< דניאל 7 >
בשנת חדה לבלאשצר מלך בבל דניאל חלם חזה וחזוי ראשה על משכבה באדין חלמא כתב ראש מלין אמר׃ | 1 |
Chaka choyamba cha ufumu wa Belisazara wa ku Babuloni, Danieli akugona pa bedi lake analota maloto ndipo anaona masomphenya. Iye analemba malotowo mwachidule.
ענה דניאל ואמר חזה הוית בחזוי עם ליליא וארו ארבע רוחי שמיא מגיחן לימא רבא׃ | 2 |
Danieli anati, “Mʼmasomphenya anga usiku, ndinaona nyanga yayikulu ikuvunduka ndi mphepo zochokera mbali zonse zinayi za mlengalenga.
וארבע חיון רברבן סלקן מן ימא שנין דא מן דא׃ | 3 |
Ndipo mʼnyangayo munatuluka zirombo zazikulu zinayi, chilichonse chosiyana ndi chinzake.
קדמיתא כאריה וגפין די נשר לה חזה הוית עד די מריטו גפיה ונטילת מן ארעא ועל רגלין כאנש הקימת ולבב אנש יהיב לה׃ | 4 |
“Choyamba chinali ngati mkango, ndipo chinali ndi mapiko ngati a chiwombankhanga. Ndinayangʼanitsitsa, kenaka mapiko ake anakhadzuka ndipo chinanyamulidwa ndi kuyimirira ndi miyendo yake iwiri ngati munthu, ndipo anachipatsa mtima wa munthu.
וארו חיוה אחרי תנינה דמיה לדב ולשטר חד הקמת ותלת עלעין בפמה בין שניה וכן אמרין לה קומי אכלי בשר שגיא׃ | 5 |
“Ndipo ndinaona chirombo chachiwiri, chimene chimaoneka ngati chimbalangondo. Chinali chonyamuka mbali imodzi, ndipo chinapana nthiti zitatu mʼkamwa mwake pakati pa mano ake. Anachilamula kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri!’
באתר דנה חזה הוית וארו אחרי כנמר ולה גפין ארבע די עוף על גביה וארבעה ראשין לחיותא ושלטן יהיב לה׃ | 6 |
“Pambuyo pake, ndinaona chirombo china, chimene chinkaoneka ngati kambuku. Pa msana pake chinali ndi mapiko anayi onga a mbalame. Chirombo ichi chinali ndi mitu inayi, ndipo chinapatsidwa mphamvu kuti chilamulire.
באתר דנה חזה הוית בחזוי ליליא וארו חיוה רביעיה דחילה ואימתני ותקיפא יתירא ושנין די פרזל לה רברבן אכלה ומדקה ושארא ברגליה רפסה והיא משניה מן כל חיותא די קדמיה וקרנין עשר לה׃ | 7 |
“Zitatha izi, mʼmasomphenya anga usiku, ndinaonanso chirombo chachinayi chitayima patsogolo panga. Chinali choopsa, chochititsa mantha ndi champhamvu kwambiri. Chinali ndi mano akuluakulu a chitsulo. Chimati chikatekedza ndi kumeza adani ake kenaka chinapondereza chilichonse chotsala. Ichi chinali chosiyana ndi zirombo zoyambirira zija, ndipo chinali ndi nyanga khumi.
משתכל הוית בקרניא ואלו קרן אחרי זעירה סלקת ביניהון ותלת מן קרניא קדמיתא אתעקרו מן קדמיה ואלו עינין כעיני אנשא בקרנא דא ופם ממלל רברבן׃ | 8 |
“Ndikulingalira za nyangazo, ndinaona nyanga ina, yocheperapo, imene inkatuluka pakati pa zinzake. Zitatu mwa nyanga zoyamba zija zinazulidwa mwa icho. Nyanga iyi inali ndi maso a munthu ndi pakamwa pamene pankayankhula zodzitama.
