< דברי הימים ב 34 >

בן שמונה שנים יאשיהו במלכו ושלשים ואחת שנה מלך בירושלם׃ 1
Yosiya anali wa zaka zisanu ndi zitatu pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 31.
ויעש הישר בעיני יהוה וילך בדרכי דויד אביו ולא סר ימין ושמאול׃ 2
Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova ndi kutsata makhalidwe a Davide abambo ake, osatembenukira kumanja kapena kumanzere.
ובשמונה שנים למלכו והוא עודנו נער החל לדרוש לאלהי דויד אביו ובשתים עשרה שנה החל לטהר את יהודה וירושלם מן הבמות והאשרים והפסלים והמסכות׃ 3
Mʼchaka chachisanu ndi chitatu cha ulamuliro wake, iye akanalibe wamngʼono, anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide abambo ake. Mʼchaka cha khumi ndi chiwiri iye anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu kuchotsa malo azipembedzo, mafano a Asera, milungu yosema ndi mafano owumbidwa.
וינתצו לפניו את מזבחות הבעלים והחמנים אשר למעלה מעליהם גדע והאשרים והפסלים והמסכות שבר והדק ויזרק על פני הקברים הזבחים להם׃ 4
Maguwa ansembe a Baala anagwetsedwa iye atalamulira. Anadula zidutswazidutswa maguwa ofukizira lubani amene anali pamwamba pake, ndipo anaphwanya mafano a Asera, milungu ndi zifaniziro zake. Anaziperapera ndipo anaziwaza pamwamba pa manda a amene ankapereka nsembe kwa mafanowo.
ועצמות כהנים שרף על מזבחותים ויטהר את יהודה ואת ירושלם׃ 5
Iye anatentha mafupa a ansembe pa maguwa awo, kotero iye anayeretsa Yuda ndi Yerusalemu.
ובערי מנשה ואפרים ושמעון ועד נפתלי בהר בתיהם סביב׃ 6
Ku mizinda ya Manase, Efereimu ndi Simeoni mpaka kufika ku Nafutali, ndiponso malo a mabanja owazungulira,
וינתץ את המזבחות ואת האשרים והפסלים כתת להדק וכל החמנים גדע בכל ארץ ישראל וישב לירושלם׃ 7
iye anagwetsa maguwa ansembe ndi mafano a Asera ndi kuphwanyaphwanya milungu yawo kukhala fumbi ndi kuduladula maguwa ofukizapo lubani mʼdziko lonse la Israeli. Atatero, anabwerera ku Yerusalemu.
ובשנת שמונה עשרה למלכו לטהר הארץ והבית שלח את שפן בן אצליהו ואת מעשיהו שר העיר ואת יואח בן יואחז המזכיר לחזק את בית יהוה אלהיו׃ 8
Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya, atayeretsa dziko ndi Yerusalemu, Yosiya anatuma Safani mwana wa Azariya ndi Maaseya, wolamulira mzinda pamodzi ndi Yowa mwana wa Yowahazi mlembi wolemba mbiri, kuti akonze Nyumba ya Yehova Mulungu wake.
ויבאו אל חלקיהו הכהן הגדול ויתנו את הכסף המובא בית אלהים אשר אספו הלוים שמרי הסף מיד מנשה ואפרים ומכל שארית ישראל ומכל יהודה ובנימן וישבי ירושלם׃ 9
Iwo anapita kwa Hilikiya, mkulu wa ansembe ndipo anamupatsa ndalama zimene zinaperekedwa mʼNyumba ya Mulungu, zimene Alevi amene anali alonda apakhomo analandira kuchokera kwa anthu a ku Manase, Efereimu ndi onse otsala a ku Israeli ndiponso anthu onse ochokera ku Yuda ndi Benjamini ndi okhala mu Yerusalemu.
ויתנו על יד עשה המלאכה המפקדים בבית יהוה ויתנו אתו עושי המלאכה אשר עשים בבית יהוה לבדוק ולחזק הבית׃ 10
Ndipo anazipereka mʼmanja mwa anthu amene anasankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Anthu amenewa ankalipira antchito amene ankakonzanso Nyumba ya Mulungu.
ויתנו לחרשים ולבנים לקנות אבני מחצב ועצים למחברות ולקרות את הבתים אשר השחיתו מלכי יהודה׃ 11
Iwo anaperekanso ndalama kwa amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba kuti agule miyala yosema ndi matabwa a phaso la nyumba ndi nsichi zomangira zomwe mfumu ya Yuda inalekerera kuti zigwe ndi kuwonongeka.
