< מלכים ב 13 >

בשנת עשרים ושלש שנה ליואש בן אחזיהו מלך יהודה מלך יהואחז בן יהוא על ישראל בשמרון שבע עשרה שנה׃ 1
Mʼchaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi, mwana wa Yehu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 17.
ויעש הרע בעיני יהוה וילך אחר חטאת ירבעם בן נבט אשר החטיא את ישראל לא סר ממנה׃ 2
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova potsatira machimo a Yeroboamu mwana Nebati amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo iye sanawaleke machimowo.
ויחר אף יהוה בישראל ויתנם ביד חזאל מלך ארם וביד בן הדד בן חזאל כל הימים׃ 3
Ndipo Yehova anakwiyira Aisraeli nawayika pansi pa ulamuliro wa Hazaeli mfumu ya Siriya ndi Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli masiku awo onse.
ויחל יהואחז את פני יהוה וישמע אליו יהוה כי ראה את לחץ ישראל כי לחץ אתם מלך ארם׃ 4
Tsono Yehowahazi anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo ndipo Yehova anamva pempho lake chifukwa anaona momwe mfumu ya Aramu inkapsinjira Aisraeli.
ויתן יהוה לישראל מושיע ויצאו מתחת יד ארם וישבו בני ישראל באהליהם כתמול שלשום׃ 5
Yehova anapatsa Aisraeli munthu woti awapulumutse ndipo anapulumuka mʼdzanja la Aramu. Choncho Aisraeli anakhala mʼnyumba zawo monga ankachitira kale.
אך לא סרו מחטאות בית ירבעם אשר החטי את ישראל בה הלך וגם האשרה עמדה בשמרון׃ 6
Komabe Aisraeli sanaleke kuchita machimo a nyumba ya Yeroboamu, amene anachimwitsa nawo Israeli. Iwo anapitirira kuchita machimowo. Ndiponso fano la Asera linakhalabe ku Samariya.
כי לא השאיר ליהואחז עם כי אם חמשים פרשים ועשרה רכב ועשרת אלפים רגלי כי אבדם מלך ארם וישמם כעפר לדש׃ 7
Yehowahazi sanatsale ndi ankhondo ambiri koma 50 okha okwera pa akavalo, magaleta khumi ndi asilikali oyenda pansi 10,000.
ויתר דברי יהואחז וכל אשר עשה וגבורתו הלוא הם כתובים על ספר דברי הימים למלכי ישראל׃ 8
Ntchito zina za Yehowahazi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
וישכב יהואחז עם אבתיו ויקברהו בשמרון וימלך יואש בנו תחתיו׃ 9
Yehowahazi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Samariya. Ndipo Yowasi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
בשנת שלשים ושבע שנה ליואש מלך יהודה מלך יהואש בן יהואחז על ישראל בשמרון שש עשרה שנה׃ 10
Mʼchaka cha 37 cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowahazi anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 16.
ויעשה הרע בעיני יהוה לא סר מכל חטאות ירבעם בן נבט אשר החטיא את ישראל בה הלך׃ 11
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo sanaleke kuchita tchimo la Yeroboamu mwana wa Nebati limene anachimwitsa nalo Israeli.
ויתר דברי יואש וכל אשר עשה וגבורתו אשר נלחם עם אמציה מלך יהודה הלוא הם כתובים על ספר דברי הימים למלכי ישראל׃ 12
Ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kuphatikizapo nkhondo yake ndi Amaziya mfumu ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
וישכב יואש עם אבתיו וירבעם ישב על כסאו ויקבר יואש בשמרון עם מלכי ישראל׃ 13
Yowasi anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo Yeroboamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. Yowasi anayikidwa mʼmanda mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israeli.
ואלישע חלה את חליו אשר ימות בו וירד אליו יואש מלך ישראל ויבך על פניו ויאמר אבי אבי רכב ישראל ופרשיו׃ 14
Tsono Elisa anadwala matenda amene anafa nawo. Yowasi mfumu ya Israeli inapita kukamuona ndipo inamulirira. Iye polira ankanena kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi okwerapo ake a Israeli!”
