< קֹהֶלֶת 2 >

אמרתי אני בלבי לכה נא אנסכה בשמחה וראה בטוב והנה גם הוא הבל׃ 1
Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Tsopano ndiyese zosangalatsa kuti ndipeze zomwe ndi zabwino.” Koma izi zinaonekanso kuti ndi zopandapake.
לשחוק אמרתי מהולל ולשמחה מה זה עשה׃ 2
“Kuseka,” ndinati, “imeneyo ndi misala. Ndipo kodi chisangalalo chimabweretsa phindu lanji?”
תרתי בלבי למשוך ביין את בשרי ולבי נהג בחכמה ולאחז בסכלות עד אשר אראה אי זה טוב לבני האדם אשר יעשו תחת השמים מספר ימי חייהם׃ 3
Ndinayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewu unali uchitsiru, pamenepo nʼkuti maganizo anga akutsogozedwa ndi nzeru. Ine ndinkati mwina kapena njira yotero nʼkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku owerengeka a moyo wawo.
הגדלתי מעשי בניתי לי בתים נטעתי לי כרמים׃ 4
Ndinagwira ntchito zikuluzikulu: Ndinadzimangira nyumba ndi kuwoka mipesa.
עשיתי לי גנות ופרדסים ונטעתי בהם עץ כל פרי׃ 5
Ndinalima madimba ndi minda yamitengo; ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso za mitundu yonse.
עשיתי לי ברכות מים להשקות מהם יער צומח עצים׃ 6
Ndinakumba mayiwe osungiramo madzi woti ndizithirira minda ya mitengo yodzalidwa ija.
קניתי עבדים ושפחות ובני בית היה לי גם מקנה בקר וצאן הרבה היה לי מכל שהיו לפני בירושלם׃ 7
Ndinagula akapolo aamuna ndi akapolo aakazi, ndiponso ndinali ndi akapolo ena omwe anabadwira mʼnyumba mwanga. Ndinalinso ndi ngʼombe ndi nkhosa zambiri kupambana aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe.
כנסתי לי גם כסף וזהב וסגלת מלכים והמדינות עשיתי לי שרים ושרות ותענוגת בני האדם שדה ושדות׃ 8
Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu.
וגדלתי והוספתי מכל שהיה לפני בירושלם אף חכמתי עמדה לי׃ 9
Ndinali munthu wotchuka kupambana wina aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Mu zonsezi nzeru zanga zinali nane.
וכל אשר שאלו עיני לא אצלתי מהם לא מנעתי את לבי מכל שמחה כי לבי שמח מכל עמלי וזה היה חלקי מכל עמלי׃ 10
Sindinadzimane chilichonse chimene maso anga anachifuna; mtima wanga sindinawumane zokondweretsa. Mtima wanga unakondwera ndi ntchito yanga yonse, ndipo iyi ndiyo inali mphotho ya ntchito zanga zonse zolemetsa.
ופניתי אני בכל מעשי שעשו ידי ובעמל שעמלתי לעשות והנה הכל הבל ורעות רוח ואין יתרון תחת השמש׃ 11
Koma pamene ndinayamba kuyangʼanayangʼana zonse zimene ndinachita ndi manja anga, ndi zimene ndinazivutikira kuti ndizipeze, zonsezi zinali zopandapake; kungodzivuta chabe, palibe chomwe ndinapindula pansi pano.
ופניתי אני לראות חכמה והוללות וסכלות כי מה האדם שיבוא אחרי המלך את אשר כבר עשוהו׃ 12
Kenaka maganizo anga anayamba kulingalira zakuti nzeru nʼchiyani, komanso kuti misala ndi uchitsiru nʼchiyani. Kodi munthu wodzalowa ufumu tsopanoyo angachite chiyani choposa chimene chinachitidwa kale?
וראיתי אני שיש יתרון לחכמה מן הסכלות כיתרון האור מן החשך׃ 13
Ndinaona kuti nzeru ndi yopambana uchitsiru, monga momwe kuwala kumapambanira mdima.
