< יחזקאל 8 >

ויהי בשנה הששית בששי בחמשה לחדש אני יושב בביתי וזקני יהודה יושבים לפני ותפל עלי שם יד אדני יהוה׃ 1
Tsiku lachisanu la mwezi wachisanu ndi chimodzi, mʼchaka chachisanu ndi chimodzi, ndinakhala mʼnyumba mwanga pamodzi ndi akuluakulu a ku Yuda. Tsono mphamvu za Ambuye Yehova zinandifikira.
ואראה והנה דמות כמראה אש ממראה מתניו ולמטה אש וממתניו ולמעלה כמראה זהר כעין החשמלה׃ 2
Nditayangʼana ndinangoona chinthu chooneka ngati munthu. Kuchokera pamene pamaoneka ngati chiwuno chake kumatsika mʼmunsi anali ngati moto, ndipo kuchokera mʼchiwuno kukwera mmwamba amaoneka mowala ngati mkuwa wonyezimira.
וישלח תבנית יד ויקחני בציצת ראשי ותשא אתי רוח בין הארץ ובין השמים ותבא אתי ירושלמה במראות אלהים אל פתח שער הפנימית הפונה צפונה אשר שם מושב סמל הקנאה המקנה׃ 3
Iye anatambasula chinthu chooneka ngati dzanja ndipo anagwira tsitsi la pamutu panga. Nthawi yomweyo Mzimu unandikweza mlengalenga. Tsono ndikumachita ngati ndikuona Mulungu kutulo, Mzimu uja unapita nane ku Yerusalemu nundiyika pa khomo la chipata chamʼkati choyangʼana kumpoto. Kumeneko kunali fano limene limaputa mkwiyo wa Mulungu.
והנה שם כבוד אלהי ישראל כמראה אשר ראיתי בבקעה׃ 4
Kumeneko ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Israeli ngati momwe ndinaonera mʼmasomphenya mʼchigwa muja.
ויאמר אלי בן אדם שא נא עיניך דרך צפונה ואשא עיני דרך צפונה והנה מצפון לשער המזבח סמל הקנאה הזה בבאה׃ 5
Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tayangʼana kumpoto.” Choncho ndinayangʼana kumpoto ndipo ndinaona pa khomo la chipata pafupi ndi guwa lansembe ndinaona fano loputa mkwiyo wa Mulungu lija.
ויאמר אלי בן אדם הראה אתה מהם עשים תועבות גדלות אשר בית ישראל עשים פה לרחקה מעל מקדשי ועוד תשוב תראה תועבות גדלות׃ 6
Ndipo Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zimene akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene Aisraeli akuchita kuno, zinthu zondichotsa Ine kumalo anga opatulika? Koma iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri.”
ויבא אתי אל פתח החצר ואראה והנה חר אחד בקיר׃ 7
Kenaka Iye anandipititsa ku khomo lolowera ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Nditayangʼanitsitsa ndinangoona dzenje pa khomapo.
ויאמר אלי בן אדם חתר נא בקיר ואחתר בקיר והנה פתח אחד׃ 8
Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano bowola pa khomapo.” Ndinabowoladi pa khomapo ndipo ndinapezapo khomo.
ויאמר אלי בא וראה את התועבות הרעות אשר הם עשים פה׃ 9
Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Lowa, ndipo ona zinthu zonyansa zimene akuchita pamenepa.”
ואבוא ואראה והנה כל תבנית רמש ובהמה שקץ וכל גלולי בית ישראל מחקה על הקיר סביב סביב׃ 10
Motero Ine ndinalowa ndi kuyangʼana, ndipo ndinaona pa makoma onse zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwawa pansi, za nyama zonyansa ndiponso za mafano onse amene Aisraeli ankapembedza.
ושבעים איש מזקני בית ישראל ויאזניהו בן שפן עמד בתוכם עמדים לפניהם ואיש מקטרתו בידו ועתר ענן הקטרת עלה׃ 11
Patsogolo pa zimenezi panayima akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Aisraeli, ndipo Yaazaniya mwana wa Safani anali atayima pakati pawo. Aliyense wa iwo anali ndi chofukizira lubani mʼdzanja lake ndipo utsi wa fungo lokoma la lubani unkafuka.
ויאמר אלי הראית בן אדם אשר זקני בית ישראל עשים בחשך איש בחדרי משכיתו כי אמרים אין יהוה ראה אתנו עזב יהוה את הארץ׃ 12
Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Aisraeli akuchita mu mdima, aliyense akupembedza fano lakelake mʼnyumbamo? Iwo akuti, ‘Yehova sakutiona; Yehova walisiya dziko!’
ויאמר אלי עוד תשוב תראה תועבות גדלות אשר המה עשים׃ 13
Iye anandiwuzanso kuti, ‘Iwe udzawaonanso akuchita zinthu zonyansa kwambiri.’”
ויבא אתי אל פתח שער בית יהוה אשר אל הצפונה והנה שם הנשים ישבות מבכות את התמוז׃ 14
Kenaka anapita nane pa khomo la ku khomo la chipata cha Nyumba ya Mulungu choyangʼana kumpoto, ndipo kumeneko ndinaona akazi ena atakhala pansi, akulira mulungu wawo wotchedwa Tamuzi.
ויאמר אלי הראית בן אדם עוד תשוב תראה תועבות גדלות מאלה׃ 15
Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi? Iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri kuposa izi.”
ויבא אתי אל חצר בית יהוה הפנימית והנה פתח היכל יהוה בין האולם ובין המזבח כעשרים וחמשה איש אחריהם אל היכל יהוה ופניהם קדמה והמה משתחויתם קדמה לשמש׃ 16
Kenaka Iye anapita nane mʼkati mwa bwalo la Nyumba ya Yehova. Kumeneko ku khomo lolowera ku Nyumba ya Yehova pakati pa khonde ndi guwa lansembe, panali amuna 25. Anafulatira Nyumba ya Mulungu wa Yehova ndipo nkhope zawo zinaloza kummawa, ndipo ankapembedza dzuwa choyangʼana kummawa.
ויאמר אלי הראית בן אדם הנקל לבית יהודה מעשות את התועבות אשר עשו פה כי מלאו את הארץ חמס וישבו להכעיסני והנם שלחים את הזמורה אל אפם׃ 17
Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waziona zimenezi? Kodi nʼchinthu chopepuka kuti anthu a ku Yuda azichita zonyansa zimene akuchitazi pano? Kodi afike mpaka pomafalitsa za ndewu mʼdziko lonse? Iwotu akuwutsa ukali wanga. Akundipsetsa mtima ndi zochita zawo!
וגם אני אעשה בחמה לא תחוס עיני ולא אחמל וקראו באזני קול גדול ולא אשמע אותם׃ 18
Choncho Ine ndidzawalanga ndili wokwiya. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka. Ngakhale atandifuwulira mʼmakutu mwanga sindidzawamvera.”

< יחזקאל 8 >