והאנשים עשים באמונה במלאכה ועליהם מפקדים יחת ועבדיהו הלוים מן בני מררי וזכריה ומשלם מן בני הקהתים לנצח והלוים כל מבין בכלי שיר׃ 12
Anthuwa anagwira ntchitoyi mokhulupirika. Amene ankawayangʼanira anali Yahati ndi Obadiya, Alevi ochokera ku banja la Merari, ndi Zekariya ndi Mesulamu ochokera ku banja la Kohati. Alevi onse amene anali aluso loyimbira zida za nyimbo
ועל הסבלים ומנצחים לכל עשה מלאכה לעבודה ועבודה ומהלוים סופרים ושטרים ושוערים׃ 13
ankayangʼanira anthu onyamula katundu, namatsogolera anthu onse amene ankagwira ntchito iliyonse yotumikira. Alevi ena anali alembi, akapitawo ndiponso alonda apamakomo.
ובהוציאם את הכסף המובא בית יהוה מצא חלקיהו הכהן את ספר תורת יהוה ביד משה׃ 14
Pa nthawi imene ankatulutsa ndalama zimene anabwera nazo ku Nyumba ya Yehova, wansembe Hilikiya anapeza Buku la Malamulo limene linaperekedwa kudzera mwa Mose.
ויען חלקיהו ויאמר אל שפן הסופר ספר התורה מצאתי בבית יהוה ויתן חלקיהו את הספר אל שפן׃ 15
Hilikiya anati kwa Safani, mlembi wa zochitika, “Ine ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Iye analipereka kwa Safani.
ויבא שפן את הספר אל המלך וישב עוד את המלך דבר לאמר כל אשר נתן ביד עבדיך הם עשים׃ 16
Ndipo Safani anapita nalo bukulo kwa mfumu ndi kumufotokozera kuti: “Akuluakulu anu akuchita zonse zimene zinapatsidwa kwa iwo.
ויתיכו את הכסף הנמצא בבית יהוה ויתנוהו על יד המפקדים ועל יד עושי המלאכה׃ 17
Iwo alipira ndalama zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndipo azipereka kwa akapitawo ndi anthu antchito.”
ויגד שפן הסופר למלך לאמר ספר נתן לי חלקיהו הכהן ויקרא בו שפן לפני המלך׃ 18
Kenaka Safani, mlembi wa zochitika anawuza mfumu, “Wansembe, Hilikiya wandipatsa ine buku ili.” Ndipo Safani anawerenga bukulo pamaso pa mfumu.
ויהי כשמע המלך את דברי התורה ויקרע את בגדיו׃ 19
Mfumu itamva mawu a Buku la Malamulo, inangʼamba mkanjo wake.
ויצו המלך את חלקיהו ואת אחיקם בן שפן ואת עבדון בן מיכה ואת שפן הסופר ואת עשיה עבד המלך לאמר׃ 20
Iye analamula izi kwa Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Abidoni mwana wa Mika, Safani mlembi wa zochitika ndi Asaya mtumiki wa mfumu:
לכו דרשו את יהוה בעדי ובעד הנשאר בישראל וביהודה על דברי הספר אשר נמצא כי גדולה חמת יהוה אשר נתכה בנו על אשר לא שמרו אבותינו את דבר יהוה לעשות ככל הכתוב על הספר הזה׃ 21
“Pitani ndipo mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa otsala a Israeli ndi Yuda za zimene zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu umene watsanulidwa pa ife chifukwa makolo athu sanasunge mawu a Yehova. Iwo sanachite motsatira zonse zimene zalembedwa mʼbuku ili.”
וילך חלקיהו ואשר המלך אל חלדה הנביאה אשת שלם בן תוקהת בן חסרה שומר הבגדים והיא יושבת בירושלם במשנה וידברו אליה כזאת׃ 22
Hilikiya pamodzi ndi anthu amene anawatuma aja, anapita kukayankhula ndi mneneri wamkazi Hulida, amene anali mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira, wosunga zovala zaufumu. Hulida ankakhala mu Yerusalemu, mʼdera lachiwiri la mzindawo.
ותאמר להם כה אמר יהוה אלהי ישראל אמרו לאיש אשר שלח אתכם אלי׃ 23
Iye anati kwa anthuwo, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, muwuzeni munthu amene wakutumani kwa ineyo kuti,
כה אמר יהוה הנני מביא רעה על המקום הזה ועל יושביו את כל האלות הכתובות על הספר אשר קראו לפני מלך יהודה׃ 24
‘Yehova akunena kuti, Ine ndidzabweretsa mavuto pamalo pano ndi pa anthu ake, matemberero onse amene alembedwa mʼbukuli amene awerengedwa pamaso pa mfumu ya Yuda.