החכם עיניו בראשו והכסיל בחשך הולך וידעתי גם אני שמקרה אחד יקרה את כלם׃ 14
Munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo, pamene chitsiru chimayenda mʼchimbulimbuli; koma ndinazindikira kuti chomwe chimawachitikira onsewo ndi chimodzi.
ואמרתי אני בלבי כמקרה הכסיל גם אני יקרני ולמה חכמתי אני אז יותר ודברתי בלבי שגם זה הבל׃ 15
Pamenepo ndinalingalira mu mtima mwanga, “Zochitikira chitsiru zidzandichitikiranso ine. Nanga tsono phindu langa nʼchiyani pakukhala wanzeru?” Ndinati mu mtima mwanga, “Ichinso ndi chopandapake.”
כי אין זכרון לחכם עם הכסיל לעולם בשכבר הימים הבאים הכל נשכח ואיך ימות החכם עם הכסיל׃ 16
Pakuti munthu wanzeru, pamodzinso ndi chitsiru sadzakumbukiridwa nthawi yayitali; mʼmasiku amʼtsogolo awiriwo adzayiwalika. Mmene chimafera chitsiru ndi mmenenso amafera wanzeru!
ושנאתי את החיים כי רע עלי המעשה שנעשה תחת השמש כי הכל הבל ורעות רוח׃ 17
Kotero ndinadana nawo moyo chifukwa ntchito zimene zimagwiridwa pansi pano ndi zosautsa kwa ine. Ntchito zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
ושנאתי אני את כל עמלי שאני עמל תחת השמש שאניחנו לאדם שיהיה אחרי׃ 18
Ine ndinadana nazo ntchito zonse zimene ndinazigwira pansi pano, chifukwa ndinayenera kudzazisiyira wina amene adzalowa mʼmalo mwanga.
ומי יודע החכם יהיה או סכל וישלט בכל עמלי שעמלתי ושחכמתי תחת השמש גם זה הבל׃ 19
Ndipo ndani amadziwa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala wolamulira zonse zimene ndinazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Izinso ndi zopandapake.
וסבותי אני ליאש את לבי על כל העמל שעמלתי תחת השמש׃ 20
Motero ndinayamba kutaya mtima chifukwa cha ntchito zonse zimene ndinazivutikira pansi pano.
כי יש אדם שעמלו בחכמה ובדעת ובכשרון ולאדם שלא עמל בו יתננו חלקו גם זה הבל ורעה רבה׃ 21
Pakuti munthu atha kugwira ntchito yake mwanzeru, chidziwitso ndi luntha, ndipo kenaka nʼkusiyira wina amene sanakhetserepo thukuta. Izinso ndi zopandapake ndiponso tsoka lalikulu.
כי מה הוה לאדם בכל עמלו וברעיון לבו שהוא עמל תחת השמש׃ 22
Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa zimene amazichita pansi pano?
כי כל ימיו מכאבים וכעס ענינו גם בלילה לא שכב לבו גם זה הבל הוא׃ 23
Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta; ngakhale usiku womwe, mtima wake supumula. Izinso ndi zopandapake.
אין טוב באדם שיאכל ושתה והראה את נפשו טוב בעמלו גם זה ראיתי אני כי מיד האלהים היא׃ 24
Kwa munthu palibe chabwino china kuposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Izinso ndaona kuti ndi zochokera kwa Mulungu,
כי מי יאכל ומי יחוש חוץ ממני׃ 25
pakuti popanda Iye, ndani angadye ndi kupeza chisangalalo?
כי לאדם שטוב לפניו נתן חכמה ודעת ושמחה ולחוטא נתן ענין לאסוף ולכנוס לתת לטוב לפני האלהים גם זה הבל ורעות רוח׃ 26
Munthu amene amakondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamusandutsa wanzeru, wozindikira ndi wachisangalalo, koma wochimwa, Mulungu amamupatsa ntchito yosonkhanitsa ndi kusunga chuma kuti adzachipereke kwa amene Mulunguyo amakondwera naye. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.

< קֹהֶלֶת 2 >