חזה הוית עד די כרסון רמיו ועתיק יומין יתב לבושה כתלג חור ושער ראשה כעמר נקא כרסיה שביבין די נור גלגלוהי נור דלק׃ | 9 |
“Ine ndikuyangʼanabe ndinaona “mipando yaufumu ikukhazikitsidwa, ndipo Mkulu Wachikhalire anakhala pa mpando wake. Zovala zake zinali zoyera ngati chisanu chowundana; tsitsi la kumutu kwake linali loyera ngati thonje. Mpando wake waufumu unali wonga malawi a moto, ndipo mikombero yake yonse inkayaka moto.
נהר די נור נגד ונפק מן קדמוהי אלף אלפים ישמשונה ורבו רבון קדמוהי יקומון דינא יתב וספרין פתיחו׃ | 10 |
Mtsinje wa moto unkayenda, kuchokera patsogolo pake. Anthu miyandamiyanda ankamutumikira; ndipo anthu osawerengeka anayima pamaso pake. Abwalo anakhala malo awo, ndipo mabuku anatsekulidwa.
חזה הוית באדין מן קל מליא רברבתא די קרנא ממללה חזה הוית עד די קטילת חיותא והובד גשמה ויהיבת ליקדת אשא׃ | 11 |
“Ndinapitiriza kuyangʼanitsitsa chifukwa cha mawu odzitamandira amene nyanga ija inkayankhula. Ndili chiyangʼanire choncho chirombo chachinayi chija chinaphedwa ndipo thupi lake linawonongedwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto.
ושאר חיותא העדיו שלטנהון וארכה בחיין יהיבת להון עד זמן ועדן׃ | 12 |
Zirombo zina zija zinalandidwa ulamuliro wawo, koma zinaloledwa kukhala ndi moyo kwa kanthawi.
חזה הוית בחזוי ליליא וארו עם ענני שמיא כבר אנש אתה הוה ועד עתיק יומיא מטה וקדמוהי הקרבוהי׃ | 13 |
“Ndikuyangʼanabe zinthu mʼmasomphenya usiku, ndinaona wina ngati mwana wa munthu, akubwera ndi mitambo ya kumwamba. Anayandikira Mkulu Wachikhalire uja. Ena anamuperekeza kwa Iye.
ולה יהיב שלטן ויקר ומלכו וכל עממיא אמיא ולשניא לה יפלחון שלטנה שלטן עלם די לא יעדה ומלכותה די לא תתחבל׃ | 14 |
Anapatsidwa ulamuliro, ulemerero ndi mphamvu za ufumu kuti anthu a mitundu ina yonse, mayiko ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana apembedze iye. Mphamvu zake ndi mphamvu zamuyaya zimene sizidzatha, ndipo ufumu wake sudzawonongeka konse.
אתכרית רוחי אנה דניאל בגוא נדנה וחזוי ראשי יבהלנני׃ | 15 |
“Ine Danieli ndinavutika mu mzimu, ndipo zimene ndinaziona mʼmasomphenya zinandisautsa mʼmaganizo.
קרבת על חד מן קאמיא ויציבא אבעא מנה על כל דנה ואמר לי ופשר מליא יהודענני׃ | 16 |
Ndinayandikira mmodzi mwa amene anayima pamenepo ndi kumufunsa tanthauzo lenileni la zonsezi. “Kotero anandiwuza ndi kundipatsa tanthauzo la zinthu zonse izi:
אלין חיותא רברבתא די אנין ארבע ארבעה מלכין יקומון מן ארעא׃ | 17 |
‘Zirombo zikuluzikulu zinayi zija ndi maufumu anayi amene adzaoneka pa dziko lapansi.
ויקבלון מלכותא קדישי עליונין ויחסנון מלכותא עד עלמא ועד עלם עלמיא׃ | 18 |
Koma oyera mtima a Wammwambamwamba adzalandira ufumu ndipo udzakhala nawo mpaka muyaya, inde ku nthawi zonse.’
אדין צבית ליצבא על חיותא רביעיתא די הות שניה מן כלהון דחילה יתירה שניה די פרזל וטפריה די נחש אכלה מדקה ושארא ברגליה רפסה׃ | 19 |
“Kenaka ndinafuna kudziwa tanthauzo lenileni la chirombo chachinayi chija, chimene chinali chosiyana ndi zinzake zonse ndi choopsa kwambiri, cha mano ake achitsulo ndi zikhadabo zamkuwa; chirombo chimene chinapweteka ndi kumeza zinazo ndi kupondaponda chilichonse chimene chinatsala.
