< תהילים 97 >
יְהוָה מָלָךְ תָּגֵל הָאָרֶץ יִשְׂמְחוּ אִיִּים רַבִּֽים׃ | 1 |
Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale; magombe akutali akondwere.
עָנָן וַעֲרָפֶל סְבִיבָיו צֶדֶק וּמִשְׁפָּט מְכוֹן כִּסְאֽוֹ׃ | 2 |
Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira; chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.
אֵשׁ לְפָנָיו תֵּלֵךְ וּתְלַהֵט סָבִיב צָרָֽיו׃ | 3 |
Moto umapita patsogolo pake ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.
הֵאִירוּ בְרָקָיו תֵּבֵל רָאֲתָה וַתָּחֵל הָאָֽרֶץ׃ | 4 |
Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse; dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.
הָרִים כַּדּוֹנַג נָמַסּוּ מִלִּפְנֵי יְהוָה מִלִּפְנֵי אֲדוֹן כָּל־הָאָֽרֶץ׃ | 5 |
Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova, pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.
הִגִּידוּ הַשָּׁמַיִם צִדְקוֹ וְרָאוּ כָל־הָעַמִּים כְּבוֹדֽוֹ׃ | 6 |
Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake, ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.
יֵבֹשׁוּ ׀ כָּל־עֹבְדֵי פֶסֶל הַמִּֽתְהַלְלִים בָּאֱלִילִים הִשְׁתַּחֲווּ־לוֹ כָּל־אֱלֹהִֽים׃ | 7 |
Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi, iwo amene amanyadira mafano; mulambireni, inu milungu yonse!
שָׁמְעָה וַתִּשְׂמַח ׀ צִיּוֹן וַתָּגֵלְנָה בְּנוֹת יְהוּדָה לְמַעַן מִשְׁפָּטֶיךָ יְהוָֽה׃ | 8 |
Ziyoni akumva ndipo akukondwera, midzi ya Yuda ikusangalala chifukwa cha maweruzo anu Yehova.
כִּֽי־אַתָּה יְהוָה עֶלְיוֹן עַל־כָּל־הָאָרֶץ מְאֹד נַעֲלֵיתָ עַל־כָּל־אֱלֹהִֽים׃ | 9 |
Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi; ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.
אֹהֲבֵי יְהוָה שִׂנְאוּ רָע שֹׁמֵר נַפְשׁוֹת חֲסִידָיו מִיַּד רְשָׁעִים יַצִּילֵֽם׃ | 10 |
Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
אוֹר זָרֻעַ לַצַּדִּיק וּֽלְיִשְׁרֵי־לֵב שִׂמְחָֽה׃ | 11 |
Kuwala kumafika pa anthu olungama, ndi chimwemwe kwa olungama mtima.
שִׂמְחוּ צַדִּיקִים בַּֽיהוָה וְהוֹדוּ לְזֵכֶר קָדְשֽׁוֹ׃ | 12 |
Kondwerani mwa Yehova Inu olungama ndipo tamandani dzina lake loyera.