< דברים 33 >

וזאת הברכה אשר ברך משה איש האלהים את בני ישראל לפני מותו׃ 1
Awa ndi madalitso amene Mose, munthu wa Mulungu, anawapereka kwa Aisraeli asanafe.
ויאמר יהוה מסיני בא וזרח משעיר למו הופיע מהר פארן ואתה מרבבת קדש מימינו אש דת למו׃ 2
Iye anati: “Yehova anabwera kuchokera ku Sinai ndipo anatulukira kuchokera ku Seiri; anawala kuchokera pa Phiri la Parani. Iye anabwera ndi chiwunyinji cha angelo kuchokera kummwera, moto woyaka uli mʼdzanja mwake.
אף חבב עמים כל קדשיו בידך והם תכו לרגלך ישא מדברתיך׃ 3
Ndithu ndinu amene mumakonda anthu anu; opatulika ake onse ali mʼmanja mwake. Onse amagwada pansi pa mapazi anu kuchokera kwa inu amalandira malangizo,
תורה צוה לנו משה מורשה קהלת יעקב׃ 4
malamulo amene Mose anatipatsa, chuma chopambana cha mtundu wa Yakobo.
ויהי בישרון מלך בהתאסף ראשי עם יחד שבטי ישראל׃ 5
Iye anali mfumu ya Yesuruni pamene atsogoleri a anthu anasonkhana, pamodzi ndi mafuko a Israeli.
יחי ראובן ואל ימת ויהי מתיו מספר׃ 6
“Lolani Rubeni akhale ndi moyo ndipo asafe, anthu ake asachepe pa chiwerengero.”
וזאת ליהודה ויאמר שמע יהוה קול יהודה ואל עמו תביאנו ידיו רב לו ועזר מצריו תהיה׃ 7
Ndipo ponena za Yuda anati: “Inu Yehova, imvani kulira kwa Yuda; mubweretseni kwa anthu ake. Ndi manja ake omwe adziteteze yekha. Inu khalani thandizo lake polimbana ndi adani ake!”
וללוי אמר תמיך ואוריך לאיש חסידך אשר נסיתו במסה תריבהו על מי מריבה׃ 8
Za fuko la Alevi anati: “Tumimu wanu ndi Urimu ndi za mtumiki wanu wokhulupirika. Munamuyesa ku Masa; munalimbana naye ku madzi a ku Meriba.
האמר לאביו ולאמו לא ראיתיו ואת אחיו לא הכיר ואת בנו לא ידע כי שמרו אמרתך ובריתך ינצרו׃ 9
Iye ananena za abambo ake ndi amayi ake kuti, ‘Sindilabadira za iwo.’ Sanasamale za abale ake kapena ana ake, koma anayangʼanira mawu anu ndipo anateteza pangano lanu.
יורו משפטיך ליעקב ותורתך לישראל ישימו קטורה באפך וכליל על מזבחך׃ 10
Iye amaphunzitsa Yakobo malangizo anu ndi malamulo anu kwa Israeli. Amafukiza lubani pamaso panu ndiponso amapereka nsembe zanu zonse zopsereza pa guwa lanu.
ברך יהוה חילו ופעל ידיו תרצה מחץ מתנים קמיו ומשנאיו מן יקומון׃ 11
Inu Yehova, dalitsani luso lake lonse ndipo mukondwere ndi ntchito za manja ake. Menyani adani awo mʼchiwuno kanthani amene amuwukira kuti asadzukenso.”
לבנימן אמר ידיד יהוה ישכן לבטח עליו חפף עליו כל היום ובין כתיפיו שכן׃ 12
Za fuko la Benjamini anati: “Wokondedwa wa Yehova akhale mwamtendere mwa Iye, pakuti amamuteteza tsiku lonse, ndipo amene Yehova amamukonda amawusa pa mapewa ake.”
וליוסף אמר מברכת יהוה ארצו ממגד שמים מטל ומתהום רבצת תחת׃ 13
Za fuko la Yosefe anati: “Yehova adalitse dziko lake ndi mame ambiri ochokera kumwamba ndiponso madzi ambiri ochokera pansi pa nthaka;
וממגד תבואת שמש וממגד גרש ירחים׃ 14
ndi zinthu zambiri zimene zimacha ndi dzuwa ndiponso ndi zokolola zabwino kwambiri zimene zimacha ndi mwezi uliwonse;
ומראש הררי קדם וממגד גבעות עולם׃ 15
ndi zipatso zabwino kwambiri zochokera mʼmapiri amakedzanawa ndiponso zokolola zochuluka zochokera ku zitunda zakalekale;
וממגד ארץ ומלאה ורצון שכני סנה תבואתה לראש יוסף ולקדקד נזיר אחיו׃ 16
ndi mphatso zabwino kwambiri zochokera pa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndiponso kukoma mtima kwa Iye amene amakhala mʼchitsamba choyaka moto. Madalitso onsewa akhale pa mutu pa Yosefe, wapaderadera pakati pa abale ake.
