< בראשית 23 >

ויהיו חיי שרה מאה שנה ועשרים שנה ושבע שנים שני חיי שרה׃ 1
Sara anakhala ndi moyo zaka 127.
ותמת שרה בקרית ארבע הוא חברון בארץ כנען ויבא אברהם לספד לשרה ולבכתה׃ 2
Anamwalirira ku Kiriyati-Araba, kumeneku ndi ku Hebroni, mʼdziko la Kanaani, ndipo Abrahamu anapita kukakhuza maliro a Sara, namulirira.
ויקם אברהם מעל פני מתו וידבר אל בני חת לאמר׃ 3
Kenaka Abrahamu ananyamuka pamene panali mtembo wa mkazi wakepo kupita kukayankhula ndi anthu a ku Hiti. Ndipo anati,
גר ותושב אנכי עמכם תנו לי אחזת קבר עמכם ואקברה מתי מלפני׃ 4
“Ine ndine mlendo wongoyendayenda kwanu kuno. Bwanji mundigulitse malo woti akhale manda kuti ndiyikepo thupi la mkazi wanga.”
ויענו בני חת את אברהם לאמר לו׃ 5
Anthu a ku Hiti aja anamuyankha Abrahamu kuti,
שמענו אדני נשיא אלהים אתה בתוכנו במבחר קברינו קבר את מתך איש ממנו את קברו לא יכלה ממך מקבר מתך׃ 6
“Tatimverani mbuye wathu, inu ndinu mwana wa mfumu wamkulu pakati pathu. Chonde ikani thupi la mkazi wanu mʼmanda aliwonse amene mungafune. Palibe mmodzi wa ife amene adzakukanizani manda ake kuti musayike mkazi wanu.”
ויקם אברהם וישתחו לעם הארץ לבני חת׃ 7
Tsono Abrahamu anayimirira naweramira anthu a dziko la Hiti aja
וידבר אתם לאמר אם יש את נפשכם לקבר את מתי מלפני שמעוני ופגעו לי בעפרון בן צחר׃ 8
nati, “Ngati mwaloladi kuti ndiyike mkazi wanga kuno, ndiye ndimvereni. Mundipemphere kwa Efroni mwana wa Zohari
ויתן לי את מערת המכפלה אשר לו אשר בקצה שדהו בכסף מלא יתננה לי בתוככם לאחזת קבר׃ 9
kuti andigulitse phanga la Makipela, limene lili kumapeto kwa munda wake. Mumupemphe kuti andigulitse pamtengo wake ndithu inu mukuona kuti akhale manda.”
ועפרון ישב בתוך בני חת ויען עפרון החתי את אברהם באזני בני חת לכל באי שער עירו לאמר׃ 10
Pamenepo nʼkuti Efroni Mhiti ali pomwepo pakati pa anthuwo amene anabwera ku chipata cha mzindawo. Ndipo onse akumva anamuyankha Abrahamu
לא אדני שמעני השדה נתתי לך והמערה אשר בו לך נתתיה לעיני בני עמי נתתיה לך קבר מתך׃ 11
nati, “Ayi mbuye wanga tandimverani, ine ndikukupatsani mundawo ndiponso phanga limene lili mʼmenemo. Ndikukupatsani malowa pamaso pa anthu a mtundu wanga. Chonde ikani mtembo wamkazi wanu.”
וישתחו אברהם לפני עם הארץ׃ 12
Apo Abrahamu anaweramanso mwaulemu pamaso pa anthu a mʼdzikolo
וידבר אל עפרון באזני עם הארץ לאמר אך אם אתה לו שמעני נתתי כסף השדה קח ממני ואקברה את מתי שמה׃ 13
ndipo anthu onse akumva Abrahamu anati kwa Efroni, “Ngati kungatheke, chonde ndimvereni. Ine ndichita kugula mundawu. Landirani ndalama za mundawu kuti ine ndiyike mkazi wanga mʼmenemo.”
ויען עפרון את אברהם לאמר לו׃ 14
Koma Efroni anamuyankha Abrahamu nati,
אדני שמעני ארץ ארבע מאת שקל כסף ביני ובינך מה הוא ואת מתך קבר׃ 15
“Mundimvere mbuye wanga; mundawo mtengo wake ndi masekeli asiliva okwana 400. Koma zimenezo nʼchiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani mtembo wa mkazi wanu.”
וישמע אברהם אל עפרון וישקל אברהם לעפרן את הכסף אשר דבר באזני בני חת ארבע מאות שקל כסף עבר לסחר׃ 16
Abrahamu anavomera mtengo umene ananena Efroni Ahiti onse akumva ndipo anamuwerengera masekeli asiliva okwana 400 monga mwa mtengo wa ndalama umene amalonda a nthawi imeneyo ankagwiritsa ntchito.
ויקם שדה עפרון אשר במכפלה אשר לפני ממרא השדה והמערה אשר בו וכל העץ אשר בשדה אשר בכל גבלו סביב׃ 17
Choncho munda wa Efroni wa ku Makipela umene unali kufupi ndi Mamre, kuphatikiza munda, phanga linali mʼmenemo pamodzi ndi mitengo yonse ya mʼmundamo, zinaperekedwa
לאברהם למקנה לעיני בני חת בכל באי שער עירו׃ 18
kwa Abrahamu ngati chuma chake pamaso pa anthu onse a ku Hiti amene anabwera ku chipata cha mzindawo.
ואחרי כן קבר אברהם את שרה אשתו אל מערת שדה המכפלה על פני ממרא הוא חברון בארץ כנען׃ 19
Zitatha izi, Abrahamu anayika mkazi wake Sara mʼphanga la mʼmunda wa ku Makipela, kufupi ndi ku Mamre (kumene ndi ku Hebroni) mʼdziko la Kanaani.
ויקם השדה והמערה אשר בו לאברהם לאחזת קבר מאת בני חת׃ 20
Choncho Ahiti anapereka munda pamodzi ndi phanga la mʼmenemo kwa Abrahamu kuti akhale manda.

< בראשית 23 >