< מלכים ב 25 >

ויהי בשנת התשיעית למלכו בחדש העשירי בעשור לחדש בא נבכדנאצר מלך בבל הוא וכל חילו על ירושלם ויחן עליה ויבנו עליה דיק סביב׃ 1
Choncho mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse la ankhondo, nadzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Iye anamanga misasa kunja kwa mzindawo ndipo anamanga mitumbira ya nkhondo kuzungulira mzindawo.
ותבא העיר במצור עד עשתי עשרה שנה למלך צדקיהו׃ 2
Mzindawo anawuzinga mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha Mfumu Zedekiya.
בתשעה לחדש ויחזק הרעב בעיר ולא היה לחם לעם הארץ׃ 3
Pa tsiku lachisanu ndi chinayi pa mwezi wachinayi, njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti anthu analibe chakudya.
ותבקע העיר וכל אנשי המלחמה הלילה דרך שער בין החמתים אשר על גן המלך וכשדים על העיר סביב וילך דרך הערבה׃ 4
Pamenepo khoma la mzindawo linabowoledwa ndipo gulu lonse la ankhondo linathawa usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Iwo anathawira cha ku Araba,
וירדפו חיל כשדים אחר המלך וישגו אתו בערבות ירחו וכל חילו נפצו מעליו׃ 5
koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika.
ויתפשו את המלך ויעלו אתו אל מלך בבל רבלתה וידברו אתו משפט׃ 6
Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula, kumene anagamula mlandu wa Zedekiyayo.
ואת בני צדקיהו שחטו לעיניו ואת עיני צדקיהו עור ויאסרהו בנחשתים ויבאהו בבל׃ 7
Iwo anapha ana a Zedekiya iyeyo akuona. Kenaka anakolowola maso a Zedekiya namumanga ndi unyolo wamkuwa ndi kupita naye ku Babuloni.
ובחדש החמישי בשבעה לחדש היא שנת תשע עשרה שנה למלך נבכדנאצר מלך בבל בא נבוזראדן רב טבחים עבד מלך בבל ירושלם׃ 8
Mwezi wachisanu, pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi, mʼchaka cha 19 cha Nebukadinezara, mfumu ya Babuloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, nduna ya mfumu ya Babuloni, anabwera ku Yerusalemu.
וישרף את בית יהוה ואת בית המלך ואת כל בתי ירושלם ואת כל בית גדול שרף באש׃ 9
Iye anatentha Nyumba ya Yehova, nyumba ya mfumu pamodzi ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu. Anatentha nyumba iliyonse yofunika.
ואת חומת ירושלם סביב נתצו כל חיל כשדים אשר רב טבחים׃ 10
Gulu lonse la ankhondo la ku Babuloni limene linali ndi mkulu wa asilikali oteteza mfumu ija, linagumula malinga ozungulira Yerusalemu.
ואת יתר העם הנשארים בעיר ואת הנפלים אשר נפלו על המלך בבל ואת יתר ההמון הגלה נבוזראדן רב טבחים׃ 11
Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, ndi ena amene anathawira kwa mfumu ya Babuloni, pamodzi ndi ena onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni.
ומדלת הארץ השאיר רב טבחים לכרמים וליגבים׃ 12
Koma mkulu wa asilikaliyo anasiya anthu ena osauka kwambiri mʼdzikomo kuti azisamalira minda ya mpesa ndi minda ina.
ואת עמודי הנחשת אשר בית יהוה ואת המכנות ואת ים הנחשת אשר בבית יהוה שברו כשדים וישאו את נחשתם בבלה׃ 13
Ababuloni anaphwanya zipilala zamkuwa, maphaka ndiponso mbiya ya mkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndipo anatenga mkuwawo napita nawo ku Babuloni.
ואת הסירת ואת היעים ואת המזמרות ואת הכפות ואת כל כלי הנחשת אשר ישרתו בם לקחו׃ 14
Iwo anatenganso miphika, mafosholo, mbaniro za nyale, mbale ndi ziwiya zonse zamkuwa zimene ankagwiritsa ntchito potumikira mʼNyumbayo.
ואת המחתות ואת המזרקות אשר זהב זהב ואשר כסף כסף לקח רב טבחים׃ 15
Mkulu wa asilikali uja anatenganso zofukizira lubani ndi mbale zowazira magazi. Zonsezi zinali zopangidwa ndi golide wabwino kwambiri kapena siliva.
העמודים שנים הים האחד והמכנות אשר עשה שלמה לבית יהוה לא היה משקל לנחשת כל הכלים האלה׃ 16
Mkuwa wochokera ku zipilala ziwiri zija, mbiya ija ndi maphaka aja, zimene Solomoni anapanga mʼNyumba ya Yehova, kuchuluka kwake kunali kosawerengeka.
