< בראשית 44 >
ויצו את אשר על ביתו לאמר מלא את אמתחת האנשים אכל כאשר יוכלון שאת ושים כסף איש בפי אמתחתו׃ | 1 |
Pambuyo pake Yosefe analamulira wantchito wa mʼnyumba mwake kuti, “Adzazire chakudya anthuwa mʼmatumba mwawo monga mmene anganyamulire, ndipo uwayikire ndalama zawo pakamwa pa matumba awowo.
ואת גביעי גביע הכסף תשים בפי אמתחת הקטן ואת כסף שברו ויעש כדבר יוסף אשר דבר׃ | 2 |
Tsono uyike chikho changa cha siliva chija, pakamwa pa thumba la wamngʼono kwambiriyu pamodzi ndi ndalama zake za chakudya” Ndipo iye anachita monga Yosefe ananenera.
הבקר אור והאנשים שלחו המה וחמריהם׃ | 3 |
Mmawa kutacha anthu aja analoledwa kuti apite ndi abulu awo.
הם יצאו את העיר לא הרחיקו ויוסף אמר לאשר על ביתו קום רדף אחרי האנשים והשגתם ואמרת אלהם למה שלמתם רעה תחת טובה׃ | 4 |
Atangotuluka mu mzinda muja, koma asanapite patali, Yosefe anati kwa wantchito wake, “Nyamuka atsatire anthu aja msanga. Ndipo ukawapeza, uwafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoyipa ndi zabwino?
הלוא זה אשר ישתה אדני בו והוא נחש ינחש בו הרעתם אשר עשיתם׃ | 5 |
Mwaberanji chikho chimene mbuye wanga amamweramo ndi kugwiritsa ntchito akafuna kuwombeza? Chimene mwachitachi ndi chinthu choyipa.’”
וישגם וידבר אלהם את הדברים האלה׃ | 6 |
Wantchito uja atawapeza ananena mawu anawuzidwa aja.
ויאמרו אליו למה ידבר אדני כדברים האלה חלילה לעבדיך מעשות כדבר הזה׃ | 7 |
Koma iwo anati kwa iye, “Kodi mbuye wanga mukuneneranji zimenezi? Sizingatheke ndi pangʼono pomwe kuti antchito anufe nʼkuchita zoterozo ayi!
הן כסף אשר מצאנו בפי אמתחתינו השיבנו אליך מארץ כנען ואיך נגנב מבית אדניך כסף או זהב׃ | 8 |
Paja ife pobwera kuchokera ku Kanaani tinatenga ndalama kubwezera zimene tinazipeza mʼmatumba mwathu. Ndiye pali chifukwa chanji kuti tikabe siliva kapena golide mʼnyumba mwa mbuye wanu?
אשר ימצא אתו מעבדיך ומת וגם אנחנו נהיה לאדני לעבדים׃ | 9 |
Ngati wantchito wanu wina pano atapezeka nacho chikhocho, ameneyo aphedwe ndipo ena tonsefe tidzakhala akapolo anu, mbuye wathu.”
ויאמר גם עתה כדבריכם כן הוא אשר ימצא אתו יהיה לי עבד ואתם תהיו נקים׃ | 10 |
Iye anati, “Chabwino, tsono zikhale monga mwaneneramu. Komatu aliyense amene angapezeke nacho chikhocho adzakhala kapolo wanga, ndipo ena nonsenu muzipita mwaufulu.”
וימהרו ויורדו איש את אמתחתו ארצה ויפתחו איש אמתחתו׃ | 11 |
Tsono onse anafulumira kutsitsa pansi aliyense thumba lake ndi kulitsekula.
ויחפש בגדול החל ובקטן כלה וימצא הגביע באמתחת בנימן׃ | 12 |
Kenaka anayamba kufufuza, kuyambira pa wamkulu mpaka pa wamngʼono. Ndipo chikhocho chinapezeka mʼthumba mwa Benjamini.
ויקרעו שמלתם ויעמס איש על חמרו וישבו העירה׃ | 13 |
Apo onse anangʼamba zovala zawo ndi chisoni. Ndipo anasenzetsa abulu katundu wawo nabwerera ku mzinda konkuja.
ויבא יהודה ואחיו ביתה יוסף והוא עודנו שם ויפלו לפניו ארצה׃ | 14 |
Pamene Yuda ndi abale ake ankafika ku nyumba kwa Yosefe nʼkuti Yosefe akanali komweko. Ndipo anadzigwetsa pansi pamaso pake.
ויאמר להם יוסף מה המעשה הזה אשר עשיתם הלוא ידעתם כי נחש ינחש איש אשר כמני׃ | 15 |
Yosefe anafunsa kuti, “Nʼchiyani mwachitachi? Kodi simudziwa kuti munthu ngati ine ndikhoza kuona zinthu mwakuwombeza?”
ויאמר יהודה מה נאמר לאדני מה נדבר ומה נצטדק האלהים מצא את עון עבדיך הננו עבדים לאדני גם אנחנו גם אשר נמצא הגביע בידו׃ | 16 |
Yuda anayankha, “Kodi tinganenenji kwa mbuye wanga? Tinena chiyani? Tingadzilungamitse bwanji? Mulungu waulula kulakwa kwa antchito anu. Ndipo tsopano ndife akapolo a mbuye wanga, ife tonse pamodzi ndi amene wapezeka ndi chikhocho.”
ויאמר חלילה לי מעשות זאת האיש אשר נמצא הגביע בידו הוא יהיה לי עבד ואתם עלו לשלום אל אביכם׃ | 17 |
Koma Yosefe anati, “Sindingachite choncho ayi! Yekhayo amene wapezeka ndi chikhocho ndi amene akhale kapolo wanga. Ena nonsenu, bwererani kwa abambo anu mu mtendere.”