ויאמר לו אלישע קח קשת וחצים ויקח אליו קשת וחצים׃ 15
Elisa anamuwuza kuti, “Tenga uta ndi mivi.” Ndipo anaterodi.
ויאמר למלך ישראל הרכב ידך על הקשת וירכב ידו וישם אלישע ידיו על ידי המלך׃ 16
Elisa anawuza mfumu ya Israeli kuti, “Tenga uta mʼdzanja lako.” Pamene anatenga utawo, Elisa anayika manja ake pa manja a mfumuyo.
ויאמר פתח החלון קדמה ויפתח ויאמר אלישע ירה ויור ויאמר חץ תשועה ליהוה וחץ תשועה בארם והכית את ארם באפק עד כלה׃ 17
Elisa anamuwuza kuti, “Tsekula zenera.” Ndipo anatsekuladi. Elisa anati, “Ponya muviwo!” Ndipo anaponyadi. Elisa anati, “Muvi wa chigonjetso cha Yehova, muvi wogonjetsera Aaramu! Iwe udzawawononga kwathunthu Aaramu ku Afeki.”
ויאמר קח החצים ויקח ויאמר למלך ישראל הך ארצה ויך שלש פעמים ויעמד׃ 18
Kenaka Elisa anati, “Tenga mivi.” Ndipo mfumu inatenga miviyo. Iye anati, “Lasa pansi.” Mfumu inalasa pansi miviyo katatu nʼkuleka.
ויקצף עליו איש האלהים ויאמר להכות חמש או שש פעמים אז הכית את ארם עד כלה ועתה שלש פעמים תכה את ארם׃ 19
Munthu wa Mulungu anapsera mtima mfumuyo ndipo anati, “Ukanalasa pansi kasanu kapena kasanu nʼkamodzi. Pamenepo ukanatha kuwagonjetsa Aaramu ndi kuwawononga kwathunthu. Koma tsopano udzawagonjetsa katatu kokha.”
וימת אלישע ויקברהו וגדודי מואב יבאו בארץ בא שנה׃ 20
Elisa anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda. Tsono magulu a ankhondo a Amowabu ankabwera kudzalowa ndi kudzathira nkhondo dzikolo nthawi ya dzinja.
ויהי הם קברים איש והנה ראו את הגדוד וישליכו את האיש בקבר אלישע וילך ויגע האיש בעצמות אלישע ויחי ויקם על רגליו׃ 21
Tsiku lina Aisraeli ena akukayika maliro mʼmanda, mwadzidzidzi anaona gulu lankhondo ndipo munthu womwalirayo anamuponyera mʼmanda a Elisa. Pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, munthu wakufayo anatsitsimuka nayimirira.
וחזאל מלך ארם לחץ את ישראל כל ימי יהואחז׃ 22
Hazaeli mfumu ya Aramu inazunza Aisraeli nthawi yonse ya ulamuliro wa Yehowahazi.
ויחן יהוה אתם וירחמם ויפן אליהם למען בריתו את אברהם יצחק ויעקב ולא אבה השחיתם ולא השליכם מעל פניו עד עתה׃ 23
Koma Yehova anawachitira chifundo Aisraeliwo ndi kukhudzika ndi zomwe zinkawachitikira chifukwa cha pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Mpaka lero lino Iye sanafune kuwawononga kapena kuwachotsa pamaso pake.
וימת חזאל מלך ארם וימלך בן הדד בנו תחתיו׃ 24
Hazaeli mfumu ya Aramu inamwalira ndipo mwana wake Beni-Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake.
וישב יהואש בן יהואחז ויקח את הערים מיד בן הדד בן חזאל אשר לקח מיד יהואחז אביו במלחמה שלש פעמים הכהו יואש וישב את ערי ישראל׃ 25
Pamenepo Yowasi mwana wa Yehowahazi analandanso kwa Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli mizinda yonse imene iye analanda Yehowahazi abambo ake. Yehowasi anagonjetsa Beni-Hadadi katatu ndipo anatenganso mizinda ya Israeli.

< מלכים ב 13 >