< ישעה 10 >
הוי החקקים חקקי און ומכתבים עמל כתבו׃ | 1 |
Tsoka kwa anthu amene amapanga malamulo opanda chilungamo, kwa iwo amene amalemba zongovutitsa anzawo,
להטות מדין דלים ולגזל משפט עניי עמי להיות אלמנות שללם ואת יתומים יבזו׃ | 2 |
kuwalanda anthu osauka ufulu wawo ndi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga, amalanda zinthu za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye.
ומה תעשו ליום פקדה ולשואה ממרחק תבוא על מי תנוסו לעזרה ואנה תעזבו כבודכם׃ | 3 |
Kodi mudzatani pa tsiku la chilango, pofika chiwonongeko chochokera kutali? Kodi mudzathawira kwa yani kuti akuthandizeni? Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?
בלתי כרע תחת אסיר ותחת הרוגים יפלו בכל זאת לא שב אפו ועוד ידו נטויה׃ | 4 |
Kudzatsala nʼkungozolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa kapena kufa pamodzi ndi ophedwa. Komabe pa zonsezi mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
הוי אשור שבט אפי ומטה הוא בידם זעמי׃ | 5 |
“Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya, chikwapu cha mkwiyo wanga, iye ndiye ndodo ya mkwiyo wanga!
בגוי חנף אשלחנו ועל עם עברתי אצונו לשלל שלל ולבז בז ולשימו מרמס כחמר חוצות׃ | 6 |
Ndidzamutuma kukalimbana ndi mtundu wosapembedza Mulungu, ndidzamutumiza kukalimbana ndi anthu amene amandikwiyitsa Ine, kukafunkha ndi kulanda chuma, ndi kuwapondereza pansi ngati matope a mʼmisewu.
והוא לא כן ידמה ולבבו לא כן יחשב כי להשמיד בלבבו ולהכרית גוים לא מעט׃ | 7 |
Koma izi si zimene akufuna kukachita, izi si zimene zili mʼmaganizo mwake; cholinga chake ndi kukawononga, kukapulula mitundu yambiri ya anthu.
כי יאמר הלא שרי יחדו מלכים׃ | 8 |
Iye akuti, ‘Kodi atsogoleri anga ankhondo si mafumu okhaokha?’
הלא ככרכמיש כלנו אם לא כארפד חמת אם לא כדמשק שמרון׃ | 9 |
‘Kodi Kalino sanagonjetsedwe monga Karikemesi? Kodi Hamati sali ngati Aripadi, nanga Samariya sali ngati Damasiko?
כאשר מצאה ידי לממלכת האליל ופסיליהם מירושלם ומשמרון׃ | 10 |
Dzanja langa linakantha maufumu a anthu opembedza mafano, mafumu amene mafano awo ndi aakulu kupambana Yerusalemu ndi Samariya;
הלא כאשר עשיתי לשמרון ולאליליה כן אעשה לירושלם ולעצביה׃ | 11 |
nanga Ine nʼkulephera kodi kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake monga ndinakanthira Samariya pamodzi ndi mafano ake?’”
והיה כי יבצע אדני את כל מעשהו בהר ציון ובירושלם אפקד על פרי גדל לבב מלך אשור ועל תפארת רום עיניו׃ | 12 |
Ambuye akadzamaliza ntchito yonse yolanga phiri la Ziyoni ndi Yerusalemu adzalanganso mfumu ya ku Asiriya chifukwa cha kudzitama ndi kunyada kwake.
כי אמר בכח ידי עשיתי ובחכמתי כי נבנותי ואסיר גבולת עמים ועתידתיהם שושתי ואוריד כאביר יושבים׃ | 13 |
Pakuti mfumuyo ikuti, “‘Ndachita zimenezi ndi dzanja langa, ndiponso ndi nzeru zanga, chifukwa ndine wozindikira zinthu. Ndinachotsa malire a mitundu ya anthu, ndinafunkha chuma chawo; ndinagonjetsa mafumu awo monga munthu wamphamvu.
ותמצא כקן ידי לחיל העמים וכאסף ביצים עזבות כל הארץ אני אספתי ולא היה נדד כנף ופצה פה ומצפצף׃ | 14 |
Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu ngati momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame, ngati momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, motero inenso ndinasonkhanitsa mayiko onse; palibe mbalame imene inakupiza mapiko ake, kapena kuyasama kukamwa kuti ilire.’”
היתפאר הגרזן על החצב בו אם יתגדל המשור על מניפו כהניף שבט את מרימיו כהרים מטה לא עץ׃ | 15 |
Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana woyigwiritsa ntchito, kapena macheka angathe kudzikuza kupambana wowagwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti chikwapu chikuzunguza munthu amene wachinyamula, kapena ngati kuti ndodo ikuopseza amene wayinyamula!
לכן ישלח האדון יהוה צבאות במשמניו רזון ותחת כבדו יקד יקד כיקוד אש׃ | 16 |
Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzatumiza matenda owondetsa kwa ankhondo amphamvu; kunyada kwa mfumuyo kudzapsa ndi moto wosazima.