ויגש אליו יהודה ויאמר בי אדני ידבר נא עבדך דבר באזני אדני ואל יחר אפך בעבדך כי כמוך כפרעה׃ | 18 |
Ndipo Yuda anamuyandikira iye nati, “Chonde mbuye wanga mulole kapolo wanune ndinene mawu pangʼono kwa mbuye wanga. Musandipsere mtima, kapolo wanune, popeza inu muli ngati Farao yemwe.
אדני שאל את עבדיו לאמר היש לכם אב או אח׃ | 19 |
Mbuye wanga munafunsa akapolo anufe kuti, ‘Kodi muli ndi abambo anu kapena mʼbale wanu?’
ונאמר אל אדני יש לנו אב זקן וילד זקנים קטן ואחיו מת ויותר הוא לבדו לאמו ואביו אהבו׃ | 20 |
Ndipo ife tinayankha, ‘Inde mbuye wathu, ife tili ndi abambo athu wokalamba, ndipo pali mwana wamwamuna wamngʼono amene anabadwa abambo athu atakalamba kale. Mʼbale wake anafa ndipo ndi yekhayo mʼmimba mwa amayi ake amene watsala ndipo abambo ake amamukonda.’
ותאמר אל עבדיך הורדהו אלי ואשימה עיני עליו׃ | 21 |
“Ndipo inu munatiwuza kuti, ‘Mubwere naye kwa ine kuti ndidzamuone ndekha.’
ונאמר אל אדני לא יוכל הנער לעזב את אביו ועזב את אביו ומת׃ | 22 |
Ife tinati, ‘Mbuye wathu, mnyamatayo sangasiye abambo ake, akawasiya ndiye kuti abambo akewo adzafa.’
ותאמר אל עבדיך אם לא ירד אחיכם הקטן אתכם לא תספון לראות פני׃ | 23 |
Koma inu munatichenjeza kuti, ‘Pokhapokha mutabwera naye mʼbale wanu wamngʼono kwambiri, simudzandionanso.’
ויהי כי עלינו אל עבדך אבי ונגד לו את דברי אדני׃ | 24 |
Ndiye pamene tinafika kwa kapolo wanu, abambo athu tinawawuza zonse zimene munanena.
ויאמר אבינו שבו שברו לנו מעט אכל׃ | 25 |
“Abambo athu anatiwuza kuti, ‘Pitaninso mukagule kachakudya pangʼono.’
ונאמר לא נוכל לרדת אם יש אחינו הקטן אתנו וירדנו כי לא נוכל לראות פני האיש ואחינו הקטן איננו אתנו׃ | 26 |
Koma tinati, ‘Sitingathe kupitanso. Sitingapite pokhapokha mngʼono wathuyu apite nafe chifukwa munthu uja anati sitingaonane naye ngati mngʼono wathuyu sakhala nafe.’
ויאמר עבדך אבי אלינו אתם ידעתם כי שנים ילדה לי אשתי׃ | 27 |
“Koma kapolo wanu, abambo athu anatiwuza kuti, ‘Inu mukudziwa kuti mkazi wanga anandiberekera ana aamuna awiri.
ויצא האחד מאתי ואמר אך טרף טרף ולא ראיתיו עד הנה׃ | 28 |
Mmodzi wa iwo anandisiya. Ine ndimati anadyedwa ndi chirombo popeza sindinamuonenso mpaka lero.
ולקחתם גם את זה מעם פני וקרהו אסון והורדתם את שיבתי ברעה שאלה׃ (Sheol ) | 29 |
Tsopano mukanditengeranso uyu, nakaphedwa mu njira ndiye kuti mudzandikankhira ku manda ndi chisoni.’ (Sheol )
ועתה כבאי אל עבדך אבי והנער איננו אתנו ונפשו קשורה בנפשו׃ | 30 |
“Tsono ngati tizibwerera kwa mtumiki wanu, abambo athu popanda mnyamatayu, amene moyo wa abambo ake uli pa iyeyu,
והיה כראותו כי אין הנער ומת והורידו עבדיך את שיבת עבדך אבינו ביגון שאלה׃ (Sheol ) | 31 |
ndipo akakaona kuti mnyamatayu palibe, basi akafa. Ife tidzakhala ngati takankhira abambo athu ku manda ndi chisoni. (Sheol )
כי עבדך ערב את הנער מעם אבי לאמר אם לא אביאנו אליך וחטאתי לאבי כל הימים׃ | 32 |
Ndiponsotu ine ndinadzipereka kwa abambo anga kukhala chikole chotsimikiza kuti mnyamatayu ndidzamuteteza, ndipo ndinati, ‘Ngati sindibwerera naye mnyamatayu kwa inu, ndiye kuti ndidzakhala wochimwira inu abambo anga moyo wanga wonse.’
ועתה ישב נא עבדך תחת הנער עבד לאדני והנער יעל עם אחיו׃ | 33 |
“Tsono, chonde mulole kuti ine kapolo wanu nditsalire kuno kukhala kapolo wa mbuye wathu mʼmalo mwa mnyamatayu. Koma iye apite pamodzi ndi abale akewa.
כי איך אעלה אל אבי והנער איננו אתי פן אראה ברע אשר ימצא את אבי׃ | 34 |
Ndingabwerere bwanji kwa abambo anga ngati sindingapite ndi mnyamatayu? Ayi! Sindifuna kukaona tsoka limene lingakagwere abambo anga.”