< עזרא 4 >

וישמעו צרי יהודה ובנימן כי בני הגולה בונים היכל ליהוה אלהי ישראל׃ 1
Adani a Yuda ndi Benjamini anamva kuti anthu obwera ku ukapolo aja akumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Israeli.
ויגשו אל זרבבל ואל ראשי האבות ויאמרו להם נבנה עמכם כי ככם נדרוש לאלהיכם ולא אנחנו זבחים מימי אסר חדן מלך אשור המעלה אתנו פה׃ 2
Tsono anapita kwa Zerubabeli ndi kwa atsogoleri a mabanja awo ndi kunena kuti, “Mutilole kuti tikuthandizeni kumangaku chifukwa ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthawi ya Esrahadoni, mfumu ya ku Asiriya, amene anabwera nafe kuno.”
ויאמר להם זרבבל וישוע ושאר ראשי האבות לישראל לא לכם ולנו לבנות בית לאלהינו כי אנחנו יחד נבנה ליהוה אלהי ישראל כאשר צונו המלך כורש מלך פרס׃ 3
Koma Zerubabeli, Yesuwa ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a Aisraeli anayankha kuti, “Inu simungatithandize kumangira Nyumba Yehova, Mulungu wathu. Tokha tidzamumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Aisraeli, monga mfumu Koresi, mfumu ya Perisiya inatilamulira.”
ויהי עם הארץ מרפים ידי עם יהודה ומבלהים אותם לבנות׃ 4
Tsono anthu a mʼdzikomo anayamba kuchititsa ulesi anthu a ku Yuda, ndi kuwachititsa mantha kuti aleke ntchito yomangayo.
וסכרים עליהם יועצים להפר עצתם כל ימי כורש מלך פרס ועד מלכות דריוש מלך פרס׃ 5
Analemba alangizi ena kuti alepheretse cholinga chawo pa ntchitoyo pa nthawi yonse ya Koresi, mfumu ya ku Perisiya, ndiponso mpaka pamene Dariyo mfumu ya ku Perisiya ankalamulira dzikolo.
ובמלכות אחשורוש בתחלת מלכותו כתבו שטנה על ישבי יהודה וירושלם׃ 6
Mfumu Ahasiwero atangoyamba kulamulira dzikolo, adani aja analemba kalata yoneneza anthu a Yuda ndi Yerusalemu.
ובימי ארתחששתא כתב בשלם מתרדת טבאל ושאר כנותו על ארתחששתא מלך פרס וכתב הנשתון כתוב ארמית ומתרגם ארמית׃ 7
Ndiponso mʼnthawi ya Aritasasita mfumu ya Perisiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli ndi anzawo ena analemba kalata inanso kwa Aritasasita. Kalatayo inalembedwa mʼChiaramu ndipo ankatanthauzira poyiwerenga.
רחום בעל טעם ושמשי ספרא כתבו אגרה חדה על ירושלם לארתחששתא מלכא כנמא׃ 8
Rehumu mkulu wankhondo ndi Simisai mlembi, nawonso analemba kalata yawo yoneneza anthu a ku Yerusalemu kwa mfumu Aritasasita. Anayilemba motere:
אדין רחום בעל טעם ושמשי ספרא ושאר כנותהון דיניא ואפרסתכיא טרפליא אפרסיא ארכוי בבליא שושנכיא דהוא עלמיא׃ 9
Kalata yochokera kwa Rehumu, mkulu wa gulu lankhondo, mlembi Simisai ndi anzawo awa: oweruza, nduna, akuluakulu ena, anthu a ku Peresiya, Ereki, Babuloni, Susa mʼdziko la Elamu,
ושאר אמיא די הגלי אסנפר רבא ויקירא והותב המו בקריה די שמרין ושאר עבר נהרה וכענת׃ 10
ndi mitundu ina imene mkulu wolemekezeka, Osanipara anayisamutsa ndi kuyikhazika mʼmizinda ya Samariya ndi mʼmadera ena apatsidya la Yufurate.
דנה פרשגן אגרתא די שלחו עלוהי על ארתחששתא מלכא עבדיך אנש עבר נהרה וכענת׃ 11
Mawu a mʼkalata ya kwa Aritasasita anali awa: Kwa mfumu Aritasasita: Kuchokera kwa atumiki anu, anthu a kutsidya kwa Yufurate:
ידיע להוא למלכא די יהודיא די סלקו מן לותך עלינא אתו לירושלם קריתא מרדתא ובאישתא בנין ושורי אשכללו ואשיא יחיטו׃ 12
Amfumu tati mudziwe kuti Ayuda amene anabwera kuno kuchokera kwanuko apita ku Yerusalemu ndipo akumanganso mzinda wa anthu owukira ndi oyipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonzanso maziko.
