< עזרא 3 >

ויגע החדש השביעי ובני ישראל בערים ויאספו העם כאיש אחד אל ירושלם׃ 1
Utafika mwezi wa chisanu ndi chiwiri Aisraeli atakhala kale mʼmidzi yawo, anthu anasonkhana ku Yerusalemu ndi cholinga chimodzi.
ויקם ישוע בן יוצדק ואחיו הכהנים וזרבבל בן שאלתיאל ואחיו ויבנו את מזבח אלהי ישראל להעלות עליו עלות ככתוב בתורת משה איש האלהים׃ 2
Kenaka Yesuwa mwana wa Yozadaki ndi ansembe anzake pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi abale ake anayamba kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Israeli. Anatero pofuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza monga analembera mʼbuku la Mose, munthu wa Mulungu uja.
ויכינו המזבח על מכונתיו כי באימה עליהם מעמי הארצות ויעל עליו עלות ליהוה עלות לבקר ולערב׃ 3
Ndi mantha ndi mantha chifukwa cha anthu a mʼmayikomo, iwo anamanga guwalo pa maziko ake akale, ndipo anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu pa guwapo mmawa ndi madzulo.
ויעשו את חג הסכות ככתוב ועלת יום ביום במספר כמשפט דבר יום ביומו׃ 4
Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe zinalembedwera. Ankaperekanso nsembe za tsiku ndi tsiku monga mwa chiwerengero chake potsata mwambo wake wa tsiku ndi tsiku monga zinalembedwa.
ואחריכן עלת תמיד ולחדשים ולכל מועדי יהוה המקדשים ולכל מתנדב נדבה ליהוה׃ 5
Pambuyo pake, ankapereka nsembe zopsereza, nsembe zopereka pa nthawi ya mwezi watsopano ndi za pa masiku onse a chikondwerero oyikidwa kutamandira Yehova, kudzanso nsembe zaufulu zopereka kwa Yehova.
מיום אחד לחדש השביעי החלו להעלות עלות ליהוה והיכל יהוה לא יסד׃ 6
Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, iwo anayambanso kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova, ngakhale kuti maziko a Nyumba ya Yehova anali asanamangidwe.
ויתנו כסף לחצבים ולחרשים ומאכל ומשתה ושמן לצדנים ולצרים להביא עצי ארזים מן הלבנון אל ים יפוא כרשיון כורש מלך פרס עליהם׃ 7
Ndipo anapereka ndalama kwa amisiri a miyala ndi kwa amisiri a matabwa, ndi chakudya, chakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo, kuti abweretse mitengo ya mkungudza pa nyanja kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Yopa. Zonsezi anachita malinga ndi chilolezo chimene analandira kuchokera kwa Koresi, mfumu ya Peresiya.
ובשנה השנית לבואם אל בית האלהים לירושלם בחדש השני החלו זרבבל בן שאלתיאל וישוע בן יוצדק ושאר אחיהם הכהנים והלוים וכל הבאים מהשבי ירושלם ויעמידו את הלוים מבן עשרים שנה ומעלה לנצח על מלאכת בית יהוה׃ 8
Tsono mu chaka chachiwiri atabwera ku Yerusalemu, ku malo akale a Nyumba ya Yehova, mwezi wachiwiri Zerubabeli mwana wa Sealatieli, Yesuwa mwana wa Yozadaki pamodzi ndi abale awo onse, ansembe, Alevi ndi onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo, anayamba kugwira ntchito. Iwo anasankha Alevi a zaka zoyambira makumi awiri kuti aziyangʼanira ntchito ya kumanga Nyumba ya Yehova.
ויעמד ישוע בניו ואחיו קדמיאל ובניו בני יהודה כאחד לנצח על עשה המלאכה בבית האלהים בני חנדד בניהם ואחיהם הלוים׃ 9
Yesuwa ndi ana ake aamuna kudzanso abale ake, Kadimieli ndi ana ake (ana a Yuda) onse pamodzi anasenza udindo woyangʼanira antchito ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizanso ana a Henadadi komanso Alevi, ana awo ndi abale awo.
ויסדו הבנים את היכל יהוה ויעמידו הכהנים מלבשים בחצצרות והלוים בני אסף במצלתים להלל את יהוה על ידי דויד מלך ישראל׃ 10
Amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Yehova, ansembe anabwera akuyimba malipenga, atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, anadza akuyimba matambolini ndi kutenga udindo wawo wotamanda Yehova, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraeli.
ויענו בהלל ובהודת ליהוה כי טוב כי לעולם חסדו על ישראל וכל העם הריעו תרועה גדולה בהלל ליהוה על הוסד בית יהוה׃ 11
Iwo ankayimba motamanda ndi mothokoza Yehova nyimbo iyi: “Yehova ndi wabwino; chikondi chake pa Israeli ndi chamuyaya.” Ndipo anthu onse ankafuwula kwambiri kumutamanda Yehova, chifukwa maziko a Nyumba ya Yehova anali kumangidwa.
ורבים מהכהנים והלוים וראשי האבות הזקנים אשר ראו את הבית הראשון ביסדו זה הבית בעיניהם בכים בקול גדול ורבים בתרועה בשמחה להרים קול׃ 12
Koma ambiri mwa ansembe, Alevi ndiponso atsogoleri amabanja, akuluakulu amene anaona Nyumba ya Yehova yakale, analira mokweza pamene anaona maziko a nyumbayi akumangidwa. Komanso ena ambiri ankafuwula mosangalala.
ואין העם מכירים קול תרועת השמחה לקול בכי העם כי העם מריעים תרועה גדולה והקול נשמע עד למרחוק׃ 13
Choncho panalibe amene ankatha kusiyanitsa liwu lofuwula mokondwerera ndi liwu la anthu olira, chifukwa anthuwo ankafuwula kwambiri. Ndipo liwu lofuwulalo limamveka kutali.

< עזרא 3 >