< הושע 11 >
כי נער ישראל ואהבהו וממצרים קראתי לבני׃ | 1 |
“Israeli ali mwana, ndinamukonda, ndipo ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.
קראו להם כן הלכו מפניהם לבעלים יזבחו ולפסלים יקטרון׃ | 2 |
Koma ndimati ndikamapitiriza kuyitana iwo amandithawa kupita kutali. Ankapereka nsembe kwa Abaala ndipo ankafukiza lubani kwa mafano.
ואנכי תרגלתי לאפרים קחם על זרועתיו ולא ידעו כי רפאתים׃ | 3 |
Ndi Ine amene ndinaphunzitsa Efereimu kuyenda, ndipo ndinawagwira pa mkono; koma iwo sanazindikire kuti ndine amene ndinawachiritsa.
בחבלי אדם אמשכם בעבתות אהבה ואהיה להם כמרימי על על לחיהם ואט אליו אוכיל׃ | 4 |
Ndinawatsogolera ndi zingwe zachifundo cha anthu ndi zomangira za chikondi; ndinachotsa goli mʼkhosi mwawo ndipo ndinawerama nʼkuwadyetsa.
לא ישוב אל ארץ מצרים ואשור הוא מלכו כי מאנו לשוב׃ | 5 |
“Sadzabwerera ku Igupto, koma Asiriya ndiye adzakhala mfumu yawo pakuti akana kutembenuka.
וחלה חרב בעריו וכלתה בדיו ואכלה ממעצותיהם׃ | 6 |
Malupanga adzangʼanima mʼmizinda yawo, ndipo adzawononga mipiringidzo ya zipata zawo nadzathetseratu malingaliro awo.
ועמי תלואים למשובתי ואל על יקראהו יחד לא ירומם׃ | 7 |
Anthu anga atsimikiza zondifulatira Ine. Ngakhale atayitana Wammwambamwamba, sizidzatheka kuti Iye awakwezenso.
איך אתנך אפרים אמגנך ישראל איך אתנך כאדמה אשימך כצבאים נהפך עלי לבי יחד נכמרו נחומי׃ | 8 |
“Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efereimu? Kodi ndingakupereke bwanji iwe Israeli? Kodi ndingakuchitire bwanji zimene ndinachitira Adima? Kodi ndingathe bwanji kukuchitira zimene ndinachitira Zeboimu? Mtima wanga wakana kutero; chifundo changa chonse chikusefukira.
לא אעשה חרון אפי לא אשוב לשחת אפרים כי אל אנכי ולא איש בקרבך קדוש ולא אבוא בעיר׃ | 9 |
Sindidzalola kuti ndikulange ndi mkwiyo wanga woopsa, kapena kutembenuka ndi kuwononga Efereimu. Pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu, Woyerayo pakati panu. Sindidzabwera mwaukali.
אחרי יהוה ילכו כאריה ישאג כי הוא ישאג ויחרדו בנים מים׃ | 10 |
Iwo adzatsatira Yehova; Iye adzabangula ngati mkango. Akadzabangula, ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo.
יחרדו כצפור ממצרים וכיונה מארץ אשור והושבתים על בתיהם נאם יהוה׃ | 11 |
Adzabwera akunjenjemera ngati mbalame kuchokera ku Igupto, ngati nkhunda kuchokera ku Asiriya. Ine ndidzawakhazikanso mʼnyumba zawo,” akutero Yehova.
סבבני בכחש אפרים ובמרמה בית ישראל ויהודה עד רד עם אל ועם קדושים נאמן׃ | 12 |
Efereimu wandizungulira ndi mabodza, nyumba ya Israeli yandizungulira ndi chinyengo. Ndipo Yuda wawukira Mulungu, wawukira ngakhale Woyerayo amene ndi wokhulupirika.