda Efereimu.
ועפו בכתף פלשתים ימה יחדו יבזו את בני קדם אדום ומואב משלוח ידם ובני עמון משמעתם׃ | 14 |
Yuda ndi Efereimu adzathira nkhondo pa Afilisti mbali ya kumadzulo; ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu a kummawa. Adzalimbana ndi Edomu ndi Mowabu, ndipo Aamoni adzawagonjera.
והחרים יהוה את לשון ים מצרים והניף ידו על הנהר בעים רוחו והכהו לשבעה נחלים והדריך בנעלים׃ | 15 |
Yehova adzaphwetsa mwendo wa nyanja ya Igupto; adzatambasula dzanja lake ndipo adzawombetsa mphepo yotentha pa mtsinje wa Yufurate. Iye adzawugawa mtsinjewo kukhala timitsinje tisanu ndi tiwiri kuti anthu athe kuwoloka powuma atavala nsapato.
והיתה מסלה לשאר עמו אשר ישאר מאשור כאשר היתה לישראל ביום עלתו מארץ מצרים׃ | 16 |
Padzakhala msewu waukulu woti ayendepo anthu ake otsalira amene anatsalira ku Asiriya, monga mmene panali msewu waukulu woyendapo Israeli pamene amachokera ku Igupto.