< מלכים א 3 >
ויתחתן שלמה את פרעה מלך מצרים ויקח את בת פרעה ויביאה אל עיר דוד עד כלתו לבנות את ביתו ואת בית יהוה ואת חומת ירושלם סביב׃ | 1 |
Solomoni anachita ubale ndi Farao mfumu ya ku Igupto ndipo anakwatira mwana wake wamkazi. Mkaziyo anabwera naye mu Mzinda wa Davide mpaka anatsiriza kumanga nyumba yaufumu ndi Nyumba ya Yehova ndiponso khoma lozungulira Yerusalemu.
רק העם מזבחים בבמות כי לא נבנה בית לשם יהוה עד הימים ההם׃ | 2 |
Koma anthu ankaperekabe nsembe ku malo achipembedzo osiyanasiyana chifukwa chakuti mpaka pa nthawi imeneyo Dzina la Yehova anali asanalimangire nyumba.
ויאהב שלמה את יהוה ללכת בחקות דוד אביו רק בבמות הוא מזבח ומקטיר׃ | 3 |
Solomoni anaonetsa chikondi chake pa Yehova poyenda motsatira malamulo a abambo ake Davide, kupatula kuti ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo osiyanasiyana achipembedzo.
וילך המלך גבענה לזבח שם כי היא הבמה הגדולה אלף עלות יעלה שלמה על המזבח ההוא׃ | 4 |
Mfumu inapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe popeza kumeneko ndiye kunali malo oposa malo ofunika kwambiri pachipembedzo. Kumeneko Solomoni anapereka nsembe zopsereza 1,000 pa guwa lansembe.
בגבעון נראה יהוה אל שלמה בחלום הלילה ויאמר אלהים שאל מה אתן לך׃ | 5 |
Ku Gibiyoniko Yehova anaonekera kwa Solomoni mʼmaloto usiku, ndipo Mulungu anati, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.”
ויאמר שלמה אתה עשית עם עבדך דוד אבי חסד גדול כאשר הלך לפניך באמת ובצדקה ובישרת לבב עמך ותשמר לו את החסד הגדול הזה ותתן לו בן ישב על כסאו כיום הזה׃ | 6 |
Solomoni anayankha kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino.
ועתה יהוה אלהי אתה המלכת את עבדך תחת דוד אבי ואנכי נער קטן לא אדע צאת ובא׃ | 7 |
“Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi.
ועבדך בתוך עמך אשר בחרת עם רב אשר לא ימנה ולא יספר מרב׃ | 8 |
Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga.
ונתת לעבדך לב שמע לשפט את עמך להבין בין טוב לרע כי מי יוכל לשפט את עמך הכבד הזה׃ | 9 |
Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”
וייטב הדבר בעיני אדני כי שאל שלמה את הדבר הזה׃ | 10 |
Ambuye anakondwera kuti Solomoni anapempha zimenezi.
ויאמר אלהים אליו יען אשר שאלת את הדבר הזה ולא שאלת לך ימים רבים ולא שאלת לך עשר ולא שאלת נפש איביך ושאלת לך הבין לשמע משפט׃ | 11 |
Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo,
הנה עשיתי כדבריך הנה נתתי לך לב חכם ונבון אשר כמוך לא היה לפניך ואחריך לא יקום כמוך׃ | 12 |
Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako.
וגם אשר לא שאלת נתתי לך גם עשר גם כבוד אשר לא היה כמוך איש במלכים כל ימיך׃ | 13 |
Kuwonjeza apo, ndidzakupatsa zimene sunazipemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti pa masiku onse a moyo wako sipadzakhala mfumu yofanana nawe.
ואם תלך בדרכי לשמר חקי ומצותי כאשר הלך דויד אביך והארכתי את ימיך׃ | 14 |
Ndipo ngati udzayenda mʼnjira zanga ndi kumvera malamulo anga ndiponso malangizo anga monga abambo ako Davide anachitira, ndidzakupatsa moyo wautali.”
ויקץ שלמה והנה חלום ויבוא ירושלם ויעמד לפני ארון ברית אדני ויעל עלות ויעש שלמים ויעש משתה לכל עבדיו׃ | 15 |
Kotero Solomoni anadzuka ndipo anazindikira kuti anali maloto. Iye anabwerera ku Yerusalemu nakayimirira patsogolo pa Bokosi la Chipangano la Ambuye ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Kenaka anakonzera phwando atumiki ake onse.
