< בראשית 42 >
וירא יעקב כי יש שבר במצרים ויאמר יעקב לבניו למה תתראו׃ | 1 |
Yakobo atamva kuti ku Igupto kuli tirigu, anati kwa ana ake, “Nʼchifukwa chiyani mukungoyangʼanana wina ndi mnzake?
ויאמר הנה שמעתי כי יש שבר במצרים רדו שמה ושברו לנו משם ונחיה ולא נמות׃ | 2 |
Ine ndamva kuti ku Igupto kuli tirigu. Pitani kumeneko mukatigulireko kuti tisafe ndi njala.”
וירדו אחי יוסף עשרה לשבר בר ממצרים׃ | 3 |
Choncho abale ake khumi a Yosefe anapita kukagula tirigu ku Igupto.
ואת בנימין אחי יוסף לא שלח יעקב את אחיו כי אמר פן יקראנו אסון׃ | 4 |
Koma Yakobo sanamulole Benjamini mngʼono wake wa Yosefe kuti apite nawo chifukwa anaopa kuti choyipa chingamuchitikire.
ויבאו בני ישראל לשבר בתוך הבאים כי היה הרעב בארץ כנען׃ | 5 |
Choncho ana a Israeli aja anapita pamodzi ndi gulu la anzawo kukagula tirigu pakuti ku Kanaani kunalinso njala.
ויוסף הוא השליט על הארץ הוא המשביר לכל עם הארץ ויבאו אחי יוסף וישתחוו לו אפים ארצה׃ | 6 |
Pakuti Yosefe anali nduna yayikulu yolamulira dziko la Igupto, ndiye kuti analinso amene ankagulitsa tirigu kwa anthu onse. Choncho abale ake a Yosefe nawonso anabwera, ndipo anamugwadira pansi.
וירא יוסף את אחיו ויכרם ויתנכר אליהם וידבר אתם קשות ויאמר אלהם מאין באתם ויאמרו מארץ כנען לשבר אכל׃ | 7 |
Yosefe atangowaona abale ake anawazindikira, koma ananamizira kukhala ngati mlendo nawayankhula mwaukali kuwafunsa kuti, “Mwachokera kuti?” Iwo anayankha, “Ku dziko la Kanaani, tikudzagula chakudya.”
ויכר יוסף את אחיו והם לא הכרהו׃ | 8 |
Ngakhale Yosefe anawazindikira abale ake, koma iwo sanamuzindikire.
ויזכר יוסף את החלמות אשר חלם להם ויאמר אלהם מרגלים אתם לראות את ערות הארץ באתם׃ | 9 |
Pamenepo anakumbukira maloto aja amene analota za iwo ndipo anati, “Inu ndinu akazitape! Mwabwera kudzazonda dziko lathu kuti muone pamene palibe chitetezo.”
ויאמרו אליו לא אדני ועבדיך באו לשבר אכל׃ | 10 |
Iwo anayankha, “Ayi mbuye wathu, antchito anufe tabwera kudzagula chakudya.
כלנו בני איש אחד נחנו כנים אנחנו לא היו עבדיך מרגלים׃ | 11 |
Tonse ndife ana a munthu mmodzi. Ndife antchito anu okhulupirika osati akazitape.”
ויאמר אלהם לא כי ערות הארץ באתם לראות׃ | 12 |
Iye anawawuza kuti, “Ayi! Inu mwabwera kudzaona pamene palibe chitetezo mʼdziko muno.”
ויאמרו שנים עשר עבדיך אחים אנחנו בני איש אחד בארץ כנען והנה הקטן את אבינו היום והאחד איננו׃ | 13 |
Koma iwo anayankha, “Tinalipo ana aamuna khumi ndi awiri. Abambo athu ndi mmodzi, ndipo kwathu ndi ku Kanaani. Panopo wotsiriza ali ndi abambo athu ndipo wina anamwalira.”
ויאמר אלהם יוסף הוא אשר דברתי אלכם לאמר מרגלים אתם׃ | 14 |
Yosefe anawawuza kuti, “Ndi momwe ndaneneramo: Inu ndinu akazitape.
