< יְשַׁעְיָהוּ 2 >
הַדָּבָר֙ אֲשֶׁ֣ר חָזָ֔ה יְשַֽׁעְיָ֖הוּ בֶּן־אָמ֑וֹץ עַל־יְהוּדָ֖ה וִירוּשָׁלִָֽם׃ | 1 |
Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya mwana wa Amozi anaziona mʼmasomphenya:
וְהָיָ֣ה ׀ בְּאַחֲרִ֣ית הַיָּמִ֗ים נָכ֨וֹן יִֽהְיֶ֜ה הַ֤ר בֵּית־יְהוָה֙ בְּרֹ֣אשׁ הֶהָרִ֔ים וְנִשָּׂ֖א מִגְּבָע֑וֹת וְנָהֲר֥וּ אֵלָ֖יו כָּל־הַגּוֹיִֽם׃ | 2 |
Mʼmasiku otsiriza, phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse, lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse, ndipo mayiko onse adzathamangira kumeneko.
וְֽהָלְכ֞וּ עַמִּ֣ים רַבִּ֗ים וְאָמְרוּ֙ לְכ֣וּ ׀ וְנַעֲלֶ֣ה אֶל־הַר־יְהוָ֗ה אֶל־בֵּית֙ אֱלֹהֵ֣י יַעֲקֹ֔ב וְיֹרֵ֙נוּ֙ מִדְּרָכָ֔יו וְנֵלְכָ֖ה בְּאֹרְחֹתָ֑יו כִּ֤י מִצִּיּוֹן֙ תֵּצֵ֣א תוֹרָ֔ה וּדְבַר־יְהוָ֖ה מִירוּשָׁלִָֽם׃ | 3 |
Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.” Malangizo adzachokera ku Ziyoni, mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
וְשָׁפַט֙ בֵּ֣ין הַגּוֹיִ֔ם וְהוֹכִ֖יחַ לְעַמִּ֣ים רַבִּ֑ים וְכִתְּת֨וּ חַרְבוֹתָ֜ם לְאִתִּ֗ים וַחֲנִיתֽוֹתֵיהֶם֙ לְמַזְמֵר֔וֹת לֹא־יִשָּׂ֨א ג֤וֹי אֶל־גּוֹי֙ חֶ֔רֶב וְלֹא־יִלְמְד֥וּ ע֖וֹד מִלְחָמָֽה׃ פ | 4 |
Iye adzaweruza pakati pa mayiko, ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu ambiri. Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera. Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina, kapena kuphunziranso za nkhondo.
בֵּ֖ית יַעֲקֹ֑ב לְכ֥וּ וְנֵלְכָ֖ה בְּא֥וֹר יְהוָֽה׃ | 5 |
Inu nyumba ya Yakobo, bwerani, tiyeni tiyende mʼkuwala kwa Yehova.
כִּ֣י נָטַ֗שְׁתָּה עַמְּךָ֙ בֵּ֣ית יַעֲקֹ֔ב כִּ֤י מָלְאוּ֙ מִקֶּ֔דֶם וְעֹֽנְנִ֖ים כַּפְּלִשְׁתִּ֑ים וּבְיַלְדֵ֥י נָכְרִ֖ים יַשְׂפִּֽיקוּ׃ | 6 |
Inu Yehova mwawakana anthu anu, nyumba ya Yakobo. Iwo adzaza ndi zamatsenga zochokera Kummawa; amawombeza mawula ngati Afilisti, ndipo amayanjana ndi anthu osapembedza Mulungu.
וַתִּמָּלֵ֤א אַרְצוֹ֙ כֶּ֣סֶף וְזָהָ֔ב וְאֵ֥ין קֵ֖צֶה לְאֹצְרֹתָ֑יו וַתִּמָּלֵ֤א אַרְצוֹ֙ סוּסִ֔ים וְאֵ֥ין קֵ֖צֶה לְמַרְכְּבֹתָֽיו׃ | 7 |
Dziko lawo ndi lodzaza ndi siliva ndi golide; ndipo chuma chawo ndi chosatha. Dziko lawo ndi lodzaza ndi akavalo; ndipo magaleta awo ankhondo ngosawerengeka.
וַתִּמָּלֵ֥א אַרְצ֖וֹ אֱלִילִ֑ים לְמַעֲשֵׂ֤ה יָדָיו֙ יִֽשְׁתַּחֲו֔וּ לַאֲשֶׁ֥ר עָשׂ֖וּ אֶצְבְּעֹתָֽיו׃ | 8 |
Dziko lawo ndi lodzaza ndi mafano; iwo amapembedza ntchito ya manja awo, amagwadira zomwe anapanga ndi zala zawo.
וַיִּשַּׁ֥ח אָדָ֖ם וַיִּשְׁפַּל־אִ֑ישׁ וְאַל־תִּשָּׂ֖א לָהֶֽם׃ | 9 |
Tsono munthu aliyense adzachepetsedwa ndi kutsitsidwa. Inu Yehova musawakhululukire.
בּ֣וֹא בַצּ֔וּר וְהִטָּמֵ֖ן בֶּֽעָפָ֑ר מִפְּנֵי֙ פַּ֣חַד יְהוָ֔ה וּמֵהֲדַ֖ר גְּאֹנֽוֹ׃ | 10 |
Lowani mʼmatanthwe, bisalani mʼmaenje, kuthawa kuopsa kwa Yehova ndi ulemerero wa ufumu wake!
