< דניאל 8 >

בשנת שלוש למלכות בלאשצר המלך חזון נראה אלי אני דניאל אחרי הנראה אלי בתחלה׃ 1
Chaka chachitatu cha ulamuliro wa mfumu Belisazara, Ine Danieli, ndinaonanso masomphenya, ena atatha amene anandionekera poyamba.
ואראה בחזון ויהי בראתי ואני בשושן הבירה אשר בעילם המדינה ואראה בחזון ואני הייתי על אובל אולי׃ 2
Ndinaona mʼmasomphenya kuti ndinali mu mzinda wotetezedwa wa Susa mʼchigawo cha Elamu. Mʼmasomphenyawo ndinaona nditayima pafupi ndi mtsinje wa Ulai.
ואשא עיני ואראה והנה איל אחד עמד לפני האבל ולו קרנים והקרנים גבהות והאחת גבהה מן השנית והגבהה עלה באחרנה׃ 3
Nditakweza maso ndinaona nkhosa yayimuna ya nyanga ziwiri, itayima pafupi ndi mtsinje. Nyanga zakezo zinali zazitali. Nyanga imodzi inali yotalika kuposa inzake, ndipo iyi inaphuka inzakeyo itamera kale.
ראיתי את האיל מנגח ימה וצפונה ונגבה וכל חיות לא יעמדו לפניו ואין מציל מידו ועשה כרצנו והגדיל׃ 4
Ndinaona nkhosa yayimunayo ikuthamanga mwaukali kupita kumadzulo, kumpoto ndi kummwera. Palibe chirombo chimene chikanatha kulimbana nayo, ndipo palibe akanatha kulanditsa kanthu kwa iyo. Iyo inachita monga inafunira ndipo inali ndi mphamvu zambiri.
ואני הייתי מבין והנה צפיר העזים בא מן המערב על פני כל הארץ ואין נוגע בארץ והצפיר קרן חזות בין עיניו׃ 5
Pamene ndinali kulingalira za zinthu zimenezi, mwadzidzidzi mbuzi yayimuna inatulukira cha kumadzulo, kudutsa dziko lonse lapansi mwaliwiro ikuyenda mʼmalele mokhamokha. Mbuzi yayimunayo inali ndi nyanga yayikulu pakati pa maso ake.
ויבא עד האיל בעל הקרנים אשר ראיתי עמד לפני האבל וירץ אליו בחמת כחו׃ 6
Inabwera molunjika nkhosa yayimuna ya nyanga ziwiri ija imene ndinaona itayima pafupi ndi mtsinje. Ndipo inayithamangira mwaukali.
וראיתיו מגיע אצל האיל ויתמרמר אליו ויך את האיל וישבר את שתי קרניו ולא היה כח באיל לעמד לפניו וישליכהו ארצה וירמסהו ולא היה מציל לאיל מידו׃ 7
Inafika pafupi ndipo inalimbana nayo mwaukali nkhosa yayimuna ija nʼkuthyola nyanga zake ziwiri. Nkhosa yayimunayo inalibenso mphamvu zogonjetsera mbuziyo; choncho mbuzi ija inagwetsa nkhosayo pansi nʼkuyipondaponda, ndipo palibe akanatha kulanditsa nkhosayo kwa mbuziyo.
וצפיר העזים הגדיל עד מאד וכעצמו נשברה הקרן הגדולה ותעלנה חזות ארבע תחתיה לארבע רוחות השמים׃ 8
Mbuziyo inayamba kudzikuza kwambiri chifukwa cha mphamvu zake koma pamene mphamvuzo zinakula kwambiri nyanga yake yayikulu inathyoka, ndipo mʼmalo mwake panamera nyanga zinayi moloza mbali zonse zinayi.
ומן האחת מהם יצא קרן אחת מצעירה ותגדל יתר אל הנגב ואל המזרח ואל הצבי׃ 9
Pa imodzi mwa nyangazo panatuluka nyanga imene inali yocheperapo koma inakula kwambiri kuloza kummwera ndi kummawa ndi kuloza dziko lokongola.
ותגדל עד צבא השמים ותפל ארצה מן הצבא ומן הכוכבים ותרמסם׃ 10
Inakula mpaka inafikira gulu lankhondo la kumwamba, ndipo inagwetsera ena a gulu lankhondolo ndi ena a gulu la nyenyezi ku dziko lapansi ndi kuwapondaponda.
ועד שר הצבא הגדיל וממנו הרים התמיד והשלך מכון מקדשו׃ 11
Inadzikuza yokha mpaka kufikira kwa mfumu ya gululo: inathetsa nsembe zimene zinkaperekedwa tsiku ndi tsiku, ndipo inagwetsa nyumba yake yopatulika.
וצבא תנתן על התמיד בפשע ותשלך אמת ארצה ועשתה והצליחה׃ 12
Gulu lake la nkhondo linathetsa nsembe zoperekera machimo za tsiku ndi tsiku; chipembedzo choonadi chinaponderezedwa pansi. Nyangayi inapambana mu zonse zimene inachita.