בזאת תבחנו חי פרעה אם תצאו מזה כי אם בבוא אחיכם הקטן הנה׃ | 15 |
Ndiye ndikuyesani motere: Ine ndikulumbira pali Farao ndithu, inuyo simudzachoka malo ano mpaka wotsirizayo atabwera kuno.
שלחו מכם אחד ויקח את אחיכם ואתם האסרו ויבחנו דבריכם האמת אתכם ואם לא חי פרעה כי מרגלים אתם׃ | 16 |
Tumizani mmodzi wa inu akamutenge mʼbale wanuyo ndipo ena nonsenu musungidwa mʼndende, kuti titsimikize ngati zimene mukunenazi ndi zoona. Apo ayi, pali Farao ndithu, inu ndinu akazitape!”
ויאסף אתם אל משמר שלשת ימים׃ | 17 |
Ndipo onse anawayika mʼndende kwa masiku atatu.
ויאמר אלהם יוסף ביום השלישי זאת עשו וחיו את האלהים אני ירא׃ | 18 |
Pa tsiku lachitatu Yosefe anawawuza kuti, “Popeza ine ndimaopa Mulungu, ndipo inuyo ngati mukufuna kukhala ndi moyo muchite izi:
אם כנים אתם אחיכם אחד יאסר בבית משמרכם ואתם לכו הביאו שבר רעבון בתיכם׃ | 19 |
Ngati muli anthu achilungamo, mmodzi wa inu atsale mʼndende, pamene ena nonse mupite kwanu kuti muwatengere chakudya anthu akwanu kuli njalako.
ואת אחיכם הקטן תביאו אלי ויאמנו דבריכם ולא תמותו ויעשו כן׃ | 20 |
Mukabwere naye kuno mngʼono wanu wotsirizayo kuti titsimikizire zimene munanena kuti musafe.” Ndipo anachita zomwezo.
ויאמרו איש אל אחיו אבל אשמים אנחנו על אחינו אשר ראינו צרת נפשו בהתחננו אלינו ולא שמענו על כן באה אלינו הצרה הזאת׃ | 21 |
Iwo anati kwa wina ndi mnzake, “Ndithu ife tinalakwira mʼbale wathu uja popeza kuti ngakhale tinaona kuvutika kwake ndi kumva kulira kwake pamene ankatidandaulira kuti timuchitire chifundo, koma ife sitinamvere. Nʼchifukwa chake masautso awa atigwera.”
ויען ראובן אתם לאמר הלוא אמרתי אליכם לאמר אל תחטאו בילד ולא שמעתם וגם דמו הנה נדרש׃ | 22 |
Rubeni anayankha, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musamuchite kanthu mnyamata uja? Koma inu simunamvere! Tsopano tikulandira malipiro a magazi ake.”
והם לא ידעו כי שמע יוסף כי המליץ בינתם׃ | 23 |
Koma sanadziwe kuti Yosefe ankawamva popeza kuti ankagwiritsa ntchito wotanthauzira poyankhula naye.
ויסב מעליהם ויבך וישב אלהם וידבר אלהם ויקח מאתם את שמעון ויאסר אתו לעיניהם׃ | 24 |
Yosefe anapita pambali payekha kukalira. Kenaka anabweranso nadzayankhula nawo. Iye anatenga Simeoni namumanga iwo akuona.
ויצו יוסף וימלאו את כליהם בר ולהשיב כספיהם איש אל שקו ולתת להם צדה לדרך ויעש להם כן׃ | 25 |
Yosefe analamula kuti awadzazire matumba awo ndi tirigu, awayikiremo ndalama zawo momwemo ndiponso awapatse chakudya cha panjira. Izi anawachitiradi.
וישאו את שברם על חמריהם וילכו משם׃ | 26 |
Abale a Yosefe aja anasenzetsa abulu awo tirigu amene anagula uja ndipo ananyamuka ulendo wawo.
ויפתח האחד את שקו לתת מספוא לחמרו במלון וירא את כספו והנה הוא בפי אמתחתו׃ | 27 |
Atafika pamalo pena poti agone, mmodzi mwa iwo anatsekula thumba lake kuti atapemo chakudya cha bulu wake. Atangomasula anaona kuti ndalama zake zili pakamwa pa thumba.
