< יחזקאל 25 >
ויהי דבר יהוה אלי לאמר׃ | 1 |
Yehova anandiyankhula kuti:
בן אדם שים פניך אל בני עמון והנבא עליהם׃ | 2 |
“Iwe mwana wa munthu, tembenukira anthu a ku Amoni ndipo unenere mowadzudzula.
ואמרת לבני עמון שמעו דבר אדני יהוה כה אמר אדני יהוה יען אמרך האח אל מקדשי כי נחל ואל אדמת ישראל כי נשמה ואל בית יהודה כי הלכו בגולה׃ | 3 |
Awawuze kuti, ‘Inu anthu a ku Amoni, imvani zimene Ambuye Yehova akunena. Iye akuti: Inu munanena mawu onyoza pamene Nyumba yanga yopatulika inkayipitsidwa. Munanyozanso dziko la Israeli pamene linaguga ndiponso anthu a ku Yuda pamene anatengedwa ukapolo.
לכן הנני נתנך לבני קדם למורשה וישבו טירותיהם בך ונתנו בך משכניהם המה יאכלו פריך והמה ישתו חלבך׃ | 4 |
Nʼchifukwa chake Ine ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu akummawa ngati cholowa chawo. Iwo adzamanga misasa yawo ndi kukhoma matenti awo pakati panu. Adzadya zipatso zanu ndi kumwa mkaka wanu.
ונתתי את רבה לנוה גמלים ואת בני עמון למרבץ צאן וידעתם כי אני יהוה׃ | 5 |
Ndidzasandutsa Raba kuti akhale busa la ngamira ndi mizinda ya Aamoni kuti ikhale makola a nkhosa. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
כי כה אמר אדני יהוה יען מחאך יד ורקעך ברגל ותשמח בכל שאטך בנפש אל אדמת ישראל׃ | 6 |
Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu munawomba mʼmanja ndi kumalumphalumpha. Munkakondwa mu mtima mwanu pamene munkanyoza dziko la Israeli.
לכן הנני נטיתי את ידי עליך ונתתיך לבג לגוים והכרתיך מן העמים והאבדתיך מן הארצות אשמידך וידעת כי אני יהוה׃ | 7 |
Nʼchifukwa chake ndidzatambasula dzanja langa kuti ndikulangeni, ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha anthu a mitundu ina. Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukufafanizani mʼmayiko onse. Ndidzakuwonongani, ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova!’”
כה אמר אדני יהוה יען אמר מואב ושעיר הנה ככל הגוים בית יהודה׃ | 8 |
“Ambuye Yehova akuti, ‘Anthu a ku Mowabu ndi a ku Seiri ananena kuti anthu a ku Yuda ali ngati mayiko ena onse.’
לכן הנני פתח את כתף מואב מהערים מעריו מקצהו צבי ארץ בית הישימת בעל מעון וקריתמה׃ | 9 |
Nʼchifukwa chake ndidzagumula mbali ina ya Mowabu, kuyambira ku mizinda yake ya kumalire; mizinda yokongola ya Beti-Yesimoti, Baala-Meoni ndi Kiriataimu.
לבני קדם על בני עמון ונתתיה למורשה למען לא תזכר בני עמון בגוים׃ | 10 |
Ndidzapereka Amowabu pamodzi ndi Aamoni mʼmanja mwa anthu akummawa kotero kuti Aamoni adzayiwalikiratu pakati pa anthu a mitundu ina.
ובמואב אעשה שפטים וידעו כי אני יהוה׃ | 11 |
Ndidzawalangadi Amowabuwo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
כה אמר אדני יהוה יען עשות אדום בנקם נקם לבית יהודה ויאשמו אשום ונקמו בהם׃ | 12 |
“Ambuye Yehova akuti, ‘Pakuti Edomu analipsira Ayuda, ndiye kuti analakwa kwambiri pochita zimenezi.
לכן כה אמר אדני יהוה ונטתי ידי על אדום והכרתי ממנה אדם ובהמה ונתתיה חרבה מתימן ודדנה בחרב יפלו׃ | 13 |
Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzatambasula dzanja langa kulanga Edomu ndi kupha anthu ake ndiponso nyama zawo. Ndidzawonongeratu Edomu ndipo adzaphedwa ndi lupanga kuchokera ku Temani mpaka ku Dedani.
ונתתי את נקמתי באדום ביד עמי ישראל ועשו באדום כאפי וכחמתי וידעו את נקמתי נאם אדני יהוה׃ | 14 |
Ndidzalanga Edomu ndi dzanja la anthu anga Aisraeli. Adzalanga anthu a ku Edomu molingana ndi mkwiyo ndi ukali wanga. Choncho adzaona kulipsira kwanga akutero Ambuye Yehova.’”
כה אמר אדני יהוה יען עשות פלשתים בנקמה וינקמו נקם בשאט בנפש למשחית איבת עולם׃ | 15 |
“Ambuye Yehova akuti, ‘Afilisti analanga anthu anga mwankhanza ndi kuwalipsira.
לכן כה אמר אדני יהוה הנני נוטה ידי על פלשתים והכרתי את כרתים והאבדתי את שארית חוף הים׃ | 16 |
Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzatambasula dzanja langa kukantha Afilistiwo. Ndidzafafaniza Akereti ndi kuwononga iwo amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.
ועשיתי בם נקמות גדלות בתוכחות חמה וידעו כי אני יהוה בתתי את נקמתי בם׃ | 17 |
Ndidzawabwezera chilango choopsa ndipo ndidzawalanga mu mkwiyo wanga. Ndikadzawalipsira ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’”