< מִשְׁלֵי 6 >
בְּנִי אִם־עָרַבְתָּ לְרֵעֶךָ תָּקַעְתָּ לַזָּר כַּפֶּֽיךָ׃ | 1 |
Mwana wanga, ngati wamuperekera mnansi wako chikole, ngati walonjeza kumulipirira mlendo,
נוֹקַשְׁתָּ בְאִמְרֵי־פִיךָ נִלְכַּדְתָּ בְּאִמְרֵי־פִֽיךָ׃ | 2 |
ngati wagwidwa ndi zimene iwe unanena, wakodwa ndi mawu a mʼkamwa mwako.
עֲשֵׂה זֹאת אֵפוֹא ׀ בְּנִי וְֽהִנָּצֵל כִּי בָאתָ בְכַף־רֵעֶךָ לֵךְ הִתְרַפֵּס וּרְהַב רֵעֶֽיךָ׃ | 3 |
Tsono popeza iwe mwana wanga wadziponya mʼmanja mwa mnansi wako, chita izi kuti udzipulumutse: pita msanga ukamupemphe mnansi wako; kuti akumasule!
אַל־תִּתֵּן שֵׁנָה לְעֵינֶיךָ וּתְנוּמָה לְעַפְעַפֶּֽיךָ׃ | 4 |
Usagone tulo, usawodzere.
הִנָּצֵל כִּצְבִי מִיָּד וּכְצִפּוֹר מִיַּד יָקֽוּשׁ׃ | 5 |
Dzipulumutse monga imachitira mphoyo mʼdzanja la mlenje, ndi monga imachitira mbalame mu msampha wa munthu wosaka.
לֵֽךְ־אֶל־נְמָלָה עָצֵל רְאֵה דְרָכֶיהָ וַחֲכָֽם׃ | 6 |
Pita kwa nyerere, mlesi iwe; kaonetsetse njira zake kuti uphunzirepo kanthu!
אֲשֶׁר אֵֽין־לָהּ קָצִין שֹׁטֵר וּמֹשֵֽׁל׃ | 7 |
Zilibe mfumu, zilibe woyangʼanira kapena wolamulira,
תָּכִין בַּקַּיִץ לַחְמָהּ אָגְרָה בַקָּצִיר מַאֲכָלָֽהּ׃ | 8 |
komabe zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe ndipo zimatuta chakudyacho nthawi yokolola.
עַד־מָתַי עָצֵל ׀ תִּשְׁכָּב מָתַי תָּקוּם מִשְּׁנָתֶֽךָ׃ | 9 |
Kodi uzingogonabe pamenepo mpaka liti mlesi iwe? Kodi tulo tako tidzatha liti?
מְעַט שֵׁנוֹת מְעַט תְּנוּמוֹת מְעַט ׀ חִבֻּק יָדַיִם לִשְׁכָּֽב׃ | 10 |
Ukati ndingogona pangʼono, ndingowodzera pangʼono ndingopinda manjawa pangʼono kuti ndipumule,
וּבָֽא־כִמְהַלֵּךְ רֵאשֶׁךָ וּמַחְסֹֽרְךָ כְּאִישׁ מָגֵֽן׃ | 11 |
umphawi udzakugwira ngati mbala ndipo usiwa udzafika ngati munthu wachifwamba.
אָדָם בְּלִיַּעַל אִישׁ אָוֶן הוֹלֵךְ עִקְּשׁוּת פֶּֽה׃ | 12 |
Munthu wachabechabe, munthu woyipa, amangoyendayenda ndi kumayankhula zoyipa,
קֹרֵץ בְּעֵינָו מֹלֵל בְּרַגְלָו מֹרֶה בְּאֶצְבְּעֹתָֽיו׃ | 13 |
amatsinzinira maso ake, namakwakwaza mapazi ake ndi kulozaloza ndi zala zake,
תַּֽהְפֻּכוֹת ׀ בְּלִבּוֹ חֹרֵשׁ רָע בְּכָל־עֵת מדנים מִדְיָנִים יְשַׁלֵּֽחַ׃ | 14 |
amalingalira zoyipa ndi mtima wake wachinyengo ndipo nthawi zonse amangokhalira kuyambitsa mikangano pakati pa anthu.
עַל־כֵּן פִּתְאֹם יָבוֹא אֵידוֹ פֶּתַע יִשָּׁבֵר וְאֵין מַרְפֵּֽא׃ | 15 |
Nʼchifukwa chake tsoka lidzamugwera modzidzimutsa; adzawonongeka msangamsanga popanda chomupulumutsa.
שֶׁשׁ־הֵנָּה שָׂנֵא יְהוָה וְשֶׁבַע תועבות תּוֹעֲבַת נַפְשֽׁוֹ׃ | 16 |
Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo, zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa:
עֵינַיִם רָמוֹת לְשׁוֹן שָׁקֶר וְיָדַיִם שֹׁפְכוֹת דָּם־נָקִֽי׃ | 17 |
maso onyada, pakamwa pabodza, manja akupha munthu wosalakwa,
לֵב חֹרֵשׁ מַחְשְׁבוֹת אָוֶן רַגְלַיִם מְמַהֲרוֹת לָרוּץ לָֽרָעָה׃ | 18 |
mtima wokonzekera kuchita zoyipa, mapazi othamangira msanga ku zoyipa,
יָפִיחַ כְּזָבִים עֵד שָׁקֶר וּמְשַׁלֵּחַ מְדָנִים בֵּין אַחִֽים׃ | 19 |
mboni yonama yoyankhula mabodza komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.
