< שמואל ב 5 >
ויבאו כל שבטי ישראל אל דוד חברונה ויאמרו לאמר הננו עצמך ובשרך אנחנו׃ | 1 |
Mafuko onse a Israeli anabwera kwa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife mafupa ndi mnofu wanu.
גם אתמול גם שלשום בהיות שאול מלך עלינו אתה הייתה מוציא והמבי את ישראל ויאמר יהוה לך אתה תרעה את עמי את ישראל ואתה תהיה לנגיד על ישראל׃ | 2 |
Kale lija, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova anakuwuzani kuti, ‘Udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’”
ויבאו כל זקני ישראל אל המלך חברונה ויכרת להם המלך דוד ברית בחברון לפני יהוה וימשחו את דוד למלך על ישראל׃ | 3 |
Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, mfumu inachita nawo pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli.
בן שלשים שנה דוד במלכו ארבעים שנה מלך׃ | 4 |
Davide anali ndi zaka makumi atatu pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka makumi anayi.
בחברון מלך על יהודה שבע שנים וששה חדשים ובירושלם מלך שלשים ושלש שנה על כל ישראל ויהודה׃ | 5 |
Analamulira Yuda ali ku Hebroni kwa zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi, ndipo ali ku Yerusalemu analamulira Israeli yense ndi Yuda kwa zaka 33.
וילך המלך ואנשיו ירושלם אל היבסי יושב הארץ ויאמר לדוד לאמר לא תבוא הנה כי אם הסירך העורים והפסחים לאמר לא יבוא דוד הנה׃ | 6 |
Mfumu ndi ankhondo ake anapita ku Yerusalemu kukathira nkhondo Ayebusi amene ankakhala kumeneko. Ayebusiwo anamuwuza Davide kuti, “Inu simulowa muno. Ngakhale osaona ndi olumala akhoza kukuthamangitsani.” Iwo ankaganiza kuti, “Davide sangathe kulowa momwemo.”
וילכד דוד את מצדת ציון היא עיר דוד׃ | 7 |
Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide.
ויאמר דוד ביום ההוא כל מכה יבסי ויגע בצנור ואת הפסחים ואת העורים שנאו נפש דוד על כן יאמרו עור ופסח לא יבוא אל הבית׃ | 8 |
Pa tsiku limenelo Davide anati, “Aliyense wogonjetsa Ayebusi ayenera kudzera mʼngalande ya madzi kuti akafike kwa iwo amene ndi ‘olumala ndi osaona,’ amene ndi adani a Davide.” Nʼchifukwa chake amanena kuti, “Olumala ndi osaona sadzalowa mʼnyumba yaufumu.”
וישב דוד במצדה ויקרא לה עיר דוד ויבן דוד סביב מן המלוא וביתה׃ | 9 |
Tsono Davide anakhazikika mu lingamo ndipo mzindawu anawutcha, Mzinda wa Davide. Iye anamanga malo onse ozungulira kuyambira ku matsitso ozungulira khoma.
וילך דוד הלוך וגדול ויהוה אלהי צבאות עמו׃ | 10 |
Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.
וישלח חירם מלך צר מלאכים אל דוד ועצי ארזים וחרשי עץ וחרשי אבן קיר ויבנו בית לדוד׃ | 11 |
Tsono Hiramu mfumu ya Turo inatumiza amithenga ake kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndi amisiri a matabwa ndi amisiri a miyala, ndipo anamumangira Davide nyumba yaufumu.
וידע דוד כי הכינו יהוה למלך על ישראל וכי נשא ממלכתו בעבור עמו ישראל׃ | 12 |
Choncho Davide anazindikira kuti Yehova wamukhazikitsa kukhala mfumu ya Israeli ndipo wakuza ufumu wake chifukwa cha anthu ake, Aisraeli.
ויקח דוד עוד פלגשים ונשים מירושלם אחרי באו מחברון ויולדו עוד לדוד בנים ובנות׃ | 13 |
Davide atafika ku Yerusalemu kuchokera ku Hebroni, anakwatira azikazi natenganso akazi ena kumeneko, ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri.
ואלה שמות הילדים לו בירושלם שמוע ושובב ונתן ושלמה׃ | 14 |
Mayina a ana amene anabereka ku Yerusalemu ndi awa: Samua, Sobabu, Natani, Solomoni,
ויבחר ואלישוע ונפג ויפיע׃ | 15 |
Ibihari, Elisua, Nefegi, Yafiya,
ואלישמע ואלידע ואליפלט׃ | 16 |
Elisama, Eliada ndi Elifeleti.
וישמעו פלשתים כי משחו את דוד למלך על ישראל ויעלו כל פלשתים לבקש את דוד וישמע דוד וירד אל המצודה׃ | 17 |
Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anakalowa mu linga.
ופלשתים באו וינטשו בעמק רפאים׃ | 18 |
Ndipo Afilisti anabwera ndi kukhala momwazika mʼChigwa cha Refaimu.
וישאל דוד ביהוה לאמר האעלה אל פלשתים התתנם בידי ויאמר יהוה אל דוד עלה כי נתן אתן את הפלשתים בידך׃ | 19 |
Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka ndithu mʼmanja mwako.”
ויבא דוד בבעל פרצים ויכם שם דוד ויאמר פרץ יהוה את איבי לפני כפרץ מים על כן קרא שם המקום ההוא בעל פרצים׃ | 20 |
Choncho Davide anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Yehova waphwanya adani anga ine ndikuona.” Choncho anawatcha malowa Baala Perazimu.
ויעזבו שם את עצביהם וישאם דוד ואנשיו׃ | 21 |
Afilisti anasiya mafano awo kumeneko ndipo Davide ndi ankhondo ake anawatenga.
ויספו עוד פלשתים לעלות וינטשו בעמק רפאים׃ | 22 |
Nthawi inanso Afilisti anabweranso namwazikana mʼChigwa cha Refaimu;
וישאל דוד ביהוה ויאמר לא תעלה הסב אל אחריהם ובאת להם ממול בכאים׃ | 23 |
Davide anafunsa Yehova ndipo Yehovayo anayankha kuti, “Usapite molunjika koma uzungulire kumbuyo kwawo ndipo ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku.
ויהי בשמעך את קול צעדה בראשי הבכאים אז תחרץ כי אז יצא יהוה לפניך להכות במחנה פלשתים׃ | 24 |
Mukakangomva phokoso pa msonga za mitengo ya mkandankhuku, mukayende mofulumira, chifukwa izi zikasonyeza kuti Yehova ali patsogolo panu kukantha ankhondo a Afilisti.”
ויעש דוד כן כאשר צוהו יהוה ויך את פלשתים מגבע עד באך גזר׃ | 25 |
Kotero Davide anachita zimene Yehova anamulamulira ndipo anakantha Afilisti njira yonse kuchokera ku Geba mpaka ku Gezeri.