< דברים 11 >
ואהבת את יהוה אלהיך ושמרת משמרתו וחקתיו ומשפטיו ומצותיו כל הימים׃ | 1 |
Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndipo nthawi zonse muzitsata zimene Iyeyo anakulamulani, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo ake.
וידעתם היום כי לא את בניכם אשר לא ידעו ואשר לא ראו את מוסר יהוה אלהיכם את גדלו את ידו החזקה וזרעו הנטויה׃ | 2 |
Lero kumbukirani kuti si ana anu amene anaona ndi kulawa chilango cha Yehova Mulungu wanu: ukulu wake, dzanja lake lamphamvu, mkono wake wotambasuka;
ואת אתתיו ואת מעשיו אשר עשה בתוך מצרים לפרעה מלך מצרים ולכל ארצו׃ | 3 |
zizindikiro zozizwitsa zimene anazionetsa ndi zinthu zimene anazichita mʼkati mwa Igupto, Farao mfumu ya Igupto ndi kwa dziko lake lonse;
ואשר עשה לחיל מצרים לסוסיו ולרכבו אשר הציף את מי ים סוף על פניהם ברדפם אחריכם ויאבדם יהוה עד היום הזה׃ | 4 |
zimene Iye anachita kwa gulu lankhondo la Aigupto, kwa akavalo ndi magaleta awo, mmene Iye anawamizira ndi madzi a mu Nyanja Yofiira pamene amakuthamangitsani, ndi mmene Yehova anawagonjetsera kufikira lero.
ואשר עשה לכם במדבר עד באכם עד המקום הזה׃ | 5 |
Si ana anu amene anaona zimene Iye anakuchitirani mʼchipululu kufikira pamene munafika pa malo anu,
ואשר עשה לדתן ולאבירם בני אליאב בן ראובן אשר פצתה הארץ את פיה ותבלעם ואת בתיהם ואת אהליהם ואת כל היקום אשר ברגליהם בקרב כל ישראל׃ | 6 |
ndi zimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu mwana wa Rubeni, pamene nthaka inatsekula pakamwa pake pakati pa Aisraeli onse ndi kuwameza pamodzi ndi katundu wawo, matenti awo ndi chilichonse chawo.
כי עיניכם הראת את כל מעשה יהוה הגדל אשר עשה׃ | 7 |
Koma ndinuyo amene munaona ntchito zonse zikuluzikulu zimenezi Yehova anakuchitirani.
ושמרתם את כל המצוה אשר אנכי מצוך היום למען תחזקו ובאתם וירשתם את הארץ אשר אתם עברים שמה לרשתה׃ | 8 |
Tsono muzisunga malamulo onse amene ndikukupatsani lero kuti mukhale ndi mphamvu ndi kuti mupite kukalanda mʼdziko limene mwakhala pangʼono kulowamo mukawoloka Yorodani,
ולמען תאריכו ימים על האדמה אשר נשבע יהוה לאבתיכם לתת להם ולזרעם ארץ זבת חלב ודבש׃ | 9 |
ndiponso kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova analumbira kupatsa makolo anu ndi zidzukulu zawo, lomwe ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi.
כי הארץ אשר אתה בא שמה לרשתה לא כארץ מצרים הוא אשר יצאתם משם אשר תזרע את זרעך והשקית ברגלך כגן הירק׃ | 10 |
Dziko limene mukukalanda ndi kulowamo silokhala ngati dziko la ku Igupto kumene mukuchokera ayi, kuja mumadzala mbewu ndi kumathirira ndi mapazi anu ngati ku dimba.
והארץ אשר אתם עברים שמה לרשתה ארץ הרים ובקעת למטר השמים תשתה מים׃ | 11 |
Koma dziko limene mukalande mukawoloka Yorodani ndi dziko la mapiri ndi zigwa, dziko limene limalandira mvula kuchokera kumwamba.
ארץ אשר יהוה אלהיך דרש אתה תמיד עיני יהוה אלהיך בה מרשית השנה ועד אחרית שנה׃ | 12 |
Ili ndi dziko limene Yehova Mulungu wanu amalisamalira. Maso a Yehova Mulungu wanu amaliyangʼanira nthawi zonse kuchokera ku mayambiriro a chaka mpaka kumapeto kwake.
והיה אם שמע תשמעו אל מצותי אשר אנכי מצוה אתכם היום לאהבה את יהוה אלהיכם ולעבדו בכל לבבכם ובכל נפשכם׃ | 13 |
Choncho mukasunga mokhulupirika malamulo amene ndikukupatsani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iyeyo ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,
ונתתי מטר ארצכם בעתו יורה ומלקוש ואספת דגנך ותירשך ויצהרך׃ | 14 |
pamenepo ndidzatumiza mvula mʼdziko mwanu pa nthawi yake mʼnyengo ya dzinja ndi chilimwe, kuti mudzakolole tirigu wambiri ndi kuti mudzakhale ndi vinyo watsopano ndi mafuta.
ונתתי עשב בשדך לבהמתך ואכלת ושבעת׃ | 15 |
Ndidzakupatsani udzu mʼminda mwanu woti muzidzadyetsera ngʼombe zanu ndipo inuyo mudzadya ndi kukhuta.