נְצֹר בְּנִי מִצְוַת אָבִיךָ וְאַל־תִּטֹּשׁ תּוֹרַת אִמֶּֽךָ׃ | 20 |
Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako; ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.
קָשְׁרֵם עַל־לִבְּךָ תָמִיד עָנְדֵם עַל־גַּרְגְּרֹתֶֽךָ׃ | 21 |
Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse, uzimangirire mʼkhosi mwako.
בְּהִתְהַלֶּכְךָ ׀ תַּנְחֶה אֹתָךְ בְּֽשָׁכְבְּךָ תִּשְׁמֹר עָלֶיךָ וַהֲקִיצוֹתָ הִיא תְשִׂיחֶֽךָ׃ | 22 |
Ukamayenda, zidzakulozera njira; ukugona, zidzakulondera; ukudzuka, zidzakuyankhula.
כִּי נֵר מִצְוָה וְתוֹרָה אוֹר וְדֶרֶךְ חַיִּים תּוֹכְחוֹת מוּסָֽר׃ | 23 |
Paja malamulo awa ali ngati nyale, malangizowa ali ngati kuwunika, ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo moyo weniweni,
לִשְׁמָרְךָ מֵאֵשֶׁת רָע מֵֽחֶלְקַת לָשׁוֹן נָכְרִיָּֽה׃ | 24 |
kukupulumutsa kwa mkazi wadama, zimenezi zidzakutchinjiriza kwa mkazi wadama, ndi kukuthandiza kuti usamvere mawu oshashalika a mkazi wachiwerewere.
אַל־תַּחְמֹד יָפְיָהּ בִּלְבָבֶךָ וְאַל־תִּקָּֽחֲךָ בְּעַפְעַפֶּֽיהָ׃ | 25 |
Mu mtima wako usakhumbire kukongola kwake, asakukope ndi zikope zake,
כִּי בְעַד־אִשָּׁה זוֹנָה עַֽד־כִּכַּר לָחֶם וְאֵשֶׁת אִישׁ נֶפֶשׁ יְקָרָה תָצֽוּד׃ | 26 |
paja mkazi wadama amakusandutsa kukhala ngati nyenyeswa za buledi ndipo mkazi wa mwini wake amasokonezeratu moyo wako wonse.
הֲיַחְתֶּה אִישׁ אֵשׁ בְּחֵיקוֹ וּבְגָדָיו לֹא תִשָּׂרַֽפְנָה׃ | 27 |
Kodi munthu angathe kutenga moto zovala zake osapsa?
אִם־יְהַלֵּךְ אִישׁ עַל־הַגֶּחָלִים וְרַגְלָיו לֹא תִכָּוֶֽינָה׃ | 28 |
Kodi munthu angathe kuyenda pa makala amoto mapazi ake osapserera?
כֵּן הַבָּא אֶל־אֵשֶׁת רֵעֵהוּ לֹא יִנָּקֶה כָּֽל־הַנֹּגֵעַ בָּֽהּ׃ | 29 |
Ndizo zimachitikira munthu amene amagonana ndi mkazi wa munthu wina. Aliyense wokhudza mkazi wotere adzalangidwa.
לֹא־יָבוּזוּ לַגַּנָּב כִּי יִגְנוֹב לְמַלֵּא נַפְשׁוֹ כִּי יִרְעָֽב׃ | 30 |
Paja anthu sayinyoza mbala ikaba chifukwa chakuti ili ndi njala.
וְנִמְצָא יְשַׁלֵּם שִׁבְעָתָיִם אֶת־כָּל־הוֹן בֵּיתוֹ יִתֵּֽן׃ | 31 |
Komabe ngati mbalayo igwidwa iyenera kulipira kasanu nʼkawiri, ngakhale kulandidwa katundu wa mʼnyumba mwake.
נֹאֵף אִשָּׁה חֲסַר־לֵב מַֽשְׁחִית נַפְשׁוֹ הוּא יַעֲשֶֽׂנָּה׃ | 32 |
Munthu wochita chigololo ndi wopanda nzeru. Wochita zimenezi amangodziwononga yekha.
נֶֽגַע־וְקָלוֹן יִמְצָא וְחֶרְפָּתוֹ לֹא תִמָּחֶֽה׃ | 33 |
Adzalandira mabala ndi mʼnyozo, ndipo manyazi ake sadzamuchokera.
כִּֽי־קִנְאָה חֲמַת־גָּבֶר וְלֹֽא־יַחְמוֹל בְּיוֹם נָקָֽם׃ | 34 |
Paja nsanje imachititsa mwini mkaziyo kukalipa, ndipo sadzachita chifundo pobwezera.
לֹא־יִשָּׂא פְּנֵי כָל־כֹּפֶר וְלֹֽא־יֹאבֶה כִּי תַרְבֶּה־שֹֽׁחַד׃ | 35 |
Iye savomera dipo lililonse; sangapepeseke ngakhale umupatse mphatso zochuluka motani.