ועל קרניא עשר די בראשה ואחרי די סלקת ונפלו מן קדמיה תלת וקרנא דכן ועינין לה ופם ממלל רברבן וחזוה רב מן חברתה׃ | 20 |
Ndinafunanso kudziwa za nyanga khumi za pa mutu pake ndiponso ina ija, nyanga imene inaphuka pambuyo pake ndi kugwetsa zitatu zija. Imeneyi ndi nyanga ija yokhala ndi maso ndi pakamwa poyankhula modzitamandira, ndipo inkaoneka yayikulu kupambana zina zonse.
חזה הוית וקרנא דכן עבדה קרב עם קדישין ויכלה להון׃ | 21 |
Ndikuyangʼanitsitsa, nyanga imeneyi inathira nkhondo anthu oyera mtima ndi kuwagonjetsa,
עד די אתה עתיק יומיא ודינא יהב לקדישי עליונין וזמנא מטה ומלכותא החסנו קדישין׃ | 22 |
mpaka pamene Mkulu Wachikhalire uja anafika ndi kuweruza mokomera oyera mtima a Wammwambamwamba. Tsono nthawi inafika imene anthu oyera mtimawo analandira ufumu.
כן אמר חיותא רביעיתא מלכו רביעיא תהוא בארעא די תשנא מן כל מלכותא ותאכל כל ארעא ותדושנה ותדקנה׃ | 23 |
“Tsono anandifotokozera kuti, ‘Chirombo chachinayi chija ndi ufumu wachinayi umene udzaoneka pa dziko lapansi. Udzakhala wosiyana ndi maufumu anzake onse ndipo udzawononga dziko lonse lapansi. Udzalipondaponda ndi kuliphwasula.
וקרניא עשר מנה מלכותה עשרה מלכין יקמון ואחרן יקום אחריהון והוא ישנא מן קדמיא ותלתה מלכין יהשפל׃ | 24 |
Nyanga khumi zija ndiwo mafumu khumi amene adzatuluka mu ufumu umenewu. Pambuyo pake mfumu ina idzadzuka, yosiyana ndi mafumu a mʼmbuyomu; iyo idzagonjetsa mafumu atatu.
ומלין לצד עליא ימלל ולקדישי עליונין יבלא ויסבר להשניה זמנין ודת ויתיהבון בידה עד עדן ועדנין ופלג עדן׃ | 25 |
Idzayankhula motsutsana ndi Wammwambamwamba ndipo adzazunza oyera mtima ndi kusintha masiku azikondwerero ndi malamulo. Oyera mtimawo adzalamulidwa ndi mfumuyi kwa zaka zitatu ndi theka.
ודינא יתב ושלטנה יהעדון להשמדה ולהובדה עד סופא׃ | 26 |
“‘Koma bwalo lidzapereka chiweruzo, ndipo mphamvu zake zidzalandidwa ndi kuwonongedwa kotheratu mpaka muyaya.
ומלכותה ושלטנא ורבותא די מלכות תחות כל שמיא יהיבת לעם קדישי עליונין מלכותה מלכות עלם וכל שלטניא לה יפלחון וישתמעון׃ | 27 |
Kenaka ulamuliro, mphamvu ndi ukulu wa maufumu pa dziko lonse lapansi zidzaperekedwa kwa oyera mtima, a Wammwambamwamba. Ufumu wawo udzakhala ufumu wosatha, ndipo olamulira onse adzawalamulira ndi kuwamvera.’”
עד כה סופא די מלתא אנה דניאל שגיא רעיוני יבהלנני וזיוי ישתנון עלי ומלתא בלבי נטרת׃ | 28 |
“Apa ndiye pa mapeto pa nkhaniyi. Ine Danieli, ndinasautsidwa kwambiri mʼmaganizo anga, ndipo nkhope yanga inasandulika, koma ndinasunga nkhaniyi mu mtima mwanga.”