< יחזקאל 36 >
ואתה בן אדם הנבא אל הרי ישראל ואמרת הרי ישראל שמעו דבר יהוה׃ | 1 |
“Iwe mwana wa munthu, yankhula kwa mapiri a Israeli ndipo unene kuti, ‘Inu mapiri a Israeli, imvani mawu a Yehova.’
כה אמר אדני יהוה יען אמר האויב עליכם האח ובמות עולם למורשה היתה לנו׃ | 2 |
Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mdani wanu ankanena kuti, ‘Aa! Dziko lamapiri lakalekale lija lasanduka lathu.’
לכן הנבא ואמרת כה אמר אדני יהוה יען ביען שמות ושאף אתכם מסביב להיותכם מורשה לשארית הגוים ותעלו על שפת לשון ודבת עם׃ | 3 |
Choncho nenera ndipo uwawuze kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anakusakazani ndi kukuponderezani ku mbali zonse motero kuti munakhala mʼmanja mwa anthu a mitundu ina yonse ndipo anthu ankakunenani ndi kukunyozani,
לכן הרי ישראל שמעו דבר אדני יהוה כה אמר אדני יהוה להרים ולגבעות לאפיקים ולגאיות ולחרבות השממות ולערים הנעזבות אשר היו לבז וללעג לשארית הגוים אשר מסביב׃ | 4 |
choncho, inu mapiri a Israeli, imvani zimene Ine Ambuye Yehova ndikuwuza mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mabwinja ndi mizinda yosiyidwa imene yakhala ikufunkhidwa komanso kunyozedwa ndi anthu a mitundu ina okuzungulirani.
לכן כה אמר אדני יהוה אם לא באש קנאתי דברתי על שארית הגוים ועל אדום כלא אשר נתנו את ארצי להם למורשה בשמחת כל לבב בשאט נפש למען מגרשה לבז׃ | 5 |
Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mu mkwiyo wanga woopsa ndinayankhula kuyimba mlandu mitundu ina yonse ya anthu makamaka a ku Edomu. Iwowa mwa chimwemwe chodzaza tsaya ndi mwa nkhwidzi analanda dziko langa ndi kulisandutsa lawo ndi kutengeratu dziko la msipu kukhala lawo.’
לכן הנבא על אדמת ישראל ואמרת להרים ולגבעות לאפיקים ולגאיות כה אמר אדני יהוה הנני בקנאתי ובחמתי דברתי יען כלמת גוים נשאתם׃ | 6 |
Nʼchifukwa chake, lengeza ku dziko la Israeli, ndipo uwuze mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikuyankhula ndi mtima wokwiya kwambiri chifukwa inu munalandira chitonzo cha anthu a mitundu ina.’
לכן כה אמר אדני יהוה אני נשאתי את ידי אם לא הגוים אשר לכם מסביב המה כלמתם ישאו׃ | 7 |
Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikulumbira nditakweza dzanja langa kuti mitundu ya anthu idzatozedwanso.
ואתם הרי ישראל ענפכם תתנו ופריכם תשאו לעמי ישראל כי קרבו לבוא׃ | 8 |
“Koma Inu mapiri a Israeli mudzaphukanso nthambi ndipo mudzawabalira zipatso anthu anga a Israeli, pakuti ali pafupi kubwerera kwawo.
כי הנני אליכם ופניתי אליכם ונעבדתם ונזרעתם׃ | 9 |
Taonani, Ine ndili mbali yanu ndipo ndidzakukomerani mtima. Mudzalimidwa ndi kudzalidwa.
והרביתי עליכם אדם כל בית ישראל כלה ונשבו הערים והחרבות תבנינה׃ | 10 |
Ndidzachulukitsa chiwerengero cha anthu anu, nyumba yonse ya Israeli. Mʼmizinda mudzakhalanso anthu ndipo mabwinja adzamangidwanso.
והרביתי עליכם אדם ובהמה ורבו ופרו והושבתי אתכם כקדמותיכם והיטבתי מראשתיכם וידעתם כי אני יהוה׃ | 11 |
Ndidzachulukitsa chiwerengero cha amuna pamodzi ndi ziweto zomwe, ndipo adzachuluka kwambiri ndi kubereka ana ambiri. Ndidzakhazika anthu mʼdzikomo monga analili kale, ndi kukulemeretsani kuposa kale. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
והולכתי עליכם אדם את עמי ישראל וירשוך והיית להם לנחלה ולא תוסף עוד לשכלם׃ | 12 |
Ndidzachititsa anthu kuyenda pa inu, ndiye kuti inu anthu anga Aisraeli. Iwowo adzakhazikika pa inu, ndipo inu mudzakhala cholowa chawo. Simudzalandanso ana awo.
