< בראשית 25 >

ויסף אברהם ויקח אשה ושמה קטורה׃ 1
Abrahamu anakwatira mkazi wina dzina lake Ketura.
ותלד לו את זמרן ואת יקשן ואת מדן ואת מדין ואת ישבק ואת שוח׃ 2
Iyeyu anamubalira Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa.
ויקשן ילד את שבא ואת דדן ובני דדן היו אשורם ולטושים ולאמים׃ 3
Yokisani anabereka Seba ndi Dedani ndipo zidzukulu za Dedani ndiwo Aasuri, Aletusi, ndi Aleumi.
ובני מדין עיפה ועפר וחנך ואבידע ואלדעה כל אלה בני קטורה׃ 4
Ana aamuna a Midiyani anali, Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida. Onsewa anali zidzukulu za Ketura.
ויתן אברהם את כל אשר לו ליצחק׃ 5
Abrahamu anasiyira Isake chilichonse anali nacho.
ולבני הפילגשים אשר לאברהם נתן אברהם מתנת וישלחם מעל יצחק בנו בעודנו חי קדמה אל ארץ קדם׃ 6
Koma pamene anali ndi moyo, Abrahamu anapereka mphatso kwa ana aakazi ake ena onse. Kenaka anawatumiza ku dziko la kummawa kuti akhale kutali ndi mwana wake Isake.
ואלה ימי שני חיי אברהם אשר חי מאת שנה ושבעים שנה וחמש שנים׃ 7
Abrahamu anakhala ndi moyo zaka 175.
ויגוע וימת אברהם בשיבה טובה זקן ושבע ויאסף אל עמיו׃ 8
Abrahamu anamwalira atakalamba kwambiri ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.
ויקברו אתו יצחק וישמעאל בניו אל מערת המכפלה אל שדה עפרן בן צחר החתי אשר על פני ממרא׃ 9
Ana ake, Isake ndi Ismaeli anamuyika mʼphanga la Makipela pafupi ndi Mamre, mʼmunda umene kale unali wa Efroni mwana wa Zohari Mhiti,
השדה אשר קנה אברהם מאת בני חת שמה קבר אברהם ושרה אשתו׃ 10
uwu ndi munda umene Abrahamu anagula kwa Ahiti. Kumeneko Abrahamu anakayikidwa pamodzi ndi mkazi wake Sara.
ויהי אחרי מות אברהם ויברך אלהים את יצחק בנו וישב יצחק עם באר לחי ראי׃ 11
Atamwalira Abrahamu, Mulungu anadalitsa mwana wake Isake, amene ankakhala pafupi ndi Beeri-lahai-roi (chitsime cha Wamoyo Wondipenya).
ואלה תלדת ישמעאל בן אברהם אשר ילדה הגר המצרית שפחת שרה לאברהם׃ 12
Nazi zidzukulu za Ismaeli, mwana wa Abrahamu amene wantchito wa Sara, Hagara Mwigupto uja, anaberekera Abrahamu.
ואלה שמות בני ישמעאל בשמתם לתולדתם בכר ישמעאל נבית וקדר ואדבאל ומבשם׃ 13
Awa ndi mayina a ana a Ismaeli monga mwa mndandanda wa mabadwidwe awo: Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli; kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu,
ומשמע ודומה ומשא׃ 14
Misima, Duma, Masa,
חדד ותימא יטור נפיש וקדמה׃ 15
Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema;
אלה הם בני ישמעאל ואלה שמתם בחצריהם ובטירתם שנים עשר נשיאם לאמתם׃ 16
Amenewa ndi ana a Ismaeli ndi mayina awo monga mwa midzi ndi misasa yawo. Anali olamulira mafuko khumi ndi awiri.
ואלה שני חיי ישמעאל מאת שנה ושלשים שנה ושבע שנים ויגוע וימת ויאסף אל עמיו׃ 17
Ismaeli anakhala ndi moyo zaka 137. Iye anamwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.
וישכנו מחוילה עד שור אשר על פני מצרים באכה אשורה על פני כל אחיו נפל׃ 18
Zidzukulu za Ismaeli zinkakhala mʼdera la pakati pa Havila ndi Suri, kummwera kwa Igupto, mukamapita cha ku Asuri. Choncho anakhala kummawa kwa abale awo.
