< דברי הימים א 23 >
ודויד זקן ושבע ימים וימלך את שלמה בנו על ישראל׃ | 1 |
Davide atakalamba, ali ndi zaka zambiri, anayika Solomoni mwana wake kukhala mfumu ya Israeli.
ויאסף את כל שרי ישראל והכהנים והלוים׃ | 2 |
Iye anasonkhanitsanso pamodzi atsogoleri onse a Israeli, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi.
ויספרו הלוים מבן שלשים שנה ומעלה ויהי מספרם לגלגלתם לגברים שלשים ושמונה אלף׃ | 3 |
Anawerenga Alevi kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo, ndipo chiwerengero cha amuna onse chinali 38,000.
מאלה לנצח על מלאכת בית יהוה עשרים וארבעה אלף ושטרים ושפטים ששת אלפים׃ | 4 |
Davide anati, “Mwa amenewa, amuna 24,000 aziyangʼanira ntchito za mʼNyumba ya Mulungu ndipo 6,000 akhale akuluakulu ndi oweruza.
וארבעת אלפים שערים וארבעת אלפים מהללים ליהוה בכלים אשר עשיתי להלל׃ | 5 |
Amuna 4,000 akhale alonda a pa zipata ndipo 4,000 azitamanda Yehova ndi zipangizo zoyimbira zimene ndazipereka ndi cholinga chimenecho.”
ויחלקם דויד מחלקות לבני לוי לגרשון קהת ומררי׃ | 6 |
Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
Ana a Geresoni: Ladani ndi Simei.
בני לעדן הראש יחיאל וזתם ויואל שלשה׃ | 8 |
Ana a Ladani: Mtsogoleri Yehieli, Zetamu ndi Yoweli. Onse analipo atatu.
בני שמעי שלמות וחזיאל והרן שלשה אלה ראשי האבות ללעדן׃ | 9 |
Ana a Simei: Selomoti, Haziyeli ndi Harani. Onse analipo atatu. Awa anali atsogoleri a mabanja a Ladani.
ובני שמעי יחת זינא ויעוש ובריעה אלה בני שמעי ארבעה׃ | 10 |
Ndipo ana a Simei anali: Yahati, Zina, Yeusi ndi Beriya. Awa anali ana a Semei. Onse analipo anayi.
ויהי יחת הראש וזיזה השני ויעוש ובריעה לא הרבו בנים ויהיו לבית אב לפקדה אחת׃ | 11 |
Mtsogoleri anali Yahati, ndipo Ziza anali wachiwiri, koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri. Kotero iwo anawerengedwa ngati banja limodzi ndipo anapatsidwa ntchito imodzinso yofanana.
בני קהת עמרם יצהר חברון ועזיאל ארבעה׃ | 12 |
Ana a Kohati: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Onse analipo anayi.
בני עמרם אהרן ומשה ויבדל אהרן להקדישו קדש קדשים הוא ובניו עד עולם להקטיר לפני יהוה לשרתו ולברך בשמו עד עולם׃ | 13 |
Ana a Amramu: Aaroni ndi Mose. Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya.
ומשה איש האלהים בניו יקראו על שבט הלוי׃ | 14 |
Ana a Mose munthu wa Mulungu anawerengedwa ngati gawo la fuko la Levi.
Ana a Mose: Geresomu ndi Eliezara.
Zidzukulu za Geresomu: Mtsogoleri anali Subaeli.
ויהיו בני אליעזר רחביה הראש ולא היה לאליעזר בנים אחרים ובני רחביה רבו למעלה׃ | 17 |
Zidzukulu za Eliezara: Mtsogoleri anali Rehabiya. Eliezara analibe ana ena aamuna, koma ana a Rehabiya anali ochuluka kwambiri.
Ana a Izihari: Mtsogoleri anali Selomiti.
בני חברון יריהו הראש אמריה השני יחזיאל השלישי ויקמעם הרביעי׃ | 19 |
Ana a Hebroni: Mtsogoleri anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, Yahazieli anali wachitatu ndipo Yekameamu anali wachinayi.
