< שמואל ב 23 >
ואלה דברי דוד האחרנים נאם דוד בן ישי ונאם הגבר הקם על משיח אלהי יעקב ונעים זמרות ישראל׃ | 1 |
Nawa mawu otsiriza a Davide: “Mawu a Davide mwana wa Yese, mawu a munthu amene wakwezedwa ndi Wammwambamwamba, munthu wodzozedwa ndi Mulungu wa Yakobo, woyimba nyimbo za Israeli:
רוח יהוה דבר בי ומלתו על לשוני׃ | 2 |
“Mzimu wa Yehova unayankhula kudzera mwa ine; mawu ake anali pakamwa panga.
אמר אלהי ישראל לי דבר צור ישראל מושל באדם צדיק מושל יראת אלהים׃ | 3 |
Mulungu wa Israeli anayankhula, Thanthwe la Israeli linati kwa ine: ‘Pamene munthu alamulira anthu mwachilungamo, pamene alamulira moopa Mulungu,
וכאור בקר יזרח שמש בקר לא עבות מנגה ממטר דשא מארץ׃ | 4 |
amakhala ngati kuwala kwa mmamawa, mmawa wopanda mitambo, monga kuwala pamene mvula yaleka kugwa imene imameretsa udzu mʼnthaka.’
כי לא כן ביתי עם אל כי ברית עולם שם לי ערוכה בכל ושמרה כי כל ישעי וכל חפץ כי לא יצמיח׃ | 5 |
“Kodi banja langa silolungama pamaso pa Mulungu? Kodi Iye sanachite pangano losatha ndi ine, lokonzedwa ndi lotetezedwa mbali zonse? Kodi sadzakwaniritsa chipulumutso changa, ndi kundipatsa chokhumba changa chilichonse?
ובליעל כקוץ מנד כלהם כי לא ביד יקחו׃ | 6 |
Koma anthu oyipa ndiwo ayenera kutayidwa kunja ngati minga, imene sitengedwa ndi manja.
ואיש יגע בהם ימלא ברזל ועץ חנית ובאש שרוף ישרפו בשבת׃ | 7 |
Aliyense amene wayikhudza mingayo amayidula pogwiritsa ntchito chigwandali kapena ndodo ya mkondo; nayitentha pa moto.”
אלה שמות הגברים אשר לדוד ישב בשבת תחכמני ראש השלשי הוא עדינו העצנו על שמנה מאות חלל בפעם אחד׃ | 8 |
Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide: Yosebu-Basebeti wa ku Takemoni mkulu wa atsogoleri a ankhondo atatu. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 800 nthawi imodzi.
ואחרו אלעזר בן דדי בן אחחי בשלשה גברים עם דוד בחרפם בפלשתים נאספו שם למלחמה ויעלו איש ישראל׃ | 9 |
Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi. Monga mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu a Davide, iye anali ndi Davide pamene anazunza Afilisti amene anasonkhana ku Pasi-Damimu kuchita nkhondo. Kenaka ankhondo a Israeli anabwerera mʼmbuyo.
הוא קם ויך בפלשתים עד כי יגעה ידו ותדבק ידו אל החרב ויעש יהוה תשועה גדולה ביום ההוא והעם ישבו אחריו אך לפשט׃ | 10 |
Koma iye anayima osasuntha ndipo anakantha Afilisti mpaka mkono wake unatopa ndipo unakanirira ku lupanga lake. Yehova anapereka chigonjetso chachikulu pa tsiku limenelo. Asilikali anabwerera kwa Eliezara, kukatenga katundu wa anthu ophedwa.
ואחריו שמא בן אגא הררי ויאספו פלשתים לחיה ותהי שם חלקת השדה מלאה עדשים והעם נס מפני פלשתים׃ | 11 |
Wotsatana naye anali Sama mwana wa Age Mharari. Pamene Afilisti anasonkhana pamalo pamene panali munda wa mphodza, ankhondo a Israeli anathawa Afilistiwo.
ויתיצב בתוך החלקה ויצילה ויך את פלשתים ויעש יהוה תשועה גדולה׃ | 12 |
Koma Sama anayima pakati pa mundawo. Iye anawuteteza nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa.
וירדו שלשים מהשלשים ראש ויבאו אל קציר אל דוד אל מערת עדלם וחית פלשתים חנה בעמק רפאים׃ | 13 |
Pa nthawi yokolola, atatu mwa atsogoleri makumi atatu anabwera kwa Davide ku phanga la Adulamu, pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu.
