< מלכים א 13 >
והנה איש אלהים בא מיהודה בדבר יהוה אל בית אל וירבעם עמד על המזבח להקטיר׃ | 1 |
Ndipo taonani, munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda anapita ku Beteli molamulidwa ndi Yehova. Nthawi imeneyo nʼkuti Yeroboamu atayimirira pambali pa guwa akufukiza lubani.
ויקרא על המזבח בדבר יהוה ויאמר מזבח מזבח כה אמר יהוה הנה בן נולד לבית דוד יאשיהו שמו וזבח עליך את כהני הבמות המקטרים עליך ועצמות אדם ישרפו עליך׃ | 2 |
Mneneriyo anatemberera guwalo mofuwula potsata mawu a Yehova nati: “Guwa iwe, guwa iwe! Yehova akuti, ‘Taonani mʼbanja la Davide mudzabadwa mwana dzina lake Yosiya. Pa iwe, iyeyo adzaperekapo ngati nsembe, ansembe otumikira ku malo achipembedzo amene tsopano akufukiza lubani pa iwe, ndipo pa iwe adzatenthapo mafupa a anthu.’”
ונתן ביום ההוא מופת לאמר זה המופת אשר דבר יהוה הנה המזבח נקרע ונשפך הדשן אשר עליו׃ | 3 |
Tsiku lomwelo munthu wa Mulungu uja anapereka chizindikiro ichi: “Chizindikiro chimene Yehova wanena ndi ichi: Taonani guwali lidzangʼambika pakati ndipo phulusa lili pamenepo lidzamwazika.”
ויהי כשמע המלך את דבר איש האלהים אשר קרא על המזבח בבית אל וישלח ירבעם את ידו מעל המזבח לאמר תפשהו ותיבש ידו אשר שלח עליו ולא יכל להשיבה אליו׃ | 4 |
Mfumu Yeroboamu atamva zimene munthu wa Mulungu ananena motemberera guwa lansembe ku Beteli, anatambasula dzanja lake ali ku guwako ndipo anati, “Mugwireni!” Koma dzanja limene anatambasula kuloza munthu wa Mulunguyo linawuma kuti gwaa, kotero kuti sanathenso kulibweza.
והמזבח נקרע וישפך הדשן מן המזבח כמופת אשר נתן איש האלהים בדבר יהוה׃ | 5 |
Nthawi yomweyo guwa lija linangʼambika pakati ndipo phulusa lake linamwazika molingana ndi chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapereka potsata mawu a Yehova.
ויען המלך ויאמר אל איש האלהים חל נא את פני יהוה אלהיך והתפלל בעדי ותשב ידי אלי ויחל איש האלהים את פני יהוה ותשב יד המלך אליו ותהי כבראשנה׃ | 6 |
Pamenepo mfumu inati kwa munthu wa Mulunguyo, “Undipempherere kwa Yehova Mulungu wako kuti andikomere mtima ndipo undipempherere kuti dzanja langa lichire.” Choncho munthu wa Mulungu anapempha kwa Yehova, ndipo dzanja la mfumu linachiritsidwa nʼkukhala ngati momwe linalili kale.
וידבר המלך אל איש האלהים באה אתי הביתה וסעדה ואתנה לך מתת׃ | 7 |
Mfumu inati kwa munthu wa Mulunguyo, “Tiye kwathu kuti ukadye chakudya, ndipo ndidzakupatsa mphatso.”
ויאמר איש האלהים אל המלך אם תתן לי את חצי ביתך לא אבא עמך ולא אכל לחם ולא אשתה מים במקום הזה׃ | 8 |
Koma munthu wa Mulunguyo anayankha mfumu kuti, “Ngakhale mutandipatsa theka la chuma chanu, sindingapite nanu, kapena kudya chakudya, kapenanso kumwa madzi kuno.
כי כן צוה אתי בדבר יהוה לאמר לא תאכל לחם ולא תשתה מים ולא תשוב בדרך אשר הלכת׃ | 9 |
Pakuti Yehova anandilamula kuti, ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi kapena kubwerera podzera njira imene unayendamo kale.’”
וילך בדרך אחר ולא שב בדרך אשר בא בה אל בית אל׃ | 10 |
Choncho munthu wa Mulunguyo anadzera njira ina ndipo sanatsate njira imene anayendamo pobwera ku Beteliko.