שמנה עשרה אמה קומת העמוד האחד וכתרת עליו נחשת וקומת הכתרת שלש אמה ושבכה ורמנים על הכתרת סביב הכל נחשת וכאלה לעמוד השני על השבכה׃ 17
Chipilala chilichonse chinali chotalika mamita asanu ndi atatu. Mutu wa mkuwa umene unali pamwamba pa chipilalacho unali mita imodzi ndi theka ndipo unakongoletsedwa ndi ukonde wa makangadza a mkuwa amene anazungulira mutuwo. Chipilala chachiwiri chinali chofanana ndi chinacho, ndipo chinali ndi ukonde.
ויקח רב טבחים את שריה כהן הראש ואת צפניהו כהן משנה ואת שלשת שמרי הסף׃ 18
Mkulu wa asilikali uja anagwira ukapolo mkulu wa ansembe Seraya, Zefaniya wachiwiri wa mkulu wa ansembe ndi alonda atatu apakhomo.
ומן העיר לקח סריס אחד אשר הוא פקיד על אנשי המלחמה וחמשה אנשים מראי פני המלך אשר נמצאו בעיר ואת הספר שר הצבא המצבא את עם הארץ וששים איש מעם הארץ הנמצאים בעיר׃ 19
Mwa anthu amene anali mu mzindamo, anatenga mkulu amene ankalamulira ankhondo ndiponso alangizi asanu a mfumu. Anatenganso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo amene ankalemba anthu ntchito ya usilikali mʼdzikomo pamodzi ndi anthu ake 60 amene anali mu mzindamo.
ויקח אתם נבוזראדן רב טבחים וילך אתם על מלך בבל רבלתה׃ 20
Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anawatenga onsewo napita nawo kwa mfumu ya Babuloni ku Ribula.
ויך אתם מלך בבל וימיתם ברבלה בארץ חמת ויגל יהודה מעל אדמתו׃ 21
Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloni inalamula kuti awakwapule ndi kuwapha. Choncho Ayuda anatengedwa ukapolo kuwachotsa mʼdziko lawo.
והעם הנשאר בארץ יהודה אשר השאיר נבוכדנאצר מלך בבל ויפקד עליהם את גדליהו בן אחיקם בן שפן׃ 22
Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kukhala woyangʼanira anthu amene anatsala ku Yuda.
וישמעו כל שרי החילים המה והאנשים כי הפקיד מלך בבל את גדליהו ויבאו אל גדליהו המצפה וישמעאל בן נתניה ויוחנן בן קרח ושריה בן תנחמת הנטפתי ויאזניהו בן המעכתי המה ואנשיהם׃ 23
Atsogoleri onse ankhondo ndi anthu awo atamva kuti mfumu ya Babuloni yasankha Gedaliya kukhala bwanamkubwa, anabwera kwa Gedaliya ku Mizipa. Atsogoleriwo mayina awo anali awa: Ismaeli mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti wa ku Netofa ndi Yaazaniya mwana wa Maakati, pamodzi ndi anthu awo.
וישבע להם גדליהו ולאנשיהם ויאמר להם אל תיראו מעבדי הכשדים שבו בארץ ועבדו את מלך בבל ויטב לכם׃ 24
Gedaliya analumbira powatsimikizira iwo ndi anthu awo. Iye anati, “Musachite mantha ndi atsogoleri Ababuloniwa. Khalani mʼdziko muno ndipo tumikirani mfumu ya Babuloni. Mukatero zinthu zidzakuyenderani bwino.”
ויהי בחדש השביעי בא ישמעאל בן נתניה בן אלישמע מזרע המלוכה ועשרה אנשים אתו ויכו את גדליהו וימת ואת היהודים ואת הכשדים אשר היו אתו במצפה׃ 25
Koma pa mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaeli mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa banja laufumu, anabwera ndi anthu khumi ndipo anapha Gedaliya pamodzi ndi Ayuda ndi anthu a ku Babuloni amene anali naye limodzi ku Mizipa.
ויקמו כל העם מקטן ועד גדול ושרי החילים ויבאו מצרים כי יראו מפני כשדים׃ 26
Chifukwa cha zimenezi, anthu onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo anathawira ku Igupto chifukwa choopa Ababuloni.
ויהי בשלשים ושבע שנה לגלות יהויכין מלך יהודה בשנים עשר חדש בעשרים ושבעה לחדש נשא אויל מרדך מלך בבל בשנת מלכו את ראש יהויכין מלך יהודה מבית כלא׃ 27
Pa chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini mfumu ya Yuda, chaka chimene Evili-Merodaki anakhala mfumu ya Babuloni, anamasula Yehoyakini mʼndende pa mwezi wa 12 pa tsiku la 27.
וידבר אתו טבות ויתן את כסאו מעל כסא המלכים אשר אתו בבבל׃ 28
Anamukomera mtima namukweza kupambana mafumu ena onse amene anali naye ku Babuloni.
ושנא את בגדי כלאו ואכל לחם תמיד לפניו כל ימי חייו׃ 29
Choncho Yoyakini anavula zovala zake za ku ndende, ndipo ankadya ndi mfumu masiku onse a moyo wake.
וארחתו ארחת תמיד נתנה לו מאת המלך דבר יום ביומו כל ימי חיו׃ 30
Mfumu inkamupatsa Yehoyakini chakudya tsiku lililonse pa moyo wake wonse.

< מלכים ב 25 >