בכור שורו הדר לו וקרני ראם קרניו בהם עמים ינגח יחדו אפסי ארץ והם רבבות אפרים והם אלפי מנשה׃ 17
Ulemerero wake uli ngati ngʼombe yayimuna yoyamba kubadwa; nyanga zake zili ngati za njati. Ndi nyanga zakezo adzapirikitsa anthu a mitundu ina, ngakhale iwo amene akukhala ku malekezero a dziko lapansi. Nyanga zimenezi ndiye anthu miyandamiyanda a Efereimu; nyanga zimenezi ndiye anthu 1,000 a Manase.”
ולזבולן אמר שמח זבולן בצאתך ויששכר באהליך׃ 18
Za fuko la Zebuloni anati: “Kondwera Zebuloni, pamene ukutuluka, ndipo iwe, Isakara, kondwera mʼmatenti ako.
עמים הר יקראו שם יזבחו זבחי צדק כי שפע ימים יינקו ושפוני טמוני חול׃ 19
Adzayitanira mitundu ya anthu kumapiri, kumeneko adzaperekako nsembe zachilungamo; kumeneko adzadyerera zinthu zochuluka zochokera ku nyanja, chuma chobisika mu mchenga.”
ולגד אמר ברוך מרחיב גד כלביא שכן וטרף זרוע אף קדקד׃ 20
Za fuko la Gadi anati: “Wodala amene amakulitsa malire a Gadi! Gadi amakhala kumeneko ngati mkango, kukhadzula mkono kapena mutu.
וירא ראשית לו כי שם חלקת מחקק ספון ויתא ראשי עם צדקת יהוה עשה ומשפטיו עם ישראל׃ 21
Iye anadzisankhira dziko labwino kwambiri; gawo la mtsogoleri anasungira iye. Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana, anachita chifuniro cha Yehova molungama, ndiponso malamulo onena za Israeli.”
ולדן אמר דן גור אריה יזנק מן הבשן׃ 22
Za fuko la Dani anati: “Dani ndi mwana wamkango, amene akutuluka ku Basani.”
ולנפתלי אמר נפתלי שבע רצון ומלא ברכת יהוה ים ודרום ירשה׃ 23
Za fuko la Nafutali anati: “Nafutali wadzaza ndi kukoma mtima kwa Yehova ndipo ndi wodzaza ndi madalitso ake; cholowa chake chidzakhala mbali ya kummwera kwa nyanja.”
ולאשר אמר ברוך מבנים אשר יהי רצוי אחיו וטבל בשמן רגלו׃ 24
Za fuko la Aseri anati: “Mwana wodalitsika kwambiri ndi Aseri; abale ake amukomere mtima, ndipo asambe mapazi ake mʼmafuta.
ברזל ונחשת מנעליך וכימיך דבאך׃ 25
Zotsekera za zipata zako zidzakhala za chitsulo ndi za mkuwa, ndi mphamvu zako zidzakhala ngati masiku a moyo wako.
אין כאל ישרון רכב שמים בעזרך ובגאותו שחקים׃ 26
“Palibe wina wofanana ndi Mulungu wa Yesuruni, amene amakwera pa thambo kukuthandizani ndiponso pa mitambo ya ulemerero wake.
מענה אלהי קדם ומתחת זרעת עולם ויגרש מפניך אויב ויאמר השמד׃ 27
Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu, ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu, adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’
וישכן ישראל בטח בדד עין יעקב אל ארץ דגן ותירוש אף שמיו יערפו טל׃ 28
Motero Israeli adzakhala yekha mwamtendere; zidzukulu za Yakobo zili pa mtendere mʼdziko la tirigu ndi vinyo watsopano, kumene thambo limagwetsa mame.
אשריך ישראל מי כמוך עם נושע ביהוה מגן עזרך ואשר חרב גאותך ויכחשו איביך לך ואתה על במותימו תדרך׃ 29
Iwe Israeli, ndiwe wodala! Wofanana nanu ndani anthu opulumutsidwa ndi Yehova? Iye ndiye chishango ndi mthandizi wanu ndi lupanga lanu la ulemerero. Adani ako adzakugonjera, ndipo iwe udzapondereza pansi malo awo achipembedzo.”

< דברים 33 >