< שמואל ב 9 >

ויאמר דוד הכי יש עוד אשר נותר לבית שאול ואעשה עמו חסד בעבור יהונתן׃ 1
Davide anafunsa kuti, “Kodi alipo amene watsala mʼbanja la Sauli kuti ndimuchitire chifundo chifukwa cha Yonatani?”
ולבית שאול עבד ושמו ציבא ויקראו לו אל דוד ויאמר המלך אליו האתה ציבא ויאמר עבדך׃ 2
Tsono panali mtumiki wina wa banja la Sauli wotchedwa Ziba. Iwo anamuyitana kuti aonekere pamaso pa Davide, ndipo mfumu inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe Ziba?” Iyeyo anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”
ויאמר המלך האפס עוד איש לבית שאול ואעשה עמו חסד אלהים ויאמר ציבא אל המלך עוד בן ליהונתן נכה רגלים׃ 3
Mfumu inafunsa kuti, “Kodi palibe amene watsala wa banja la Sauli amene ndingamuchitire chifundo cha Mulungu?” Ziba anayankha mfumu kuti, “Alipo mwana wa Yonatani, koma ndi wolumala mapazi ake onse.”
ויאמר לו המלך איפה הוא ויאמר ציבא אל המלך הנה הוא בית מכיר בן עמיאל בלו דבר׃ 4
Mfumu inafunsa kuti, “Ali kuti?” Ziba anayankha kuti, “Iye ali ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli ku Lodebara.”
וישלח המלך דוד ויקחהו מבית מכיר בן עמיאל מלו דבר׃ 5
Kotero mfumu inamubweretsa kuchokera ku Lodebara, ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli.
ויבא מפיבשת בן יהונתן בן שאול אל דוד ויפל על פניו וישתחו ויאמר דוד מפיבשת ויאמר הנה עבדך׃ 6
Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli atafika kwa Davide, anawerama pansi kupereka ulemu kwa iye. Davide anati, “Mefiboseti!” Iye anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”
ויאמר לו דוד אל תירא כי עשה אעשה עמך חסד בעבור יהונתן אביך והשבתי לך את כל שדה שאול אביך ואתה תאכל לחם על שלחני תמיד׃ 7
Davide anati kwa iye, “Usachite mantha, pakuti ndidzakuchitira ndithu chifundo chifukwa cha abambo ako Yonatani. Ine ndidzakubwezera iwe dziko lonse limene linali la agogo ako Sauli, ndipo iweyo udzadya ndi ine nthawi zonse.”
וישתחו ויאמר מה עבדך כי פנית אל הכלב המת אשר כמוני׃ 8
Mefiboseti anawerama pansi ndipo anati, “Mtumiki wanu ndine yani kuti musamale galu wakufa ngati ine?”
ויקרא המלך אל ציבא נער שאול ויאמר אליו כל אשר היה לשאול ולכל ביתו נתתי לבן אדניך׃ 9
Kenaka Davide anayitanitsa Ziba, mtumiki wa Sauli, ndipo anati, “Ine ndapereka kwa chidzukulu cha mbuye wako chilichonse chimene chinali cha Sauli ndi banja lake.
ועבדת לו את האדמה אתה ובניך ועבדיך והבאת והיה לבן אדניך לחם ואכלו ומפיבשת בן אדניך יאכל תמיד לחם על שלחני ולציבא חמשה עשר בנים ועשרים עבדים׃ 10
Iwe ndi ana ndi antchito anu muzimulimira mʼdziko lake ndipo muzibweretsa zokololazo kuti chidzukulu cha mbuye wako chikhale ndi chakudya. Ndipo Mefiboseti, chidzukulu cha mbuye wako adzadya ndi ine nthawi zonse.” (Tsono Ziba anali ndi ana aamuna khumi ndi asanu ndi antchito makumi awiri).
ויאמר ציבא אל המלך ככל אשר יצוה אדני המלך את עבדו כן יעשה עבדך ומפיבשת אכל על שלחני כאחד מבני המלך׃ 11
Ndipo Ziba anati kwa mfumu, “Mtumiki wanu adzachita chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mudzalamulire wantchito wanu kuti achite.” Kotero Mefiboseti ankadya ndi Davide monga mmodzi wa ana a mfumu.
ולמפיבשת בן קטן ושמו מיכא וכל מושב בית ציבא עבדים למפיבשת׃ 12
Mefiboseti anali ndi mwana wamngʼono wamwamuna wotchedwa Mika, ndipo onse a banja la Ziba anali antchito a Mefiboseti.
ומפיבשת ישב בירושלם כי על שלחן המלך תמיד הוא אכל והוא פסח שתי רגליו׃ 13
Ndipo Mefiboseti anakhala mu Yerusalemu chifukwa nthawi zonse amadya ndi mfumu. Iye anali wolumala mapazi ake onse.

< שמואל ב 9 >