כען ידיע להוא למלכא די הן קריתא דך תתבנא ושוריה ישתכללון מנדה בלו והלך לא ינתנון ואפתם מלכים תהנזק׃ 13
Kuwonjeza apo amfumu mudziwe kuti ngati amalize kumanganso mzindawu ndi kukonzanso makoma ake, adzaleka kukhoma msonkho, kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko kapena msonkho wina uliwonse, ndipo chuma cha thumba la ufumu chidzachepa.
כען כל קבל די מלח היכלא מלחנא וערות מלכא לא אריך לנא למחזא על דנה שלחנא והודענא למלכא׃ 14
Popeza tsono ife timadya nawo kwa mfumu sitiyenera tizingoonerera zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nʼchifukwa chake tikutumiza uthenga kwa inu a mfumu kuti mudziwe zonse.
די יבקר בספר דכרניא די אבהתך ותהשכח בספר דכרניא ותנדע די קריתא דך קריא מרדא ומהנזקת מלכין ומדנן ואשתדור עבדין בגוה מן יומת עלמא על דנה קריתא דך החרבת׃ 15
Choncho pachitike kafukufuku mʼbuku la mbiri yakale ya makolo anu. Mʼbuku la mbiri zakale mudzapezamo ndi kuwerenga kuti mzinda umenewu ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zamʼmadera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuwukira ulamuliro uliwonse. Nʼchifukwa chake mzinda umenewu anawuwononga.
מהודעין אנחנה למלכא די הן קריתא דך תתבנא ושוריה ישתכללון לקבל דנה חלק בעבר נהרא לא איתי לך׃ 16
Tsono tikukudziwitsani amfumu kuti ngati mzinda umenewu umangidwanso ndi makoma ake nʼkutsirizidwanso ndiye kuti inu simudzalamuliranso chigawo cha patsidya pa Yufurate.
פתגמא שלח מלכא על רחום בעל טעם ושמשי ספרא ושאר כנותהון די יתבין בשמרין ושאר עבר נהרה שלם וכעת׃ 17
Mfumu inatumiza yankho ili: Mkulu wa gulu lankhondo Rehumu, mlembi Simisai ndi anzanu onse amene akukhala ku Samariya ndi mʼzigawo zina zonse za Patsidya pa Yufurate. Landirani moni.
נשתונא די שלחתון עלינא מפרש קרי קדמי׃ 18
Kalata imene munatumiza ija yawerengedwa bwino lomwe pamaso panga.
ומני שים טעם ובקרו והשכחו די קריתא דך מן יומת עלמא על מלכין מתנשאה ומרד ואשתדור מתעבד בה׃ 19
Ine nditalamula kuti afufuze nkhaniyi kwapezekadi kuti mzinda umenewu uli ndi mbiri yowukira mafumu ndi kuti zaupandu ndi zowukira zinkachitikadi mʼmenemo.
ומלכין תקיפין הוו על ירושלם ושליטין בכל עבר נהרה ומדה בלו והלך מתיהב להון׃ 20
Mafumu amphamvu akhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonse cha Patsidya pa Yufurate. Iwo ankalandira msonkho ndi kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko pa kanthu kena kalikonse.
כען שימו טעם לבטלא גבריא אלך וקריתא דך לא תתבנא עד מני טעמא יתשם׃ 21
Tsopano inu khazikitsani lamulo kuti anthu amenewo asiye ntchitoyo, asamangenso mzindawo mpaka ine nditalamula
וזהירין הוו שלו למעבד על דנה למה ישגא חבלא להנזקת מלכין׃ 22
Musachedwe kuchita zimenezi. Kodi ine ndingalole bwanji kuti zowononga zotere zikule ndi kupweteka ine mfumu?
אדין מן די פרשגן נשתונא די ארתחששתא מלכא קרי קדם רחום ושמשי ספרא וכנותהון אזלו בבהילו לירושלם על יהודיא ובטלו המו באדרע וחיל׃ 23
Kalata ya mfumu Aritasasitayi itangowerengedwa pamaso pa Rehumu ndi Simisai mlembi uja, ndi anzawo onse, iwo anapita msangamsanga ku Yerusalemu kukawaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirire ntchito yawo.
באדין בטלת עבידת בית אלהא די בירושלם והות בטלא עד שנת תרתין למלכות דריוש מלך פרס׃ 24
Motero ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu inayimitsidwa mpaka chaka cha chiwiri cha ulamuliro wa Dariyo mfumu ya ku Perisiya.

< עזרא 4 >