אז תבאנה שתים נשים זנות אל המלך ותעמדנה לפניו׃ | 16 |
Nthawi ina amayi awiri adama anabwera kwa mfumu ndipo anayima pamaso pake.
ותאמר האשה האחת בי אדני אני והאשה הזאת ישבת בבית אחד ואלד עמה בבית׃ | 17 |
Mmodzi mwa amayiwo anati, “Mbuye wanga, mayi uyu ndi ine timakhala nyumba imodzi. Ine ndinabala mwana tili limodzi ndi mnzangayu.
ויהי ביום השלישי ללדתי ותלד גם האשה הזאת ואנחנו יחדו אין זר אתנו בבית זולתי שתים אנחנו בבית׃ | 18 |
Tsiku lachitatu ine nditabala mwana, mnzangayunso anabereka mwana wake. Tinalipo awiriwiri mʼnyumbamo ndipo munalibe wina aliyense.
וימת בן האשה הזאת לילה אשר שכבה עליו׃ | 19 |
“Nthawi ya usiku mwana wa mnzangayu anafa chifukwa anamugonera.
ותקם בתוך הלילה ותקח את בני מאצלי ואמתך ישנה ותשכיבהו בחיקה ואת בנה המת השכיבה בחיקי׃ | 20 |
Tsono iyeyu anadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga ku mimba kwanga pamene ine mdzakazi wanu ndinali mʼtulo. Anamuyika mwanayo ku mimba kwake ndi kuyika mwana wake wakufayo ku mimba kwanga.
ואקם בבקר להיניק את בני והנה מת ואתבונן אליו בבקר והנה לא היה בני אשר ילדתי׃ | 21 |
Mmawa nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga ndinapeza kuti ndi wakufa! Koma kutacha nditamuyangʼanitsitsa ndinaona kuti si mwana amene ine ndinabala.”
ותאמר האשה האחרת לא כי בני החי ובנך המת וזאת אמרת לא כי בנך המת ובני החי ותדברנה לפני המלך׃ | 22 |
Koma mayi winayo anati, “Ayi! Mwana wamoyoyu ndi wanga, mwana wakufayu ndi wako.” Koma mayi woyambayo analimbikira kuti. “Ayi! Mwana wakufayu ndi wako; wamoyoyu ndi wanga.” Motero akaziwa anatsutsana pamaso pa mfumu.
ויאמר המלך זאת אמרת זה בני החי ובנך המת וזאת אמרת לא כי בנך המת ובני החי׃ | 23 |
Pamenepo mfumu inati, “Wina akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu ndipo mwana wako ndi wakufayu,’ pamene winanso akuti, ‘Ayi! Mwana wako ndi wakufayu wanga ndi wamoyoyu.’”
ויאמר המלך קחו לי חרב ויבאו החרב לפני המלך׃ | 24 |
Pamenepo mfumu inati, “Patseni lupanga.” Ndipo anabwera nalo lupanga kwa mfumu.
ויאמר המלך גזרו את הילד החי לשנים ותנו את החצי לאחת ואת החצי לאחת׃ | 25 |
Tsono mfumu inagamula kuti, “Muduleni pakati mwana wamoyoyu ndipo wina mumupatse gawo limodzi, gawo linalo mumupatse winayo.”
ותאמר האשה אשר בנה החי אל המלך כי נכמרו רחמיה על בנה ותאמר בי אדני תנו לה את הילוד החי והמת אל תמיתהו וזאת אמרת גם לי גם לך לא יהיה גזרו׃ | 26 |
Mayi amene mwana wake anali moyo anagwidwa ndi chisoni chifukwa cha mwana wakeyo ndipo anawuza mfumu kuti, “Chonde mbuye wanga, mupatseni mnzangayu mwana wamoyoyu! Musamuphe!” Koma winayo anati, “Ayi, asandipatse ine kapena iwe. Muduleni pakati!”
ויען המלך ויאמר תנו לה את הילוד החי והמת לא תמיתהו היא אמו׃ | 27 |
Choncho mfumu inagamula kuti, “Perekani mwana wamoyoyu kwa mayi woyambayu. Musamuphe, iyeyu ndiye mayi wake wa mwanayu.”
וישמעו כל ישראל את המשפט אשר שפט המלך ויראו מפני המלך כי ראו כי חכמת אלהים בקרבו לעשות משפט׃ | 28 |
Pamene Aisraeli onse anamva za chigamulo chimene mfumu inapereka, anaopa mfumuyo kwambiri, chifukwa anaona kuti mfumu inali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu zoweruzira mwachilungamo.