< תְהִלִּים 17 >

תְּפִלָּ֗ה לְדָ֫וִ֥ד שִׁמְעָ֤ה יְהוָ֨ה ׀ צֶ֗דֶק הַקְשִׁ֥יבָה רִנָּתִ֗י הַאֲזִ֥ינָה תְפִלָּתִ֑י בְּ֝לֹ֗א שִׂפְתֵ֥י מִרְמָֽה׃ 1
Pemphero la Davide. Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo; mverani kulira kwanga. Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.
מִ֭לְּפָנֶיךָ מִשְׁפָּטִ֣י יֵצֵ֑א עֵ֝ינֶ֗יךָ תֶּחֱזֶ֥ינָה מֵישָׁרִֽים׃ 2
Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu; maso anu aone chimene ndi cholungama.
בָּ֘חַ֤נְתָּ לִבִּ֨י ׀ פָּ֘קַ֤דְתָּ לַּ֗יְלָה צְרַפְתַּ֥נִי בַל־תִּמְצָ֑א זַ֝מֹּתִ֗י בַּל־יַעֲבָר־פִּֽי׃ 3
Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku, ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu; Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
לִפְעֻלּ֣וֹת אָ֭דָם בִּדְבַ֣ר שְׂפָתֶ֑יךָ אֲנִ֥י שָׁ֝מַ֗רְתִּי אָרְח֥וֹת פָּרִֽיץ׃ 4
Kunena za ntchito za anthu, monga mwa mawu a pakamwa panu, Ine ndadzisunga ndekha posatsata njira zachiwawa.
תָּמֹ֣ךְ אֲ֭שֻׁרַי בְּמַעְגְּלוֹתֶ֑יךָ בַּל־נָמ֥וֹטּוּ פְעָמָֽי׃ 5
Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu; mapazi anga sanaterereke.
אֲנִֽי־קְרָאתִ֣יךָ כִֽי־תַעֲנֵ֣נִי אֵ֑ל הַֽט־אָזְנְךָ֥ לִ֝֗י שְׁמַ֣ע אִמְרָתִֽי׃ 6
Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha; tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.
הַפְלֵ֣ה חֲ֭סָדֶיךָ מוֹשִׁ֣יעַ חוֹסִ֑ים מִ֝מִּתְקוֹמְמִ֗ים בִּֽימִינֶֽךָ׃ 7
Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu, Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.
שָׁ֭מְרֵנִי כְּאִישׁ֣וֹן בַּת־עָ֑יִן בְּצֵ֥ל כְּ֝נָפֶ֗יךָ תַּסְתִּירֵֽנִי׃ 8
Mundisunge ine ngati mwanadiso; mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,
מִפְּנֵ֣י רְ֭שָׁעִים ז֣וּ שַׁדּ֑וּנִי אֹיְבַ֥י בְּ֝נֶ֗פֶשׁ יַקִּ֥יפוּ עָלָֽי׃ 9
kuchoka kwa oyipa amene amandizinga ine, kuchoka kwa anthu amene ndi adani anga, amene andizungulira ine.
חֶלְבָּ֥מוֹ סָּגְר֑וּ פִּ֝֗ימוֹ דִּבְּר֥וּ בְגֵאֽוּת׃ 10
Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo, ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira.
אַ֭שֻּׁרֵינוּ עַתָּ֣ה סבבוני עֵינֵיהֶ֥ם יָ֝שִׁ֗יתוּ לִנְט֥וֹת בָּאָֽרֶץ׃ 11
Andisaka, tsopano andizungulira ndi maso awo atcheru, kuti andigwetse pansi.
דִּמְיֹנ֗וֹ כְּ֭אַרְיֵה יִכְס֣וֹף לִטְר֑וֹף וְ֝כִכְפִ֗יר יֹשֵׁ֥ב בְּמִסְתָּרִֽים׃ 12
Iwo ali ngati mkango wofuna nyama; ngati mkango waukulu wokhala mobisala.
קוּמָ֤ה יְהוָ֗ה קַדְּמָ֣ה פָ֭נָיו הַכְרִיעֵ֑הוּ פַּלְּטָ֥ה נַ֝פְשִׁ֗י מֵרָשָׁ֥ע חַרְבֶּֽךָ׃ 13
Dzukani Yehova, mulimbane nawo ndipo muwagwetse pansi; landitseni kuchoka kwa oyipa ndi lupanga lanu.
מִֽמְתִ֥ים יָדְךָ֨ ׀ יְהוָ֡ה מִֽמְתִ֬ים מֵחֶ֗לֶד חֶלְקָ֥ם בַּֽחַיִּים֮ וצפינך תְּמַלֵּ֪א בִ֫טְנָ֥ם יִשְׂבְּע֥וּ בָנִ֑ים וְהִנִּ֥יחוּ יִ֝תְרָ֗ם לְעוֹלְלֵיהֶֽם׃ 14
Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere, kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno. Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu; ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri, ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.
אֲנִ֗י בְּ֭צֶדֶק אֶחֱזֶ֣ה פָנֶ֑יךָ אֶשְׂבְּעָ֥ה בְ֝הָקִ֗יץ תְּמוּנָתֶֽךָ׃ 15
Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu; pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.

< תְהִלִּים 17 >