ואלה תולדת יצחק בן אברהם אברהם הוליד את יצחק׃ 19
Iyi ndi mbiri ya Isake mwana wa Abrahamu. Abrahamu anabereka Isake
ויהי יצחק בן ארבעים שנה בקחתו את רבקה בת בתואל הארמי מפדן ארם אחות לבן הארמי לו לאשה׃ 20
ndipo Isake anali ndi zaka makumi anayi pamene anakwatira Rebeka mwana wa Betueli Mwaramu wa ku Padanaramu mlongo wa Labani Mwaramu.
ויעתר יצחק ליהוה לנכח אשתו כי עקרה הוא ויעתר לו יהוה ותהר רבקה אשתו׃ 21
Isake anapempherera mkazi wake kwa Yehova popeza iye anali wosabereka. Yehova anayankha pemphero lake ndipo mkazi wake Rebeka anatenga pathupi.
ויתרצצו הבנים בקרבה ותאמר אם כן למה זה אנכי ותלך לדרש את יהוה׃ 22
Koma pamene anawo amalimbana mʼmimba mwake, iye anati, “Bwanji zikundichitikira zoterezi?” Choncho anapita kukafunsa kwa Yehova.
ויאמר יהוה לה שני גיים בבטנך ושני לאמים ממעיך יפרדו ולאם מלאם יאמץ ורב יעבד צעיר׃ 23
Yehova anati kwa iye, “Udzabala mafuko awiri a anthu olimbana, ndipo magulu awiri a anthu ochokera mwa iwe adzasiyana; fuko limodzi lidzakhala la mphamvu kuposa linzake, ndipo wamkulu adzatumikira wamngʼono.”
וימלאו ימיה ללדת והנה תומם בבטנה׃ 24
Pamene nthawi inakwana yakuti abeleke, Rebeka anaberekadi mapasa.
ויצא הראשון אדמוני כלו כאדרת שער ויקראו שמו עשו׃ 25
Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala cha ubweya; choncho anamutcha Esau.
ואחרי כן יצא אחיו וידו אחזת בעקב עשו ויקרא שמו יעקב ויצחק בן ששים שנה בלדת אתם׃ 26
Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa.
ויגדלו הנערים ויהי עשו איש ידע ציד איש שדה ויעקב איש תם ישב אהלים׃ 27
Anyamatawo anakula ndipo Esau anakhala katswiri wosaka, munthu wamʼthengo, pamene Yakobo anali munthu wofatsa, wokonda kukhala pa nyumba.
ויאהב יצחק את עשו כי ציד בפיו ורבקה אהבת את יעקב׃ 28
Isake ankakonda Esau chifukwa cha nyama za kutchire zomwe ankakonda kudya, koma Rebeka ankakonda Yakobo.
ויזד יעקב נזיד ויבא עשו מן השדה והוא עיף׃ 29
Tsiku lina pamene Yakobo ankaphika chakudya, Esau anabwera kuchokera kuthengo ali wolefuka ndi njala.
ויאמר עשו אל יעקב הלעיטני נא מן האדם האדם הזה כי עיף אנכי על כן קרא שמו אדום׃ 30
Iye anati kwa Yakobo, “Tandipatsako phala lofiiralo, ndimwe! Ndalefuka ndi njala.” (Nʼchifukwa chake amatchedwanso Edomu).
ויאמר יעקב מכרה כיום את בכרתך לי׃ 31
Yakobo anayankha, “Choyamba undigulitse ukulu wako.”
ויאמר עשו הנה אנכי הולך למות ולמה זה לי בכרה׃ 32
Esau anati, “Chabwino, ine ndatsala pangʼono kufa, ukulu undithandiza chiyani?”
ויאמר יעקב השבעה לי כיום וישבע לו וימכר את בכרתו ליעקב׃ 33
Koma Yakobo anati, “Lumbira kwa ine choyamba.” Kotero Esau analumbiradi, ndipo anagulitsa ukulu wake kwa Yakobo.
ויעקב נתן לעשו לחם ונזיד עדשים ויאכל וישת ויקם וילך ויבז עשו את הבכרה׃ 34
Choncho Yakobo anamupatsa Esau buledi ndi phala lofiira lija. Iye anadya ndi kumwa, nanyamuka kumapita. Motero Esau anapeputsa ukulu wake wachisamba uja.

< בראשית 25 >