כה אמר אדני יהוה יען אמרים לכם אכלת אדם אתי ומשכלת גויך היית׃ | 13 |
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anthu amanena kuti, ndiwe dziko limene limadya anthu ake ‘kulanda ana a mtundu wake,’
לכן אדם לא תאכלי עוד וגויך לא תכשלי עוד נאם אדני יהוה׃ | 14 |
nʼchifukwa chake, simudzadyanso anthu kapena kulanda ana a mtundu wako. Ine Ambuye Yehova ndikutero.
ולא אשמיע אליך עוד כלמת הגוים וחרפת עמים לא תשאי עוד וגויך לא תכשלי עוד נאם אדני יהוה׃ | 15 |
Sindidzakulolaninso kumva mnyozo wa anthu a mitundu ina, kapena kupirira kunyogodola kwawo kapenanso kupunthwitsanso anthu a mʼdziko lako. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
ויהי דבר יהוה אלי לאמר׃ | 16 |
Yehova anandiyankhulanso kuti:
בן אדם בית ישראל ישבים על אדמתם ויטמאו אותה בדרכם ובעלילותם כטמאת הנדה היתה דרכם לפני׃ | 17 |
“Iwe mwana wa munthu, pamene anthu a Israeli ankakhala mʼdziko lawolawo, analiyipitsa ndi makhalidwe awo ndiponso zochita zawo. Machitidwe awo pamaso panga anali onyansa pa zachipembedzo ngati msambo wa mkazi amene ali pa nthawi yake.
ואשפך חמתי עליהם על הדם אשר שפכו על הארץ ובגלוליהם טמאוה׃ | 18 |
Tsono ndinawalanga chifukwa cha magazi amene anakhetsa mʼdzikomo, ndiponso chifukwa anayipitsa dziko ndi mafano awo.
ואפיץ אתם בגוים ויזרו בארצות כדרכם וכעלילותם שפטתים׃ | 19 |
Ndinawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anabalalikira mʼmayiko onse. Ndinawalanga molingana ndi makhalidwe awo ndi zochita zawo.
ויבוא אל הגוים אשר באו שם ויחללו את שם קדשי באמר להם עם יהוה אלה ומארצו יצאו׃ | 20 |
Atafika kwa anthu a mitundu ina, kulikonse kumene anapitako, anayipitsa dzina langa loyera. Zinatero popeza anthu ponena za iwo ankanena kuti, ‘Awa ndi anthu a Yehova, komatu anachotsedwa ku dziko lake.’
ואחמל על שם קדשי אשר חללוהו בית ישראל בגוים אשר באו שמה׃ | 21 |
Koma Ine ndinkadera nkhawa dzina langa loyera, limene Aisraeli analiyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapitako.
לכן אמר לבית ישראל כה אמר אדני יהוה לא למענכם אני עשה בית ישראל כי אם לשם קדשי אשר חללתם בגוים אשר באתם שם׃ | 22 |
“Nʼchifukwa chake awuze Aisraeliwo kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndidzachita zimene ndidzachitezo osati chifukwa cha inuyo Aisraelinu ayi, koma chifukwa cha dzina langa, limene mwaliyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapitako.
וקדשתי את שמי הגדול המחלל בגוים אשר חללתם בתוכם וידעו הגוים כי אני יהוה נאם אדני יהוה בהקדשי בכם לעיניהם׃ | 23 |
Ndidzaonetsa chiyero cha dzina langa lotchuka, limene layipitsidwa pakati pawo. Anthu a mitundu inayo atadzazindikira kuti ndaonetsa kudzera mwa inu kuti dzina langa ndi loyera, iwo adzadziwanso kuti Ine ndine Yehova. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
ולקחתי אתכם מן הגוים וקבצתי אתכם מכל הארצות והבאתי אתכם אל אדמתכם׃ | 24 |
“Pakuti Ine ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzakusonkhanitsani kuchoka ku mayiko onse ndi kukubwezerani ku dziko lanulanu.
וזרקתי עליכם מים טהורים וטהרתם מכל טמאותיכם ומכל גלוליכם אטהר אתכם׃ | 25 |
Ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera mtima. Zonse zimene zimakuyipitsani zidzachoka. Ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse.
