< דברי הימים ב 19 >
וישב יהושפט מלך יהודה אל ביתו בשלום לירושלם׃ | 1 |
Yehosafati, mfumu ya Yuda itabwerera mwamtendere ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu,
ויצא אל פניו יהוא בן חנני החזה ויאמר אל המלך יהושפט הלרשע לעזר ולשנאי יהוה תאהב ובזאת עליך קצף מלפני יהוה׃ | 2 |
mlosi Yehu, mwana wa Hanani, anatuluka kukakumana naye ndipo anati kwa mfumu, “Kodi nʼkoyenera kuthandiza oyipa ndi kukonda iwo amene amadana ndi Yehova? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Yehova uli pa inu.
אבל דברים טובים נמצאו עמך כי בערת האשרות מן הארץ והכינות לבבך לדרש האלהים׃ | 3 |
Komabe, muli zinthu zina zabwino mwa inu, pakuti inu mwachotsa mʼdziko muno mafano a Asera ndipo mwakhazikitsa mtima wanu pa kufunafuna Mulungu.”
וישב יהושפט בירושלם וישב ויצא בעם מבאר שבע עד הר אפרים וישיבם אל יהוה אלהי אבותיהם׃ | 4 |
Yehosafati anakakhala ku Yerusalemu, ndipo amayenda pakati pa anthu kuchokera ku Beeriseba mpaka ku dziko lamapiri la Efereimu ndipo anawatembenuzira kwa Yehova, Mulungu wa makolo awo.
ויעמד שפטים בארץ בכל ערי יהודה הבצרות לעיר ועיר׃ | 5 |
Iye anasankha oweruza mʼdzikomo, mu mzinda uliwonse wotetezedwa wa Yuda.
ויאמר אל השפטים ראו מה אתם עשים כי לא לאדם תשפטו כי ליהוה ועמכם בדבר משפט׃ | 6 |
Ndipo anawawuza kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, chifukwa simukuweruza mʼmalo mwa munthu koma Yehova, amene ali nanu pamene mukupereka chiweruzo.
ועתה יהי פחד יהוה עליכם שמרו ועשו כי אין עם יהוה אלהינו עולה ומשא פנים ומקח שחד׃ | 7 |
Tsopano kuopsa kwa Yehova kukhale pa inu. Muweruze mosamala, pakuti ndi Yehova Mulungu wathu palibe kupotoza chilungamo kapena kukondera kapenanso kulandira ziphuphu.”
וגם בירושלם העמיד יהושפט מן הלוים והכהנים ומראשי האבות לישראל למשפט יהוה ולריב וישבו ירושלם׃ | 8 |
Mu Yerusalemu, Yehosafati anasankha Alevi ena, ansembe ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli kuti aziyangʼanira Malamulo a Yehova ndi kuweruza milandu. Ndipo iwo amakhala mu Yerusalemu.
ויצו עליהם לאמר כה תעשון ביראת יהוה באמונה ובלבב שלם׃ | 9 |
Iye anawalamula kuti, “Inu mutumikire mokhulupirika ndi mtima wanu wonse moopa Yehova.
וכל ריב אשר יבוא עליכם מאחיכם הישבים בעריהם בין דם לדם בין תורה למצוה לחקים ולמשפטים והזהרתם אתם ולא יאשמו ליהוה והיה קצף עליכם ועל אחיכם כה תעשון ולא תאשמו׃ | 10 |
Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene amakhala mʼmizinda, mlandu wokhetsa magazi kapena mlandu wosamvera malamulo kapena malangizo kapena ziphunzitso zina, inu muziwachenjeza kuti asachimwire Yehova pakuti mukapanda kutero mkwiyo wake udzakhala pa inu ndi abale anu. Chitani zimenezi ndipo simudzachimwa.
והנה אמריהו כהן הראש עליכם לכל דבר יהוה וזבדיהו בן ישמעאל הנגיד לבית יהודה לכל דבר המלך ושטרים הלוים לפניכם חזקו ועשו ויהי יהוה עם הטוב׃ | 11 |
“Amariya, mkulu wa ansembe adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza Yehova, ndipo Zebadiya mwana wa Ismaeli, mtsogoleri wa fuko la Yuda, adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza mfumu ndipo Alevi adzatumikira ngati okuyangʼanirani. Muchite molimba mtima ndipo Yehova akhale ndi iwo amene adzachita bwino.”