ואשמעה אחד קדוש מדבר ויאמר אחד קדוש לפלמוני המדבר עד מתי החזון התמיד והפשע שמם תת וקדש וצבא מרמס׃ 13
Kenaka ndinamva wina akuyankhula; ndipo woyera winanso anamufunsa kuti, “Kodi zimene ndikuziona mʼmasomphenyazi zidzatha liti? Nsembe zoperekera machimo za tsiku ndi tsiku zidzakhala zoletsedwa mpaka liti? Nanga chonyansa chosokoneza chidzakhalapo mpaka liti? Kodi gulu la ankhondo lidzapondereza malo opatulika mpaka liti?”
ויאמר אלי עד ערב בקר אלפים ושלש מאות ונצדק קדש׃ 14
Iye anandiyankha kuti, “Zidzachitika patapita masiku 2,300; pambuyo pake malo opatulika adzabwezeretsedwa monga kale.”
ויהי בראתי אני דניאל את החזון ואבקשה בינה והנה עמד לנגדי כמראה גבר׃ 15
Ine Danieli ndikuyangʼanitsitsa masomphenyawa ndi kuyesa kuwazindikira, kuwamvetsa, ndinangoona wina wooneka ngati munthu atayima patsogolo panga.
ואשמע קול אדם בין אולי ויקרא ויאמר גבריאל הבן להלז את המראה׃ 16
Ndipo ndinamva mawu a munthu kuchokera mʼmbali mwa mtsinje wa Ulai akuyitana kuti, “Gabrieli, muwuze munthuyu tanthauzo la masomphenyawo.”
ויבא אצל עמדי ובבאו נבעתי ואפלה על פני ויאמר אלי הבן בן אדם כי לעת קץ החזון׃ 17
Atayandikira kumene ndinayima, ndinachita mantha ndi kugwa chafufumimba. Iye anati, “Mwana wa munthu, zindikira kuti masomphenyawa akunena za nthawi yachimaliziro.”
ובדברו עמי נרדמתי על פני ארצה ויגע בי ויעמידני על עמדי׃ 18
Pamene ankandiyankhula ndinadzigwetsa pansi chafufumimba, nʼkugona tulo tofa nato. Kenaka anandikhudza ndi kundiyimiritsa.
ויאמר הנני מודיעך את אשר יהיה באחרית הזעם כי למועד קץ׃ 19
Iye anati, “Ine ndikuwuza zimene zidzachitike ukadzatha mkwiyo, chifukwa masomphenyawa ndi a nthawi ya chimaliziro.”
האיל אשר ראית בעל הקרנים מלכי מדי ופרס׃ 20
Nkhosa yayimuna ya nyanga ziwiri imene unayiona, ikuyimira mafumu a Amedi ndi Aperezi.
והצפיר השעיר מלך יון והקרן הגדולה אשר בין עיניו הוא המלך הראשון׃ 21
Mbuzi yayimuna ija ndi mfumu ya Agriki, ndipo nyanga yayikulu pakati pa maso ake aja ndi mfumu yoyamba.
והנשברת ותעמדנה ארבע תחתיה ארבע מלכיות מגוי יעמדנה ולא בכחו׃ 22
Kunena za nyanga inathyoka ija ndi nyanga zinayi zimene zinaphuka mʼmalo mwake zikutanthauza maufumu anayi amene adzatuluka mʼdziko lake; koma sizidzafanana mphamvu ndi ufumu woyambawo.
ובאחרית מלכותם כהתם הפשעים יעמד מלך עז פנים ומבין חידות׃ 23
“Pa masiku otsiriza a maufumuwa, machimo awo atachulukitsa, padzadzuka mfumu yaukali ndi yochenjera kwambiri.
ועצם כחו ולא בכחו ונפלאות ישחית והצליח ועשה והשחית עצומים ועם קדשים׃ 24
Idzakhala yamphamvu kwambiri koma osati mphamvu za iyo yokha. Idzawononga koopsa ndipo idzapambana mu chilichonse chimene idzachite. Mfumuyi idzawononga anthu amphamvu ndi anthu oyera omwe.
ועל שכלו והצליח מרמה בידו ובלבבו יגדיל ובשלוה ישחית רבים ועל שר שרים יעמד ובאפס יד ישבר׃ 25
Chifukwa cha kuchenjera kwake chinyengo chidzachuluka pa nthawi ya ulamuliro wake, ndipo idzadzikuza kuposa onse. Pamene oyera mtima adzaona ngati kuti ali otetezedwa, iyo idzawononga ambiri ndi kuwukira ngakhale Mfumu ya mafumu. Komabe idzawonongedwa, koma osati ndi mphamvu za munthu.
ומראה הערב והבקר אשר נאמר אמת הוא ואתה סתם החזון כי לימים רבים׃ 26
“Masomphenya okhudza madzulo ndi mmawa amene unawaona aja ndi woona, koma uwasunge masomphenyawa mwachinsinsi popeza ndi onena za masiku a mʼtsogolo kwambiri.”
ואני דניאל נהייתי ונחליתי ימים ואקום ואעשה את מלאכת המלך ואשתומם על המראה ואין מבין׃ 27
Ine Danieli ndinafowoka ndipo ndinadwala masiku angapo. Kenaka ndinadzuka ndi kupitiriza ntchito za mfumu. Ndinada nkhawa ndi masomphenyawo; ndipo sindinathe kuwamvetsa.

< דניאל 8 >