ונתתי לכם לב חדש ורוח חדשה אתן בקרבכם והסרתי את לב האבן מבשרכם ונתתי לכם לב בשר׃ | 26 |
Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzachotsa mwa inu mtima wanu wowuma ngati mwala ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu.
ואת רוחי אתן בקרבכם ועשיתי את אשר בחקי תלכו ומשפטי תשמרו ועשיתם׃ | 27 |
Ndipo ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzakuthandizani kutsatira malangizo anga ndi kukusungitsani mosamala kwambiri malamulo anga.
וישבתם בארץ אשר נתתי לאבתיכם והייתם לי לעם ואנכי אהיה לכם לאלהים׃ | 28 |
Mudzakhala mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu. Mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.
והושעתי אתכם מכל טמאותיכם וקראתי אל הדגן והרביתי אתו ולא אתן עליכם רעב׃ | 29 |
Ndidzakupulumutsani ku zonse zokuyipitsani. Ndidzakuchulukitsirani tirigu ndipo sindidzakugwetseraninso njala.
והרביתי את פרי העץ ותנובת השדה למען אשר לא תקחו עוד חרפת רעב בגוים׃ | 30 |
Ndidzachulukitsa zipatso za mʼmitengo yanu ndi zokolola za mʼmunda mwanu, kotero kuti simudzanyozedwanso pakati pa anthu a mitundu ina chifukwa cha njala.
וזכרתם את דרכיכם הרעים ומעלליכם אשר לא טובים ונקטתם בפניכם על עונתיכם ועל תועבתיכם׃ | 31 |
Pamenepo mudzakumbukira makhalidwe anu oyipa ndi ntchito zanu zoyipa. Machimo anu ndi ntchito zanu zonyansa zidzakuchititsa nokha manyazi.
לא למענכם אני עשה נאם אדני יהוה יודע לכם בושו והכלמו מדרכיכם בית ישראל׃ | 32 |
Tsono dziwani kuti Ine sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo ayi, ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. Ndiyetu chitani manyazi ndipo mugwetse nkhope zanu, inu Aisraeli chifukwa cha makhalidwe anu!
כה אמר אדני יהוה ביום טהרי אתכם מכל עונותיכם והושבתי את הערים ונבנו החרבות׃ | 33 |
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limene ndidzayeretse machimo anu onse, ndidzayikamonso anthu mʼmizinda yanu, ndipo ndidzamanganso nyumba pa mabwinja.
והארץ הנשמה תעבד תחת אשר היתה שממה לעיני כל עובר׃ | 34 |
Dziko limene linasanduka chipululu lizidzalimidwanso. Mʼmalo moti aliyense wopitamo alione dzikolo ngati chipululu tsopano adzaliona lolimidwa.
ואמרו הארץ הלזו הנשמה היתה כגן עדן והערים החרבות והנשמות והנהרסות בצורות ישבו׃ | 35 |
Iwo adzati, ‘Dziko ili, limene linali chipululu, lasanduka munda wa Edeni. Mizinda imene inali mabwinja osiyidwa ndi owonongedwa, tsopano ndi yotetezedwa ndi yokhalamo anthu.
וידעו הגוים אשר ישארו סביבותיכם כי אני יהוה בניתי הנהרסות נטעתי הנשמה אני יהוה דברתי ועשיתי׃ | 36 |
Ndipo anthu a mitundu ina okhala pafupi nanu amene anatsala adzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndinamanganso mizinda yowonongeka ndi kudzalanso zinthu zatsopano mʼmalo mʼmene munali chipululu. Ine Yehova ndayankhula ndipo ndidzazichitadi.’
כה אמר אדני יהוה עוד זאת אדרש לבית ישראל לעשות להם ארבה אתם כצאן אדם׃ | 37 |
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzalolanso Aisraeli kuti andipemphe zoti ndiwachitire: Ndidzachulukitsa anthu awo ngati nkhosa.
כצאן קדשים כצאן ירושלם במועדיה כן תהיינה הערים החרבות מלאות צאן אדם וידעו כי אני יהוה׃ | 38 |
Adzachulukadi ngati nkhosa zomwe ankapereka ngati nsembe ku Yerusalemu pa nthawi za chikondwerero. Choncho mizinda ya mabwinja idzadzaza ndi anthu. Zikadzatero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”