< תהילים 135 >

הַלְלוּ יָהּ ׀ הַֽלְלוּ אֶת־שֵׁם יְהוָה הֽ͏ַלְלוּ עַבְדֵי יְהוָֽה׃ 1
Tamandani Yehova. Tamandani dzina la Yehova; mutamandeni, inu atumiki a Yehova,
שֶׁעֹֽמְדִים בְּבֵית יְהוָה בְּחַצְרוֹת בֵּית אֱלֹהֵֽינוּ׃ 2
amene mumatumikira mʼnyumba ya Yehova, mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.
הַֽלְלוּ־יָהּ כִּי־טוֹב יְהוָה זַמְּרוּ לִשְׁמוֹ כִּי נָעִֽים׃ 3
Tamandani Yehova, pakuti Yehova ndi wabwino; imbani nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nʼkokoma kutero,
כִּֽי־יַעֲקֹב בָּחַר לוֹ יָהּ יִשְׂרָאֵל לִסְגֻלָּתֽוֹ׃ 4
Pakuti Yehova wasankha Yakobo kuti akhale wake, Israeli kuti akhale chuma chake chapamtima.
כִּי אֲנִי יָדַעְתִּי כִּי־גָדוֹל יְהוָה וַאֲדֹנֵינוּ מִכָּל־אֱלֹהִֽים׃ 5
Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu, kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.
כֹּל אֲשֶׁר־חָפֵץ יְהוָה עָשָׂה בַּשָּׁמַיִם וּבָאָרֶץ בַּיַּמִּים וְכָל־תְּהוֹמֽוֹת׃ 6
Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera, kumwamba ndi dziko lapansi, ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.
מַֽעֲלֶה נְשִׂאִים מִקְצֵה הָאָרֶץ בְּרָקִים לַמָּטָר עָשָׂה מֽוֹצֵא־רוּחַ מֵאֽוֹצְרוֹתָֽיו׃ 7
Iye amatulutsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, amatumiza zingʼaningʼani pamodzi ndi mvula ndipo amatulutsa mphepo ku malo ake osungiramo.
שֶֽׁהִכָּה בְּכוֹרֵי מִצְרָיִם מֵאָדָם עַד־בְּהֵמָֽה׃ 8
Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto, ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.
שָׁלַח ׀ אֹתוֹת וּמֹפְתִים בְּתוֹכֵכִי מִצְרָיִם בְּפַרְעֹה וּבְכָל־עֲבָדָֽיו׃ 9
Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto, kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.
שֶֽׁהִכָּה גּוֹיִם רַבִּים וְהָרַג מְלָכִים עֲצוּמִֽים׃ 10
Iye anakantha mitundu yambiri ya anthu ndi kupha mafumu amphamvu:
לְסִיחוֹן ׀ מֶלֶךְ הָאֱמֹרִי וּלְעוֹג מֶלֶךְ הַבָּשָׁן וּלְכֹל מַמְלְכוֹת כְּנָֽעַן׃ 11
Sihoni mfumu ya Aamori, Ogi mfumu ya Basani, ndi maufumu onse a ku Kanaani;
וְנָתַן אַרְצָם נַחֲלָה נַחֲלָה לְיִשְׂרָאֵל עַמּֽוֹ׃ 12
ndipo anapereka dziko lawo ngati cholowa, cholowa cha anthu ake Aisraeli.
יְהוָה שִׁמְךָ לְעוֹלָם יְהוָה זִכְרְךָ לְדֹר־וָדֹֽר׃ 13
Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya, mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.
כִּֽי־יָדִין יְהוָה עַמּוֹ וְעַל־עֲבָדָיו יִתְנֶחָֽם׃ 14
Pakuti Yehova adzaonetsa kuti anthu ake ngosalakwa, ndipo adzachitira chifundo atumiki ake.
עֲצַבֵּי הַגּוֹיִם כֶּסֶף וְזָהָב מַעֲשֵׂה יְדֵי אָדָֽם׃ 15
Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu.
פֶּֽה־לָהֶם וְלֹא יְדַבֵּרוּ עֵינַיִם לָהֶם וְלֹא יִרְאֽוּ׃ 16
Pakamwa ali napo koma sayankhula maso ali nawo, koma sapenya;
אָזְנַיִם לָהֶם וְלֹא יַאֲזִינוּ אַף אֵין־יֶשׁ־רוּחַ בְּפִיהֶֽם׃ 17
makutu ali nawo, koma sakumva ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse.
כְּמוֹהֶם יִהְיוּ עֹשֵׂיהֶם כֹּל אֲשֶׁר־בֹּטֵחַ בָּהֶֽם׃ 18
Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo, chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.
בֵּית יִשְׂרָאֵל בָּרֲכוּ אֶת־יְהוָה בֵּית אַהֲרֹן בָּרֲכוּ אֶת־יְהוָֽה׃ 19
Inu nyumba ya Israeli, tamandani Yehova; inu nyumba ya Aaroni, tamandani Yehova;
בֵּית הַלֵּוִי בָּרֲכוּ אֶת־יְהוָה יִֽרְאֵי יְהוָה בָּרֲכוּ אֶת־יְהוָֽה׃ 20
Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova; Inu amene mumaopa Iye, tamandani Yehova.
בָּרוּךְ יְהוָה ׀ מִצִיּוֹן שֹׁכֵן יְֽרוּשָׁלִָם הַֽלְלוּ־יָֽהּ׃ 21
Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni, amene amakhala mu Yerusalemu. Tamandani Yehova.

< תהילים 135 >