< מלכים א 17 >

ויאמר אליהו התשבי מתשבי גלעד אל אחאב חי יהוה אלהי ישראל אשר עמדתי לפניו אם יהיה השנים האלה טל ומטר כי אם לפי דברי׃ 1
Ndipo mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, anati kwa Ahabu, “Pali Yehova wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene ndimamutumikira, sipadzakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditanena.”
ויהי דבר יהוה אליו לאמר׃ 2
Pamenepo Yehova anayankhula ndi Eliya kuti,
לך מזה ופנית לך קדמה ונסתרת בנחל כרית אשר על פני הירדן׃ 3
“Choka kuno, upite kummawa, ukabisale mʼmbali mwa mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani.
והיה מהנחל תשתה ואת הערבים צויתי לכלכלך שם׃ 4
Uzikamwa mu mtsinjemo, ndipo ndalamula makwangwala kuti azikakudyetsa kumeneko.”
וילך ויעש כדבר יהוה וילך וישב בנחל כרית אשר על פני הירדן׃ 5
Choncho Eliya anachita zomwe Yehova anamuwuza. Anapita ku mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani, nakakhala kumeneko.
והערבים מביאים לו לחם ובשר בבקר ולחם ובשר בערב ומן הנחל ישתה׃ 6
Makwangwala ankabweretsera buledi ndi nyama mmawa ndi madzulo, ndipo ankamwa mu mtsinjemo.
ויהי מקץ ימים וייבש הנחל כי לא היה גשם בארץ׃ 7
Patapita masiku, mtsinjewo unaphwa chifukwa mvula sinagwe mʼdzikomo.
ויהי דבר יהוה אליו לאמר׃ 8
Yehova anayankhula naye kuti,
קום לך צרפתה אשר לצידון וישבת שם הנה צויתי שם אשה אלמנה לכלכלך׃ 9
“Nyamuka tsopano, pita ku Zarefati ku Sidoni ndipo ukakhale kumeneko. Ndalamula mkazi wamasiye wa kumeneko kuti azikakudyetsa.”
ויקם וילך צרפתה ויבא אל פתח העיר והנה שם אשה אלמנה מקששת עצים ויקרא אליה ויאמר קחי נא לי מעט מים בכלי ואשתה׃ 10
Choncho iye ananyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, taonani mkazi wamasiye amatola nkhuni. Anamuyitana ndi kumuwuza kuti, “Patseni madzi pangʼono mʼchikho kuti ndimwe.”
ותלך לקחת ויקרא אליה ויאמר לקחי נא לי פת לחם בידך׃ 11
Mayi wamasiye uja ankapita kukatunga madzi, Eliya anamuyitananso namuwuza kuti, “Chonde munditengerekonso buledi.”
ותאמר חי יהוה אלהיך אם יש לי מעוג כי אם מלא כף קמח בכד ומעט שמן בצפחת והנני מקששת שנים עצים ובאתי ועשיתיהו לי ולבני ואכלנהו ומתנו׃ 12
Iye anayankha kuti “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, ine ndilibe chakudya china chilichonse, koma kaufa pangʼono mʼmbiya ndi mafuta pangʼono mʼbotolo. Ine ndikutola tinkhuni tochepa kuti ndipite nato ku nyumba ndi kukaphika chakudya changa ndi cha mwana wanga, kuti tikadye kenaka tife.”
ויאמר אליה אליהו אל תיראי באי עשי כדברך אך עשי לי משם עגה קטנה בראשנה והוצאת לי ולך ולבנך תעשי באחרנה׃ 13
Eliya anati kwa iye, “Musachite mantha. Pitani mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mundipangire kachakudya pangʼono kuchokera pa ufa umene muli nawo ndi kubwera nako kwa ine, ndipo kenaka mukaphike choti mudye inuyo ndi mwana wanuyo.
כי כה אמר יהוה אלהי ישראל כד הקמח לא תכלה וצפחת השמן לא תחסר עד יום תתן יהוה גשם על פני האדמה׃ 14
Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ufa umene uli mʼmbiyamo sudzatha ndipo mafuta amene ali mʼbotolomo sadzathanso mpaka tsiku limene Yehova adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’”
ותלך ותעשה כדבר אליהו ותאכל הוא והיא וביתה ימים׃ 15
Mayi wamasiyeyo anapita nakachita zimene Eliya anamuwuza. Choncho panali chakudya cha Eliya, mayiyo pamodzi ndi banja lake lonse chimene anadya masiku ambiri.
כד הקמח לא כלתה וצפחת השמן לא חסר כדבר יהוה אשר דבר ביד אליהו׃ 16
Pakuti ufa umene unali mʼmbiya sunathe ndiponso mafuta amene anali mʼbotolo sanathe, monga momwe ananenera Yehova kudzera mwa Eliya.
ויהי אחר הדברים האלה חלה בן האשה בעלת הבית ויהי חליו חזק מאד עד אשר לא נותרה בו נשמה׃ 17
Tsiku lina mwana wake wa mkazi wamasiye uja, mwini nyumbayo, anadwala. Matenda ananka nakulirakulirabe, ndipo kenaka analeka kupuma.
ותאמר אל אליהו מה לי ולך איש האלהים באת אלי להזכיר את עוני ולהמית את בני׃ 18
Mayiyo anati kwa Eliya, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu munthu wa Mulungu? Kodi munabwera kuno kudzandikumbutsa tchimo langa ndi kudzandiphera mwana wanga?”
ויאמר אליה תני לי את בנך ויקחהו מחיקה ויעלהו אל העליה אשר הוא ישב שם וישכבהו על מטתו׃ 19
Eliya anayankha kuti, “Patseni mwana wanuyo.” Iye anatenga mwanayo mʼmanja mwa mayiyo napita naye mʼchipinda chapamwamba, kumene Eliyayo amagona, namugoneka pa bedi lake.
ויקרא אל יהוה ויאמר יהוה אלהי הגם על האלמנה אשר אני מתגורר עמה הרעות להמית את בנה׃ 20
Kenaka Eliya anafuwula kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wanga, kodi mwabweretsanso choyipa chotere pa mkazi wamasiye amene ine ndikukhala naye, pakuchititsa kuti mwana wake afe?”
ויתמדד על הילד שלש פעמים ויקרא אל יהוה ויאמר יהוה אלהי תשב נא נפש הילד הזה על קרבו׃ 21
Pamenepo Eliya anakumbatira mwanayo katatu ndi kufuwula kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wanga, mubwezereni mwanayu moyo wake!”
וישמע יהוה בקול אליהו ותשב נפש הילד על קרבו ויחי׃ 22
Yehova anamva kufuwula kwa Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unabwerera mwa iye ndipo anatsitsimuka.
ויקח אליהו את הילד וירדהו מן העליה הביתה ויתנהו לאמו ויאמר אליהו ראי חי בנך׃ 23
Eliya ananyamula mwanayo natsika naye kuchoka mʼchipinda chapamwamba chija nalowa naye mʼnyumba. Anamupereka kwa amayi ake ndipo anati, “Taonani, mwana wanu ali ndi moyo!”
ותאמר האשה אל אליהו עתה זה ידעתי כי איש אלהים אתה ודבר יהוה בפיך אמת׃ 24
Pamenepo mayiyo anati kwa Eliya, “Tsopano ndadziwa kuti ndinu munthu wa Mulungu ndipo mawu a Yehova amene mumayankhula ndi owona.”

< מלכים א 17 >