< מלכים ב 22 >
בן שמנה שנה יאשיהו במלכו ושלשים ואחת שנה מלך בירושלם ושם אמו ידידה בת עדיה מבצקת׃ | 1 |
Yosiya anakhala mfumu ali ndi zaka zisanu ndi zitatu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 31. Amayi ake anali Yedida mwana wa Adaiya wochokera ku Bozikati.
ויעש הישר בעיני יהוה וילך בכל דרך דוד אביו ולא סר ימין ושמאול׃ | 2 |
Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira zonse za Davide kholo lake, osatembenukira kumanja kapena kumanzere.
ויהי בשמנה עשרה שנה למלך יאשיהו שלח המלך את שפן בן אצליהו בן משלם הספר בית יהוה לאמר׃ | 3 |
Mʼchaka cha 18 cha ufumu wake, Mfumu Yosiya anatuma mlembi wa nyumba ya mfumu, Safani, mwana wa Azariya, mwana wa Mesulamu, ku Nyumba ya Yehova. Iye anati,
עלה אל חלקיהו הכהן הגדול ויתם את הכסף המובא בית יהוה אשר אספו שמרי הסף מאת העם׃ | 4 |
“Pita kwa mkulu wa ansembe Hilikiya ndipo ukamuwuze kuti awerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Yehova, zimene alonda a pa khomo anasonkhanitsa kwa anthu.
ויתנה על יד עשי המלאכה המפקדים בבית יהוה ויתנו אתו לעשי המלאכה אשר בבית יהוה לחזק בדק הבית׃ | 5 |
Ndalamazo azipereke kwa anthu amene asankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Ndipo anthu amenewa azilipira antchito amene akukonzanso Nyumba ya Yehova,
לחרשים ולבנים ולגדרים ולקנות עצים ואבני מחצב לחזק את הבית׃ | 6 |
amisiri a matabwa, amisiri omanga ndi amisiri a miyala. Iwo akagulenso matabwa ndi miyala yosemedwa kuti akonzere Nyumba ya Yehova.
אך לא יחשב אתם הכסף הנתן על ידם כי באמונה הם עשים׃ | 7 |
Koma anthu amene apatsidwa ndalama zolipira antchito okonza Nyumbayo asawafunse za kagwiritsidwe ntchito ka ndalamazo, popeza ndi anthu wokhulupirika.”
ויאמר חלקיהו הכהן הגדול על שפן הספר ספר התורה מצאתי בבית יהוה ויתן חלקיה את הספר אל שפן ויקראהו׃ | 8 |
Mkulu wa ansembe Hilikiya anawuza Safani, mlembiyo kuti, “Ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Anapereka bukulo kwa Safani amene analiwerenga.
ויבא שפן הספר אל המלך וישב את המלך דבר ויאמר התיכו עבדיך את הכסף הנמצא בבית ויתנהו על יד עשי המלאכה המפקדים בית יהוה׃ | 9 |
Ndipo Safani mlembi uja, anapita nakafotokozera mfumu kuti, “Atumiki anu apereka ndalama zija zinali mʼNyumba ya Yehova kwa anthu amene akugwira ntchito ndi kuyangʼanira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova.”
ויגד שפן הספר למלך לאמר ספר נתן לי חלקיה הכהן ויקראהו שפן לפני המלך׃ | 10 |
Kenaka Safani mlembiyo, anafotokozera mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsa buku.” Ndipo Safani analiwerenga pamaso pa mfumu.
ויהי כשמע המלך את דברי ספר התורה ויקרע את בגדיו׃ | 11 |
Mfumu itamva mawu a mʼBuku la Malamulo, inangʼamba zovala zake.
ויצו המלך את חלקיה הכהן ואת אחיקם בן שפן ואת עכבור בן מיכיה ואת שפן הספר ואת עשיה עבד המלך לאמר׃ | 12 |
Iyo inalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Akibo mwana wa Mikaya, Safani mlembi uja ndi Asaiya mtumiki wa mfumu, kuti,
לכו דרשו את יהוה בעדי ובעד העם ובעד כל יהודה על דברי הספר הנמצא הזה כי גדולה חמת יהוה אשר היא נצתה בנו על אשר לא שמעו אבתינו על דברי הספר הזה לעשות ככל הכתוב עלינו׃ | 13 |
“Pitani mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa anthu onse a mʼdziko la Yuda, za zomwe zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu kwambiri pa ife ndipo watiyakira chifukwa makolo athu sanamvere mawu a buku ili. Iwo sanachite molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼmenemu zokhudza ife.”
וילך חלקיהו הכהן ואחיקם ועכבור ושפן ועשיה אל חלדה הנביאה אשת שלם בן תקוה בן חרחס שמר הבגדים והיא ישבת בירושלם במשנה וידברו אליה׃ | 14 |
Choncho Hilikiya wansembe, Ahikamu, Akibo, Safani ndi Asaiya anapita kukayankhula ndi Hulida, mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala zaufumu. Mneneri wamkaziyu ankakhala mu Yerusalemu, ku chigawo chachiwiri cha mzindawo.
ותאמר אליהם כה אמר יהוה אלהי ישראל אמרו לאיש אשר שלח אתכם אלי׃ | 15 |
Ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Kamuwuzeni munthu amene wakutumani kwa ine kuti,
כה אמר יהוה הנני מביא רעה אל המקום הזה ועל ישביו את כל דברי הספר אשר קרא מלך יהודה׃ | 16 |
‘Ichi ndi chimene Yehova akunena: Taonani, ndidzabweretsa mavuto pa malo ano ndi pa anthu ake, molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼbuku limene mfumu ya Yuda yawerenga.
תחת אשר עזבוני ויקטרו לאלהים אחרים למען הכעיסני בכל מעשה ידיהם ונצתה חמתי במקום הזה ולא תכבה׃ | 17 |
Chifukwa anthuwo andisiya Ine ndi kumafukiza lubani kwa milungu ina nandikwiyitsa ndi mafano onse amene manja awo anapanga, mkwiyo wanga udzayaka pa malo ano ndipo sudzazimitsidwa.’
ואל מלך יהודה השלח אתכם לדרש את יהוה כה תאמרו אליו כה אמר יהוה אלהי ישראל הדברים אשר שמעת׃ | 18 |
Koma mfumu ya Yuda imene inakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova kayiwuzeni kuti, ‘Ichi ndi chimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena molingana ndi mawu amene unamva:
יען רך לבבך ותכנע מפני יהוה בשמעך אשר דברתי על המקום הזה ועל ישביו להיות לשמה ולקללה ותקרע את בגדיך ותבכה לפני וגם אנכי שמעתי נאם יהוה׃ | 19 |
Chifukwa unasweka mtima ndi kudzichepetsa wekha pamaso pa Yehova, pamene unamva zomwe zinayankhulidwa zotsutsana ndi malo ano ndi anthu ake, kuti adzakhala otembereredwa nasanduka bwinja, ndiponso chifukwa unangʼamba zovala ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, akutero Yehova.
לכן הנני אספך על אבתיך ונאספת אל קברתיך בשלום ולא תראינה עיניך בכל הרעה אשר אני מביא על המקום הזה וישיבו את המלך דבר׃ | 20 |
Choncho taona, Ine ndidzakutenga kupita kwa makolo ako ndipo udzayikidwa mʼmanda mwako mwamtendere. Maso ako sadzaona mavuto onse amene ndidzabweretse pamalo pano.’” Ndipo anthu aja anabwerera nakafotokoza mawu amenewa kwa mfumu.