ויאמר אל אחיו הושב כספי וגם הנה באמתחתי ויצא לבם ויחרדו איש אל אחיו לאמר מה זאת עשה אלהים לנו׃ | 28 |
Iye anati kwa abale akewo, “Ndalama zanga andibwezera, izi zili mʼthumba mwangamu.” Mitima yawo inachita ngati yachokamo ndipo anali ndi mantha ambiri, nati, “Ndi chiyani chimene Mulungu watichitira?”
ויבאו אל יעקב אביהם ארצה כנען ויגידו לו את כל הקרת אתם לאמר׃ | 29 |
Atafika kwa abambo awo Yakobo mʼdziko la Kanaani anafotokoza zonse zimene zinawachitikira nati,
דבר האיש אדני הארץ אתנו קשות ויתן אתנו כמרגלים את הארץ׃ | 30 |
“Nduna yayikulu ya mʼdzikomo inatiyankhula mwa ukali kwambiri ndipo inkatiyesa kuti ndife akazitape.
ונאמר אליו כנים אנחנו לא היינו מרגלים׃ | 31 |
Koma tinamuwuza kuti, ‘Ndife anthu woona mtima osati akazitape.
שנים עשר אנחנו אחים בני אבינו האחד איננו והקטן היום את אבינו בארץ כנען׃ | 32 |
Ife tonse tinalipo ana aamuna khumi ndi awiri, abambo mmodzi. Mmodzi anamwalira, ndipo wamngʼono ali ndi abambo athu ku Kanaani.’”
ויאמר אלינו האיש אדני הארץ בזאת אדע כי כנים אתם אחיכם האחד הניחו אתי ואת רעבון בתיכם קחו ולכו׃ | 33 |
Ndipo nduna ija inati kwa ife, “Kuti ndidziwedi kuti ndinu anthu owona mtima muchite izi: Mmodzi mwa inu atsale ndi ine kuno, ndipo enanu mutenge chakudya ndi kubwerera kwanu kumene kuli njalako.
והביאו את אחיכם הקטן אלי ואדעה כי לא מרגלים אתם כי כנים אתם את אחיכם אתן לכם ואת הארץ תסחרו׃ | 34 |
Koma mundibweretsere wotsirizayo kuti ndidziwedi kuti sindinu akazitape koma anthu achilungamo. Kenaka ndidzakubwezerani mʼbale wanuyu ndipo mukhoza kuchita malonda mʼdzikoli.”
ויהי הם מריקים שקיהם והנה איש צרור כספו בשקו ויראו את צררות כספיהם המה ואביהם וייראו׃ | 35 |
Pamene amakhuthula matumba awo a tirigu aliyense anapeza kuti kathumba kake ka ndalama kali momwemo. Ataona zimenezi, iwo pamodzi ndi abambo awo anachita mantha kwambiri.
ויאמר אלהם יעקב אביהם אתי שכלתם יוסף איננו ושמעון איננו ואת בנימן תקחו עלי היו כלנה׃ | 36 |
Abambo awo Yakobo anawawuza kuti, “Mwandilanda ana anga ine. Yosefe anamwalira ndipo Simeoni palibenso, ndiye tsopano mukufuna mutengenso Benjamini. Zonsezi zandigwera ine!”
ויאמר ראובן אל אביו לאמר את שני בני תמית אם לא אביאנו אליך תנה אתו על ידי ואני אשיבנו אליך׃ | 37 |
Koma Rubeni anati kwa abambo ake, “Ngati sindidzabwera naye kwa inu, mudzaphe ana anga aamuna awiri. Muperekeni mʼmanja mwangamu ndipo ndidzamusamala ndi kubwera naye kwa inu.”
ויאמר לא ירד בני עמכם כי אחיו מת והוא לבדו נשאר וקראהו אסון בדרך אשר תלכו בה והורדתם את שיבתי ביגון שאולה׃ (Sheol ) | 38 |
Koma Yakobo anati, “Mwana wanga sapita nanu kumeneko; mkulu wake anamwalira ndipo watsala yekha. Ngati choyipa chitamuchitikira pa ulendo mukupitawu, ndiye kuti ndi mmene ndakalambiramu inu mudzandipha ndi chisoni chotere.” (Sheol )