ונביא אחד זקן ישב בבית אל ויבוא בנו ויספר לו את כל המעשה אשר עשה איש האלהים היום בבית אל את הדברים אשר דבר אל המלך ויספרום לאביהם׃ | 11 |
Tsono ku Beteli kunkakhala mneneri wina wokalamba. Mmodzi mwa ana ake anamufotokozera zonse zomwe munthu wa Mulungu anachita kumeneko tsiku limenelo. Anawuzanso abambo ake zimene ananena kwa mfumu.
וידבר אלהם אביהם אי זה הדרך הלך ויראו בניו את הדרך אשר הלך איש האלהים אשר בא מיהודה׃ | 12 |
Abambo awo aja anawafunsa kuti, “Kodi wadzera njira iti?” Ana akewo anamufotokozera njira imene munthu wa Mulungu wochokera ku Yudayo anadzera.
ויאמר אל בניו חבשו לי החמור ויחבשו לו החמור וירכב עליו׃ | 13 |
Ndipo abambo aja anati kwa ana akewo, “Mangireni chishalo pa bulu.” Anawo atamangirira chishalo pa bulu, nkhalambayo inakwera buluyo
וילך אחרי איש האלהים וימצאהו ישב תחת האלה ויאמר אליו האתה איש האלהים אשר באת מיהודה ויאמר אני׃ | 14 |
ndipo inalondola munthu wa Mulunguyo. Inamupeza atakhala pansi pa mtengo wa thundu ndipo inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene anabwera kuchokera ku Yuda?” Munthuyo anayankha kuti, “Inde, ndineyo.”
ויאמר אליו לך אתי הביתה ואכל לחם׃ | 15 |
Choncho mneneri wokalambayo anati kwa iye, “Tiye kwathu kuti ukadye chakudya.”
ויאמר לא אוכל לשוב אתך ולבוא אתך ולא אכל לחם ולא אשתה אתך מים במקום הזה׃ | 16 |
Munthu wa Mulungu uja anati, “Sindingabwerere nanu kapena kudya chakudya kapenanso kumwa madzi kuno.
כי דבר אלי בדבר יהוה לא תאכל לחם ולא תשתה שם מים לא תשוב ללכת בדרך אשר הלכת בה׃ | 17 |
Pakuti ndawuzidwa ndi Yehova kuti, ‘Usadye chakudya kapena kumwa madzi kumeneko kapenanso kubwerera poyenda njira imene unayendamo popita.’”
ויאמר לו גם אני נביא כמוך ומלאך דבר אלי בדבר יהוה לאמר השבהו אתך אל ביתך ויאכל לחם וישת מים כחש לו׃ | 18 |
Mneneri wokalambayo anayankha kuti, “Inenso ndine mneneri ngati iwe. Ndipo mngelo wa Yehova anayankhula nane mawu a Yehova kuti, ‘Kamubweze abwere ku nyumba yako kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi.’” Koma anamunamiza.
וישב אתו ויאכל לחם בביתו וישת מים׃ | 19 |
Choncho munthu wa Mulungu uja anabwerera naye ndipo anakadya ndi kumwa madzi mʼnyumba mwake.
ויהי הם ישבים אל השלחן ויהי דבר יהוה אל הנביא אשר השיבו׃ | 20 |
Ali pa tebulo, Yehova anayankhula ndi mneneri wokalambayo amene anamubweza munthu wa Mulunguyo.
ויקרא אל איש האלהים אשר בא מיהודה לאמר כה אמר יהוה יען כי מרית פי יהוה ולא שמרת את המצוה אשר צוך יהוה אלהיך׃ | 21 |
Iye anafuwulira munthu wa Mulungu wochokera ku Yudayo kuti, “Yehova akuti, ‘Iwe wanyoza mawu a Yehova ndipo sunasunge lamulo limene Yehova Mulungu wako anakupatsa.
ותשב ותאכל לחם ותשת מים במקום אשר דבר אליך אל תאכל לחם ואל תשת מים לא תבוא נבלתך אל קבר אבתיך׃ | 22 |
Iwe wabwerera ndi kudya chakudya ndiponso kumwa madzi ku malo amene Iye anakuwuza kuti usadye chakudya kapena kumwa madzi. Choncho mtembo wako sadzawuyika mʼmanda a makolo ako.’”
ויהי אחרי אכלו לחם ואחרי שתותו ויחבש לו החמור לנביא אשר השיבו׃ | 23 |
Munthu wa Mulungu atatha kudya ndi kumwa, mneneri amene anamubweza uja anamangirira chishalo pa bulu wa munthu wa Mulunguyo.