עֵינֵ֞י גַּבְה֤וּת אָדָם֙ שָׁפֵ֔ל וְשַׁ֖ח ר֣וּם אֲנָשִׁ֑ים וְנִשְׂגַּ֧ב יְהוָ֛ה לְבַדּ֖וֹ בַּיּ֥וֹם הַהֽוּא׃ ס | 11 |
Kudzikuza kwa anthu kudzatha, ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa; Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu pa tsiku limenelo.
כִּ֣י י֞וֹם לַיהוָ֧ה צְבָא֛וֹת עַ֥ל כָּל־גֵּאֶ֖ה וָרָ֑ם וְעַ֖ל כָּל־נִשָּׂ֥א וְשָׁפֵֽל׃ | 12 |
Yehova Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku limene adzatsitse onse onyada ndi odzitama, ndipo adzagonjetsa onse amphamvu,
וְעַל֙ כָּל־אַרְזֵ֣י הַלְּבָנ֔וֹן הָרָמִ֖ים וְהַנִּשָּׂאִ֑ים וְעַ֖ל כָּל־אַלּוֹנֵ֥י הַבָּשָֽׁן׃ | 13 |
tsiku la mikungudza yonse ya ku Lebanoni, yayitali ndi yoonekera patali, ndiponso la mitengo yonse ya thundu ya ku Basani,
וְעַ֖ל כָּל־הֶהָרִ֣ים הָרָמִ֑ים וְעַ֖ל כָּל־הַגְּבָע֥וֹת הַנִּשָּׂאֽוֹת׃ | 14 |
tsiku la mapiri onse ataliatali ndiponso la zitunda zonse zazitali,
וְעַ֖ל כָּל־מִגְדָּ֣ל גָּבֹ֑הַ וְעַ֖ל כָּל־חוֹמָ֥ה בְצוּרָֽה׃ | 15 |
tsiku la nsanja zonse zazitali ndiponso malinga onse olimba,
וְעַ֖ל כָּל־אֳנִיּ֣וֹת תַּרְשִׁ֑ישׁ וְעַ֖ל כָּל־שְׂכִיּ֥וֹת הַחֶמְדָּֽה׃ | 16 |
tsiku la sitima zapamadzi zonse za ku Tarisisi ndiponso la mabwato onse okongola.
וְשַׁח֙ גַּבְה֣וּת הָאָדָ֔ם וְשָׁפֵ֖ל ר֣וּם אֲנָשִׁ֑ים וְנִשְׂגַּ֧ב יְהוָ֛ה לְבַדּ֖וֹ בַּיּ֥וֹם הַהֽוּא׃ | 17 |
Kudzikuza kwa munthu kudzatha ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa, Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo,
וְהָאֱלִילִ֖ים כָּלִ֥יל יַחֲלֹֽף׃ | 18 |
ndipo mafano onse adzatheratu.
וּבָ֙אוּ֙ בִּמְעָר֣וֹת צֻרִ֔ים וּבִמְחִלּ֖וֹת עָפָ֑ר מִפְּנֵ֞י פַּ֤חַד יְהוָה֙ וּמֵהֲדַ֣ר גְּאוֹנ֔וֹ בְּקוּמ֖וֹ לַעֲרֹ֥ץ הָאָֽרֶץ׃ | 19 |
Anthu adzathawira mʼmapanga a matanthwe ndi mʼmaenje a nthaka, kuthawa mkwiyo wa Yehova, ndiponso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
בַּיּ֤וֹם הַהוּא֙ יַשְׁלִ֣יךְ הָאָדָ֔ם אֵ֚ת אֱלִילֵ֣י כַסְפּ֔וֹ וְאֵ֖ת אֱלִילֵ֣י זְהָב֑וֹ אֲשֶׁ֤ר עָֽשׂוּ־לוֹ֙ לְהִֽשְׁתַּחֲוֺ֔ת לַחְפֹּ֥ר פֵּר֖וֹת וְלָעֲטַלֵּפִֽים׃ | 20 |
Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano awo asiliva ndi mafano awo agolide, amene anawapanga kuti aziwapembedza.
לָבוֹא֙ בְּנִקְר֣וֹת הַצֻּרִ֔ים וּבִסְעִפֵ֖י הַסְּלָעִ֑ים מִפְּנֵ֞י פַּ֤חַד יְהוָה֙ וּמֵהֲדַ֣ר גְּאוֹנ֔וֹ בְּקוּמ֖וֹ לַעֲרֹ֥ץ הָאָֽרֶץ׃ | 21 |
Adzathawira mʼmapanga a matanthwe ndiponso mʼmingʼalu ya nthaka kuthawa mkwiyo wa Yehova ndiponso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
חִדְל֤וּ לָכֶם֙ מִן־הָ֣אָדָ֔ם אֲשֶׁ֥ר נְשָׁמָ֖ה בְּאַפּ֑וֹ כִּֽי־בַמֶּ֥ה נֶחְשָׁ֖ב הֽוּא׃ פ | 22 |
Lekani kudalira munthu, amene moyo wake sukhalira kutha. Iye angathandize bwanji wina aliyense?