בני עזיאל מיכה הראש וישיה השני׃ | 20 |
Ana a Uzieli: Mtsogoleri anali Mika ndipo wachiwiri anali Isiya.
בני מררי מחלי ומושי בני מחלי אלעזר וקיש׃ | 21 |
Ana a Merari: Mahili ndi Musi. Ana a Mahili: Eliezara ndi Kisi.
וימת אלעזר ולא היו לו בנים כי אם בנות וישאום בני קיש אחיהם׃ | 22 |
Eliezara anamwalira wopanda ana aamuna. Iye anali ndi ana aakazi okhaokha. Abale awo, ana a Kisi, ndiwo amene anawakwatira.
בני מושי מחלי ועדר וירמות שלשה׃ | 23 |
Ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yeremoti. Onse analipo atatu.
אלה בני לוי לבית אבתיהם ראשי האבות לפקודיהם במספר שמות לגלגלתם עשה המלאכה לעבדת בית יהוה מבן עשרים שנה ומעלה׃ | 24 |
Izi zinali zidzukulu za Levi mwa mabanja awo, atsogoleri a mabanja monga momwe analembedwera mayina awo ndi monga momwenso anawerengedwera, banja lililonse pa lokha. Awa ndi anthu ogwira ntchito oyambira zaka makumi awiri zobadwa kapena kupitirirapo, amene amatumikira mʼNyumba ya Yehova.
כי אמר דויד הניח יהוה אלהי ישראל לעמו וישכן בירושלם עד לעולם׃ | 25 |
Popeza Davide anati, “Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli, wapereka mpumulo kwa anthu ake ndipo wabwera kudzakhala mu Yerusalemu kwamuyaya,
וגם ללוים אין לשאת את המשכן ואת כל כליו לעבדתו׃ | 26 |
sikofunikiranso kuti Alevi azinyamula tenti kapena zipangizo za chipembedzo.”
כי בדברי דויד האחרנים המה מספר בני לוי מבן עשרים שנה ולמעלה׃ | 27 |
Potsata malangizo otsiriza a Davide, Alevi anawerengedwa kuyambira amuna a zaka makumi awiri zakubadwa kapena kupitirirapo.
כי מעמדם ליד בני אהרן לעבדת בית יהוה על החצרות ועל הלשכות ועל טהרת לכל קדש ומעשה עבדת בית האלהים׃ | 28 |
Ntchito ya Alevi inali kuthandiza zidzukulu za Aaroni pa ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova monga kuyangʼanira mabwalo, zipinda zamʼmbali, kuyeretsa zinthu zonse zachipembedzo, ndiponso kuchita ntchito zina za mʼnyumba ya Mulungu.
וללחם המערכת ולסלת למנחה ולרקיקי המצות ולמחבת ולמרבכת ולכל משורה ומדה׃ | 29 |
Iwo amayangʼanira buledi amene amayikidwa pa tebulo, ufa wa nsembe yachakudya, timitanda ta buledi wopanda yisiti: kuphika ndi kusakaniza, ndiponso miyeso yonse ndi kukula kwake.
ולעמד בבקר בבקר להדות ולהלל ליהוה וכן לערב׃ | 30 |
Iwo amayimiriranso mmawa uliwonse kuthokoza ndi kutamanda Yehova. Amachitanso chomwecho madzulo,
ולכל העלות עלות ליהוה לשבתות לחדשים ולמעדים במספר כמשפט עליהם תמיד לפני יהוה׃ | 31 |
ndiponso popereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Sabata ndi pa chikondwerero cha Mwezi Watsopano, ndi pa nthawi yosankhidwa ya Chikondwerero. Iwo amatumikira pamaso pa Yehova nthawi zonse mwa chiwerengero chawo ndi momwe analangizidwira.
ושמרו את משמרת אהל מועד ואת משמרת הקדש ומשמרת בני אהרן אחיהם לעבדת בית יהוה׃ | 32 |
Ndipo kotero Alevi anachita ntchito yawo ya ku tenti ya msonkhano ya ku Malo Opatulika ndiponso molamulidwa ndi abale awo, zidzukulu za Aaroni, pa ntchito ya mʼNyumba ya Yehova.