והיה אור ישראל לאש וקדושו ללהבה ובערה ואכלה שיתו ושמירו ביום אחד׃ | 17 |
Mulungu, Kuwala kwa Israeli, adzakhala ngati moto, Woyera uja wa Israeli adzakhala ngati malawi a moto. Motowo udzawatentha ndi kuwapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.
וכבוד יערו וכרמלו מנפש ועד בשר יכלה והיה כמסס נסס׃ | 18 |
Ankhondo ake adzawonongedwa ngati nkhalango yayikulu ndi ngati nthaka yachonde.
ושאר עץ יערו מספר יהיו ונער יכתבם׃ | 19 |
Mitengo yotsalira ya mʼnkhalango zake idzakhala yochepa kwambiri, yoti ndi mwana yemwe ndi kuyiwerenga.
והיה ביום ההוא לא יוסיף עוד שאר ישראל ופליטת בית יעקב להשען על מכהו ונשען על יהוה קדוש ישראל באמת׃ | 20 |
Tsiku limenelo otsalira a ku Israeli, opulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzadaliranso anthu amene anawakantha, koma adzadalira Yehova, Woyerayo wa Israeli.
שאר ישוב שאר יעקב אל אל גבור׃ | 21 |
Otsalira adzabwerera, otsalira a Yakobo adzabwerera kwa Mulungu Wamphamvu.
כי אם יהיה עמך ישראל כחול הים שאר ישוב בו כליון חרוץ שוטף צדקה׃ | 22 |
Iwe Israeli, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wa ku nyanja, otsala okha ndiwo adzabwerere. Chiwonongeko chalamulidwa, chidzaonetsa chilungamo chosefukira.
כי כלה ונחרצה אדני יהוה צבאות עשה בקרב כל הארץ׃ | 23 |
Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzawononga ndithu dziko lonse monga momwe analamulira.
לכן כה אמר אדני יהוה צבאות אל תירא עמי ישב ציון מאשור בשבט יככה ומטהו ישא עליך בדרך מצרים׃ | 24 |
Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, “Inu anthu anga okhala mu Ziyoni, musawaope Asiriya, amene amakukanthani ndi ndodo nakumenyani ndi zibonga monga mmene Igupto anachitira.
כי עוד מעט מזער וכלה זעם ואפי על תבליתם׃ | 25 |
Patsala pangʼonongʼono kuti mkwiyo wanga uchoke pa inu ndipo ndidzaonetsa ukali wanga pa iwo mpaka kuwawononga.”
ועורר עליו יהוה צבאות שוט כמכת מדין בצור עורב ומטהו על הים ונשאו בדרך מצרים׃ | 26 |
Yehova Wamphamvuzonse adzawakwapula ndi chikwapu, monga momwe anakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu; ndipo adzatukula ndodo yake pa madzi ndikuwalanga monga analangira Igupto pa nyanja.
והיה ביום ההוא יסור סבלו מעל שכמך ועלו מעל צוארך וחבל על מפני שמן׃ | 27 |
Tsiku limenelo katundu wawo adzachotsedwa pa mapewa anu, goli lawo lidzachoka mʼkhosi mwanu; golilo lidzathyoka chifukwa cha kunenepa kwambiri.
בא על עית עבר במגרון למכמש יפקיד כליו׃ | 28 |
Adani alowa mu Ayati apyola ku Migironi; asunga katundu wawo ku Mikimasi.
עברו מעברה גבע מלון לנו חרדה הרמה גבעת שאול נסה׃ | 29 |
Adutsa pa mpata uja, ndipo akuti, “Tikagona ku Geba” Rama akunjenjemera; Gibeya, mzinda wa Saulo ukuthawa.
צהלי קולך בת גלים הקשיבי לישה עניה ענתות׃ | 30 |
Lilani mokweza, inu anthu a ku Galimu! Tchera khutu, iwe Laisa! Iwe Anatoti wosauka!
נדדה מדמנה ישבי הגבים העיזו׃ | 31 |
Anthu a ku Madimena akuthawa; anthu a ku Gebimu bisalani.
עוד היום בנב לעמד ינפף ידו הר בית ציון גבעת ירושלם׃ | 32 |
Lero lomwe lino adaniwo adzayima ku Nobu; adzagwedeza mikono yawo, kuopseza anthu a ku Ziyoni, pa phiri la Yerusalemu.
הנה האדון יהוה צבאות מסעף פארה במערצה ורמי הקומה גדועים והגבהים ישפלו׃ | 33 |
Taonani, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse, adzadula mwamphamvu nthambi za mitengo, mitengo yodzikweza idzadulidwa, mitengo yayitali idzagwetsedwa.
ונקף סבכי היער בברזל והלבנון באדיר יפול׃ | 34 |
Yehova adzadula ndi nkhwangwa mitengo ya mʼnkhalango yowirira; Lebanoni adzagwa pamaso pa Wamphamvu.