ודוד אז במצודה ומצב פלשתים אז בית לחם׃ | 14 |
Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu.
ויתאוה דוד ויאמר מי ישקני מים מבאר בית לחם אשר בשער׃ | 15 |
Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!”
ויבקעו שלשת הגברים במחנה פלשתים וישאבו מים מבאר בית לחם אשר בשער וישאו ויבאו אל דוד ולא אבה לשתותם ויסך אתם ליהוה׃ | 16 |
Choncho anthu amphamvu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova.
ויאמר חלילה לי יהוה מעשתי זאת הדם האנשים ההלכים בנפשותם ולא אבה לשתותם אלה עשו שלשת הגברים׃ | 17 |
Iye anati, “Inu Yehova, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi awa si magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Ndipo Davide sanamwe madziwo. Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.
ואבישי אחי יואב בן צרויה הוא ראש השלשי והוא עורר את חניתו על שלש מאות חלל ולו שם בשלשה׃ | 18 |
Abisai mʼbale wa Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300, choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja.
מן השלשה הכי נכבד ויהי להם לשר ועד השלשה לא בא׃ | 19 |
Kodi iyeyo sanali wolemekezeka koposa? Iye anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti sanali mʼgulu la anthu atatu aja.
ובניהו בן יהוידע בן איש חי רב פעלים מקבצאל הוא הכה את שני אראל מואב והוא ירד והכה את האריה בתוך הבאר ביום השלג׃ | 20 |
Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango.
והוא הכה את איש מצרי אשר מראה וביד המצרי חנית וירד אליו בשבט ויגזל את החנית מיד המצרי ויהרגהו בחניתו׃ | 21 |
Ndipo iye anakanthanso Mwigupto wamkulu msinkhu. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe.
אלה עשה בניהו בן יהוידע ולו שם בשלשה הגברים׃ | 22 |
Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja.
מן השלשים נכבד ואל השלשה לא בא וישמהו דוד אל משמעתו׃ | 23 |
Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu aja, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza.
עשה אל אחי יואב בשלשים אלחנן בן דדו בית לחם׃ | 24 |
Mʼgulu la anthu makumi atatu aja munalinso awa: Asaheli mʼbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,
שמה החרדי אליקא החרדי׃ | 25 |
Sama Mharodi, Elika Mherodi,
חלץ הפלטי עירא בן עקש התקועי׃ | 26 |
Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa,
אביעזר הענתתי מבני החשתי׃ | 27 |
Abiezeri wa ku Anatoti, Sibekai Mhusati,
צלמון האחחי מהרי הנטפתי׃ | 28 |
Zalimoni Mwahohi, Maharai Mnetofa,
חלב בן בענה הנטפתי אתי בן ריבי מגבעת בני בנימן׃ | 29 |
Heledi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini,
בניהו פרעתני הדי מנחלי געש׃ | 30 |
Benaya Mpiratoni, Hidayi wa ku zigwa za Gaasi.
אבי עלבון הערבתי עזמות הברחמי׃ | 31 |
Abi-Aliboni Mwaribati, Azimaveti Mbarihumi,
אליחבא השעלבני בני ישן יהונתן׃ | 32 |
Eliyahiba Msaaliboni, ana a Yaseni, Yonatani,
שמה ההררי אחיאם בן שרר האררי׃ | 33 |
mwana wa Sama Mharari, Ahiamu mwana wa Sarari Mharari,
אליפלט בן אחסבי בן המעכתי אליעם בן אחיתפל הגלני׃ | 34 |
Elifeleti mwana wa Ahasibai Mmaakati, Eliamu mwana wa Ahitofele Mgiloni,
חצרו הכרמלי פערי הארבי׃ | 35 |
Heziro wa ku Karimeli, Paarai Mwaribi,
יגאל בן נתן מצבה בני הגדי׃ | 36 |
Igala mwana wa Natani wa ku Zoba, mwana wa Hagiri,
צלק העמני נחרי הבארתי נשאי כלי יואב בן צריה׃ | 37 |
Zeleki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, mnyamata wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya,
Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri,
אוריה החתי כל שלשים ושבעה׃ | 39 |
ndi Uriya Mhiti. Onse pamodzi analipo 37.