וילך וימצאהו אריה בדרך וימיתהו ותהי נבלתו משלכת בדרך והחמור עמד אצלה והאריה עמד אצל הנבלה׃ | 24 |
Akupita, anakumana ndi mkango pa msewu ndipo unamupha, mtembo wake unagwera pansi pa msewu, bulu uja anayima pambali pake ndipo mkango unayima pafupi ndi mtembowo.
והנה אנשים עברים ויראו את הנבלה משלכת בדרך ואת האריה עמד אצל הנבלה ויבאו וידברו בעיר אשר הנביא הזקן ישב בה׃ | 25 |
Ndipo taonani, anthu ena amene ankapita mu msewumo anaona mtembowo uli pansi potero, mkango utayima pa mbali pa mtembo uja ndipo anapita nakafotokozera anthu mu mzinda umene mumakhala mneneri wokalamba uja.
וישמע הנביא אשר השיבו מן הדרך ויאמר איש האלהים הוא אשר מרה את פי יהוה ויתנהו יהוה לאריה וישברהו וימתהו כדבר יהוה אשר דבר לו׃ | 26 |
Mneneri amene anamubweza mnzake ku njira uja atamva zimenezi, anati, “Ameneyo ndi munthu wa Mulungu amene wanyoza mawu a Yehova. Yehova wamupereka kwa mkango umene wamukhadzula ndi kumupha, monga momwe Yehova anamuchenjezera.”
וידבר אל בניו לאמר חבשו לי את החמור ויחבשו׃ | 27 |
Mneneri wokalambayo anati kwa ana ake, “Mundimangire chishalo pa bulu,” ndipo anaterodi.
וילך וימצא את נבלתו משלכת בדרך וחמור והאריה עמדים אצל הנבלה לא אכל האריה את הנבלה ולא שבר את החמור׃ | 28 |
Ndipo anapita, nakapezadi mtembo utagwera pansi mu msewu, bulu pamodzi ndi mkango atayima pambali pake. Koma mkangowo sunadye mtembowo kapena kukhadzula buluyo.
וישא הנביא את נבלת איש האלהים וינחהו אל החמור וישיבהו ויבא אל עיר הנביא הזקן לספד ולקברו׃ | 29 |
Choncho mneneri wokalambayo anatenga mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nawuyika pa bulu, ndipo anabwera nawo ku mzinda kuti alire maliro ndi kuyika mtembowo mʼmanda.
וינח את נבלתו בקברו ויספדו עליו הוי אחי׃ | 30 |
Tsono anayika mtembowo mʼmanda amene mneneri wokalamba uja anadzikonzera, ndipo anamulira pomanena kuti, “Mʼbale wanga ine! Mʼbale wanga ine!”
ויהי אחרי קברו אתו ויאמר אל בניו לאמר במותי וקברתם אתי בקבר אשר איש האלהים קבור בו אצל עצמתיו הניחו את עצמתי׃ | 31 |
Atamuyika mʼmanda, iye anati kwa ana ake, “Ine ndikafa, mudzandiyike mʼmanda amene munthu wa Mulungu wayikidwa. Mudzayike mafupa anga pambali pa mafupa ake.
כי היה יהיה הדבר אשר קרא בדבר יהוה על המזבח אשר בבית אל ועל כל בתי הבמות אשר בערי שמרון׃ | 32 |
Pakuti uthenga umene Yehova anamuyankhulitsa, wotsutsana ndi guwa lansembe la ku Beteli ndi nyumba zonse za chipembedzo za mʼmizinda ya ku Samariya, zidzachitika ndithu.”
אחר הדבר הזה לא שב ירבעם מדרכו הרעה וישב ויעש מקצות העם כהני במות החפץ ימלא את ידו ויהי כהני במות׃ | 33 |
Ngakhale izi zinachitika, Yeroboamu sanasiye njira zake zoyipa, koma anasankhanso anthu wamba kukhala ansembe pa malo ake achipembedzo. Aliyense amene ankafuna kukhala wansembe iye anamupatula kukhala wansembe.
ויהי בדבר הזה לחטאת בית ירבעם ולהכחיד ולהשמיד מעל פני האדמה׃ | 34 |
Limeneli ndiye linali tchimo la nyumba ya Yeroboamu limene linabweretsa kugwa kwake ndiponso chiwonongeko mʼdzikomo.