< דברי הימים ב 11 >

ויבא רחבעם ירושלם ויקהל את בית יהודה ובנימן מאה ושמונים אלף בחור עשה מלחמה להלחם עם ישראל להשיב את הממלכה לרחבעם׃ 1
Rehobowamu atafika ku Yerusalemu anasonkhanitsa asilikali 180,000 a fuko la Yuda ndi Benjamini kuti akachite nkhondo ndi Israeli, kuti abwezeretse ufumu kwa Rehobowamu.
ויהי דבר יהוה אל שמעיהו איש האלהים לאמר׃ 2
Koma Yehova anayankhula ndi munthu wa Mulungu Semaya kuti,
אמר אל רחבעם בן שלמה מלך יהודה ואל כל ישראל ביהודה ובנימן לאמר׃ 3
“Kawuze Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda ndi Aisraeli onse ali mu Yuda ndi Benjamini kuti,
כה אמר יהוה לא תעלו ולא תלחמו עם אחיכם שובו איש לביתו כי מאתי נהיה הדבר הזה וישמעו את דברי יהוה וישבו מלכת אל ירבעם׃ 4
‘Yehova akuti: Musapite kukamenyana ndi abale anu. Pitani kwanu, aliyense wa inu, pakuti izi ndikuchita ndine.’” Choncho anamvera mawu a Yehova ndi kubwerera osapita kukamenyana ndi Yeroboamu.
וישב רחבעם בירושלם ויבן ערים למצור ביהודה׃ 5
Rehobowamu amakhala mu Yerusalemu ndipo anamanga mizinda ya chitetezo iyi mu Yuda:
ויבן את בית לחם ואת עיטם ואת תקוע׃ 6
Betelehemu, Etamu, Tekowa,
ואת בית צור ואת שוכו ואת עדלם׃ 7
Beti Zuri, Soko, Adulamu,
ואת גת ואת מרשה ואת זיף׃ 8
Gati, Maresa, Zifi,
ואת אדורים ואת לכיש ואת עזקה׃ 9
Adoraimu, Lakisi, Azeka,
ואת צרעה ואת אילון ואת חברון אשר ביהודה ובבנימן ערי מצרות׃ 10
Zora, Ayaloni ndi Hebroni. Iyi ndiye inali mizinda yotetezedwa ya Yuda ndi Benjamini.
ויחזק את המצרות ויתן בהם נגידים ואצרות מאכל ושמן ויין׃ 11
Iye anakhwimitsa chitetezo cha mizindayi ndipo anayikamo atsogoleri a ankhondo, pamodzi ndi chakudya, mafuta a olivi ndi vinyo.
ובכל עיר ועיר צנות ורמחים ויחזקם להרבה מאד ויהי לו יהודה ובנימן׃ 12
Mʼmizinda yonse anayikamo zishango zikuluzikulu ndi mikondo, ndipo anachititsa kuti mizindayo ikhale yamphamvu. Choncho iye amalamulira Yuda ndi Benjamini.
והכהנים והלוים אשר בכל ישראל התיצבו עליו מכל גבולם׃ 13
Ansembe ndi Alevi a mʼmadera onse a Israeli anakhala mbali ya Rehobowamu.
כי עזבו הלוים את מגרשיהם ואחזתם וילכו ליהודה ולירושלם כי הזניחם ירבעם ובניו מכהן ליהוה׃ 14
Alevi anasiya malo awo owetera ziweto ndi katundu wawo, ndi kubwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu chifukwa Yeroboamu ndi ana ake anawakana kukhala ansembe a Yehova.
ויעמד לו כהנים לבמות ולשעירים ולעגלים אשר עשה׃ 15
Ndipo iye anasankha ansembe akeake a pa malo opatulika ndi a mafano a mbuzi ndi mwana wangʼombe amene anapanga.
ואחריהם מכל שבטי ישראל הנתנים את לבבם לבקש את יהוה אלהי ישראל באו ירושלם לזבוח ליהוה אלהי אבותיהם׃ 16
Anthu ochokera fuko lililonse la Israeli amene anatsimikiza mitima yawo kufunafuna Yehova Mulungu wa Israeli, ankapitabe ku Yerusalemu kukapereka nsembe kwa Yehova, Mulungu wa makolo awo.
ויחזקו את מלכות יהודה ויאמצו את רחבעם בן שלמה לשנים שלוש כי הלכו בדרך דויד ושלמה לשנים שלוש׃ 17
Iwo analimbikitsa ufumu wa Yuda, ndipo anathandiza Rehobowamu mwana wa Solomoni kwa zaka zitatu. Pa nthawi imeneyi iye amatsatira zochita za Davide ndi Solomoni.
ויקח לו רחבעם אשה את מחלת בן ירימות בן דויד אביהיל בת אליאב בן ישי׃ 18
Rehobowamu anakwatira Mahalati, amene abambo ake anali Yerimoti, mwana wa Davide, ndipo amayi ake anali Abihaili, mwana wa Eliabu, mwana wa Yese.
ותלד לו בנים את יעוש ואת שמריה ואת זהם׃ 19
Mkaziyo anamubereka ana aamuna awa: Yeusi, Semariya ndi Zahamu.
ואחריה לקח את מעכה בת אבשלום ותלד לו את אביה ואת עתי ואת זיזא ואת שלמית׃ 20
Kenaka anakwatira Maaka, mwana wamkazi wa Abisalomu, amene anamubereka Abiya, Atai, Ziza ndi Selomiti.
ויאהב רחבעם את מעכה בת אבשלום מכל נשיו ופילגשיו כי נשים שמונה עשרה נשא ופילגשים ששים ויולד עשרים ושמונה בנים וששים בנות׃ 21
Rehobowamu ankamukonda Maaka mwana wa Abisalomu kuposa aliyense mwa akazi ake ndi azikazi. Iye anali ndi akazi 18, azikazi 60, ana aamuna 28 ndi ana aakazi 60.
ויעמד לראש רחבעם את אביה בן מעכה לנגיד באחיו כי להמליכו׃ 22
Rehobowamu anasankha Abiya mwana wa Maaka kuti akhale mtsogoleri pa abale ake, ndi cholinga choti adzakhale mfumu.
ויבן ויפרץ מכל בניו לכל ארצות יהודה ובנימן לכל ערי המצרות ויתן להם המזון לרב וישאל המון נשים׃ 23
Iye anachita mwanzeru, pomwaza ena mwa ana ake ku madera onse a Yuda ndi Benjamini, ndi ku mizinda yonse yotetezedwa. Iye anawapatsa zinthu zambiri ndiponso anawafunira akazi ambiri.

< דברי הימים ב 11 >