השמרו לכם פן יפתה לבבכם וסרתם ועבדתם אלהים אחרים והשתחויתם להם׃ | 16 |
Dzisamalireni nokha, kuopa kuti mungakopeke mtima ndi kubwerera mʼmbuyo kuyamba kutumikira milungu ina ndi kumayigwadira.
וחרה אף יהוה בכם ועצר את השמים ולא יהיה מטר והאדמה לא תתן את יבולה ואבדתם מהרה מעל הארץ הטבה אשר יהוה נתן לכם׃ | 17 |
Mukatero Yehova Mulungu wanu adzakukwiyirani kwambiri, nadzaletsa thambo kuti lisabweretsenso mvula ndipo dziko silidzapereka zokolola. Choncho mudzawonongeka msanga mʼdziko limene Yehova akukupatsani.
ושמתם את דברי אלה על לבבכם ועל נפשכם וקשרתם אתם לאות על ידכם והיו לטוטפת בין עיניכם׃ | 18 |
Sungani mawu amenewa mu mtima mwanu ndi mʼmaganizo mwanu, muwamangirire pa mikono yanu ndipo muwayike pamphumi panu.
ולמדתם אתם את בניכם לדבר בם בשבתך בביתך ובלכתך בדרך ובשכבך ובקומך׃ | 19 |
Mawuwa muziphunzitsa ana anu, muzikamba za iwo pamene mukhala pansi mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mugona ndi pamene mukudzuka.
וכתבתם על מזוזות ביתך ובשעריך׃ | 20 |
Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu,
למען ירבו ימיכם וימי בניכם על האדמה אשר נשבע יהוה לאבתיכם לתת להם כימי השמים על הארץ׃ | 21 |
kuti inu ndi ana anu mukhale mʼdziko limene Yehova analumbira kupatsa makolo anu mpaka kalekale monga umakhalira mlengalenga pamwamba pa dziko.
כי אם שמר תשמרון את כל המצוה הזאת אשר אנכי מצוה אתכם לעשתה לאהבה את יהוה אלהיכם ללכת בכל דרכיו ולדבקה בו׃ | 22 |
Mukatsatira mosamalitsa malamulo amene ndikukupatsaniwa, kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira zake zonse ndi kumugwiritsitsa Iye
והוריש יהוה את כל הגוים האלה מלפניכם וירשתם גוים גדלים ועצמים מכם׃ | 23 |
Yehova adzapirikitsa mitundu ina yonseyi inu musanafike ndipo mudzagonjetsa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa inu.
כל המקום אשר תדרך כף רגלכם בו לכם יהיה מן המדבר והלבנון מן הנהר נהר פרת ועד הים האחרון יהיה גבלכם׃ | 24 |
Malo aliwonse amene mudzaponda adzakhala anu: dziko lanu lidzachokera ku chipululu mpaka ku Lebanoni, ndi ku Mtsinje wa Yufurate mpaka ku nyanja ya kumadzulo.
לא יתיצב איש בפניכם פחדכם ומוראכם יתן יהוה אלהיכם על פני כל הארץ אשר תדרכו בה כאשר דבר לכם׃ | 25 |
Palibe munthu amene adzalimbana nanu. Monga analonjezera, Yehova adzachititsa kuti anthu onse mʼdziko limene mukupitalo adzachite nanu mantha ndi kukuopani.
ראה אנכי נתן לפניכם היום ברכה וקללה׃ | 26 |
Taonani, lero ndikuyika dalitso ndi temberero pakati panu,
את הברכה אשר תשמעו אל מצות יהוה אלהיכם אשר אנכי מצוה אתכם היום׃ | 27 |
dalitso ngati mumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero.
והקללה אם לא תשמעו אל מצות יהוה אלהיכם וסרתם מן הדרך אשר אנכי מצוה אתכם היום ללכת אחרי אלהים אחרים אשר לא ידעתם׃ | 28 |
Temberero ngati simumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu ndi kupatuka pa njira imene ndikulamulirani lero potsata milungu ina imene simunayidziwe.
והיה כי יביאך יהוה אלהיך אל הארץ אשר אתה בא שמה לרשתה ונתתה את הברכה על הר גרזים ואת הקללה על הר עיבל׃ | 29 |
Yehova Mulungu wanu akakakufikitsani mʼdziko mukukalandalo kuti mulowemo mukanene za madalitso pa Phiri la Gerizimu, ndi za matemberero pa Phiri la Ebala.
הלא המה בעבר הירדן אחרי דרך מבוא השמש בארץ הכנעני הישב בערבה מול הגלגל אצל אלוני מרה׃ | 30 |
Monga mudziwa, mapiriwa ali kutsidya kwa Yorodani, kumadzulo kolowera dzuwa, kufupi ndi mitengo ya thundu ya More, mʼdziko la Akanaani aja okhala ku Araba moyangʼanana ndi Giligala.
כי אתם עברים את הירדן לבא לרשת את הארץ אשר יהוה אלהיכם נתן לכם וירשתם אתה וישבתם בה׃ | 31 |
Mwatsala pangʼono kuwoloka Yorodani kuti mulowe ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Mukadzalitenga dzikolo ndi kukhalamo,
ושמרתם לעשות את כל החקים ואת המשפטים אשר אנכי נתן לפניכם היום׃ | 32 |
mudzaonetsetse kuti mukumvera malangizo ndi malamulo amene ndikukuwuzani lero.