תחת אשר עזבוני ויקטירו לאלהים אחרים למען הכעיסני בכל מעשי ידיהם ותתך חמתי במקום הזה ולא תכבה׃ 25
Chifukwa iwo anasiya Ine ndi kufukiza lubani kwa milungu ina ndi kuwutsa mkwiyo wanga ndi zonse zimene manja awo anapanga, mkwiyo wanga udzatsanulidwa pamalo pano ndipo sudzazimitsidwa.’
ואל מלך יהודה השלח אתכם לדרוש ביהוה כה תאמרו אליו כה אמר יהוה אלהי ישראל הדברים אשר שמעת׃ 26
Uzani mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova Mulungu wa Israeli, ‘Chimene Yehova, Mulungu wa Israeli akunena mokhudzana ndi mawu amene mwamva ndi ichi:
יען רך לבבך ותכנע מלפני אלהים בשמעך את דבריו על המקום הזה ועל ישביו ותכנע לפני ותקרע את בגדיך ותבך לפני וגם אני שמעתי נאם יהוה׃ 27
Pakuti mtima wako walapa, ndipo wadzichepetsa wekha pamaso pa Mulungu pamene unamva zimene Iye ananena motsutsa malo ano ndi anthu ake, ndipo chifukwa iwe unadzichepetsa wekha pamaso pa Ine ndi kungʼamba zovala zako ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, atero Yehova.
הנני אספך אל אבתיך ונאספת אל קברתיך בשלום ולא תראינה עיניך בכל הרעה אשר אני מביא על המקום הזה ועל ישביו וישיבו את המלך דבר׃ 28
Tsono Ine ndidzakutengera kwa makolo ako, ndipo udzayikidwa mʼmanda mwamtendere. Maso ako sadzaona mavuto onse amene Ine ndidzabweretsa pa malo ano ndi pa iwo amene amakhala pano.’” Choncho iwo anatenga yankho lakelo ndi kubwerera kwa mfumu.
וישלח המלך ויאסף את כל זקני יהודה וירושלם׃ 29
Ndipo mfumu inasonkhanitsa pamodzi akuluakulu onse a Yuda ndi Yerusalemu.
ויעל המלך בית יהוה וכל איש יהודה וישבי ירושלם והכהנים והלוים וכל העם מגדול ועד קטן ויקרא באזניהם את כל דברי ספר הברית הנמצא בית יהוה׃ 30
Iye anapita ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi anthu a Yuda, anthu a mu Yerusalemu, ansembe ndi Alevi, anthu onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Iye anawerenga pamaso pawo mawu onse a Buku la Chipangano, limene linapezeka mʼNyumba ya Yehova.
ויעמד המלך על עמדו ויכרת את הברית לפני יהוה ללכת אחרי יהוה ולשמור את מצותיו ועדותיו וחקיו בכל לבבו ובכל נפשו לעשות את דברי הברית הכתובים על הספר הזה׃ 31
Mfumu inayimirira pa chipilala chake ndipo inachitanso pangano pamaso pa Yehova: kutsatira Yehova, ndi kusunga malamulo ake, machitidwe ake ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndi moyo wake wonse, ndi kumvera mawu a pangano olembedwa mʼbukulo.
ויעמד את כל הנמצא בירושלם ובנימן ויעשו ישבי ירושלם כברית אלהים אלהי אבותיהם׃ 32
Tsono Yosiya anawuza aliyense amene anali mu Yerusalemu ndi Benjamini kuti azisunga panganoli. Anthu a mu Yerusalemu anachita izi motsata pangano la Mulungu, Mulungu wa makolo awo.
ויסר יאשיהו את כל התועבות מכל הארצות אשר לבני ישראל ויעבד את כל הנמצא בישראל לעבוד את יהוה אלהיהם כל ימיו לא סרו מאחרי יהוה אלהי אבותיהם׃ 33
Yosiya anachotsa mafano onse onyansa mʼdziko lonse limene linali la Aisraeli ndipo anawuza onse amene anali mu Israeli kutumikira Yehova Mulungu wawo. Pa masiku onse a moyo wake, iye sanaleke kutsatira Yehova, Mulungu wa makolo awo.

< דברי הימים ב 34 >