< הושע 12 >
אפרים רעה רוח ורדף קדים כל היום כזב ושד ירבה וברית עם אשור יכרתו ושמן למצרים יובל׃ | 1 |
Efereimu amadya mpweya; tsiku lonse amasaka mphepo ya kummawa ndipo amachulukitsa mabodza ndi chiwawa. Amachita mgwirizano ndi Asiriya ndipo amatumiza mphatso za mafuta a olivi ku Igupto.
וריב ליהוה עם יהודה ולפקד על יעקב כדרכיו כמעלליו ישיב לו׃ | 2 |
Yehova akuyimba mlandu Yuda; Iye adzalanga Yakobo molingana ndi makhalidwe ake, adzamulanga molingana ndi ntchito zake.
בבטן עקב את אחיו ובאונו שרה את אלהים׃ | 3 |
Akali mʼmimba mwa amayi ake, Yakobo anagwira chidendene cha mʼbale wake; iye atakula analimbana ndi Mulungu.
וישר אל מלאך ויכל בכה ויתחנן לו בית אל ימצאנו ושם ידבר עמנו׃ | 4 |
Yakobo analimbana ndi mngelo ndipo anapambana; analira napempha kuti amukomere mtima. Mulungu anakumana naye ku Beteli ndipo anayankhula naye kumeneko,
ויהוה אלהי הצבאות יהוה זכרו׃ | 5 |
Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Yehova ndiye dzina lake lotchuka!
ואתה באלהיך תשוב חסד ומשפט שמר וקוה אל אלהיך תמיד׃ | 6 |
Koma inu muyenera kubwerera kwa Mulungu wanu; pitirizani chikondi ndi chiweruzo cholungama, ndipo muzidikira Mulungu wanu nthawi zonse.
כנען בידו מאזני מרמה לעשק אהב׃ | 7 |
Munthu wamalonda amagwiritsa ntchito masikelo achinyengo; iyeyo amakonda kubera anthu.
ויאמר אפרים אך עשרתי מצאתי און לי כל יגיעי לא ימצאו לי עון אשר חטא׃ | 8 |
Efereimu amadzitama ponena kuti, “Ndine wolemera kwambiri; ndili ndi chuma chambiri. Palibe amene angandiloze chala chifukwa cha kulemera kwanga.”
ואנכי יהוה אלהיך מארץ מצרים עד אושיבך באהלים כימי מועד׃ | 9 |
“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa mu Igupto. Ndidzakukhazikaninso mʼmatenti, monga munkachitira masiku aja pa nthawi ya zikondwerero zanu.
ודברתי על הנביאים ואנכי חזון הרביתי וביד הנביאים אדמה׃ | 10 |
Ndinayankhula ndi aneneri, ndinawaonetsa masomphenya ambiri, ndipo ndinawawuza mafanizo kudzera mwa iwo.”
אם גלעד און אך שוא היו בגלגל שורים זבחו גם מזבחותם כגלים על תלמי שדי׃ | 11 |
Kodi Giliyadi ndi woyipa? Anthu ake ndi achabechabe! Kodi amapereka nsembe za ngʼombe zazimuna ku Giligala? Maguwa awo ansembe adzakhala ngati milu ya miyala mʼmunda molimidwa.
ויברח יעקב שדה ארם ויעבד ישראל באשה ובאשה שמר׃ | 12 |
Yakobo anathawira ku dziko la Aramu, Israeli anagwira ntchito kuti apeze mkazi, ndipo anaweta nkhosa kuti akwatire mkaziyo.
ובנביא העלה יהוה את ישראל ממצרים ובנביא נשמר׃ | 13 |
Yehova anagwiritsa ntchito mneneri kuti atulutse Israeli mu Igupto; kudzera mwa mneneriyo Iye anawasamalira.
הכעיס אפרים תמרורים ודמיו עליו יטוש וחרפתו ישיב לו אדניו׃ | 14 |
Koma Efereimu wamukwiyitsa kwambiri. Nʼchifukwa chake Yehova adzawalanga ndi imfa. Adzawalanga chifukwa anamuchititsa manyazi kwambiri.