< מִשְׁלֵי 20 >
לֵץ הַיַּין הֹמֶה שֵׁכָר וְכָל־שֹׁגֶה בּוֹ לֹא יֶחְכָּֽם׃ | 1 |
Vinyo amachititsa munthu kukhala wonyoza ndipo chakumwa choledzeretsa chimachititsa munthu kukhala wolongolola; aliyense wosochera nazo zimenezi alibe nzeru.
נַהַם כַּכְּפִיר אֵימַת מֶלֶךְ מִתְעַבְּרוֹ חוֹטֵא נַפְשֽׁוֹ׃ | 2 |
Ukali wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango; amene amawuputa mkwiyowo amataya moyo wake.
כָּבוֹד לָאִישׁ שֶׁבֶת מֵרִיב וְכָל־אֱוִיל יִתְגַּלָּֽע׃ | 3 |
Nʼchaulemu kwa munthu kupewa mikangano, koma chitsiru chilichonse chimafulumira kulongolola.
מֵחֹרֶף עָצֵל לֹא־יַחֲרֹשׁ ישאל וְשָׁאַל בַּקָּצִיר וָאָֽיִן׃ | 4 |
Munthu waulesi satipula mʼmunda pa nthawi yoyenera; kotero pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzapeza kanthu kalikonse.
מַיִם עֲמֻקִּים עֵצָה בְלֶב־אִישׁ וְאִישׁ תְּבוּנָה יִדְלֶֽנָּה׃ | 5 |
Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi akuya, munthu womvetsa zinthu ndiye yekha angawatunge.
רָב־אָדָם יִקְרָא אִישׁ חַסְדּוֹ וְאִישׁ אֱמוּנִים מִי יִמְצָֽא׃ | 6 |
Anthu ambiri amayankhula za kukhulupirika kwawo, koma munthu wokhulupirika angamupeze ndani?
מִתְהַלֵּךְ בְּתֻמּוֹ צַדִּיק אַשְׁרֵי בָנָיו אַחֲרָֽיו׃ | 7 |
Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino; odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.
מֶלֶךְ יוֹשֵׁב עַל־כִּסֵּא־דִין מְזָרֶה בְעֵינָיו כָּל־רָֽע׃ | 8 |
Mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo, imapeta ndi maso ake anthu onse oyipa.
מִֽי־יֹאמַר זִכִּיתִי לִבִּי טָהַרְתִּי מֵחַטָּאתִֽי׃ | 9 |
Ndani amene anganene kuti, “Ndawuyeretsa mtima wanga; ndilibe tchimo lililonse?”
אֶבֶן וָאֶבֶן אֵיפָה וְאֵיפָה תּוֹעֲבַת יְהוָה גַּם־שְׁנֵיהֶֽם׃ | 10 |
Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengo zonsezi Yehova zimamunyansa.
גַּם בְּמַעֲלָלָיו יִתְנַכֶּר־נָעַר אִם־זַךְ וְאִם־יָשָׁר פָּעֳלֽוֹ׃ | 11 |
Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake, ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera.
אֹזֶן שֹׁמַעַת וְעַיִן רֹאָה יְהוָה עָשָׂה גַם־שְׁנֵיהֶֽם׃ | 12 |
Makutu amene amamva ndi maso amene amaona, zonsezi anazilenga ndi Yehova.
אַל־תֶּֽאֱהַב שֵׁנָה פֶּן־תִּוָּרֵשׁ פְּקַח עֵינֶיךָ שְֽׂבַֽע־לָֽחֶם׃ | 13 |
Usakonde tulo ungasauke; khala maso ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.
רַע רַע יֹאמַר הַקּוֹנֶה וְאֹזֵל לוֹ אָז יִתְהַלָּֽל׃ | 14 |
Munthu wogula chinthu amati, “Sichabwino, sichabwino.” Koma akagula nʼkuchokapo amayamba kudzitama.
יֵשׁ זָהָב וְרָב־פְּנִינִים וּכְלִי יְקָר שִׂפְתֵי־דָֽעַת׃ | 15 |
Pali golide ndi miyala yamtengowapatali, koma milomo yoyankhula zanzeru ndi yamtengowapatali koposa zonsezi.
לְֽקַח־בִּגְדוֹ כִּי־עָרַב זָר וּבְעַד נכרים נָכְרִיָּה חַבְלֵֽהוּ׃ | 16 |
Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole; kuti chikhale chikole chako chifukwa waperekera chikole munthu wachilendo.
עָרֵב לָאִישׁ לֶחֶם שָׁקֶר וְאַחַר יִמָּֽלֵא־פִיהוּ חָצָֽץ׃ | 17 |
Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu, koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake.
מַחֲשָׁבוֹת בְּעֵצָה תִכּוֹן וּבְתַחְבֻּלוֹת עֲשֵׂה מִלְחָמָֽה׃ | 18 |
Zokonzekera zimapindula utafunsira uphungu; ndipo usanamenye nkhondo yamba wapempha malangizo oyenera.
גּֽוֹלֶה־סּוֹד הוֹלֵךְ רָכִיל וּלְפֹתֶה שְׂפָתָיו לֹא תִתְעָרָֽב׃ | 19 |
Amene amanka nanena miseche amawulula zachinsinsi. Choncho usamagwirizane naye munthu woyankhula zopusayo.
מְקַלֵּל אָבִיו וְאִמּוֹ יִֽדְעַךְ נֵרוֹ באישון בֶּאֱשׁוּן חֹֽשֶׁךְ׃ | 20 |
Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake, moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani.
נַחֲלָה מבחלת מְבֹהֶלֶת בָּרִאשֹׁנָה וְאַחֲרִיתָהּ לֹא תְבֹרָֽךְ׃ | 21 |
Cholowa chochipeza mofulumira poyamba, sichidzakhala dalitso pa mapeto pake.
אַל־תֹּאמַר אֲשַׁלְּמָה־רָע קַוֵּה לַֽיהוָה וְיֹשַֽׁע לָֽךְ׃ | 22 |
Usanene kuti, “Ine ndidzabwezera choyipa chimenechi!” Dikira Yehova, ndipo Iye adzakupulumutsa.
תּוֹעֲבַת יְהוָה אֶבֶן וָאָבֶן וּמֹאזְנֵי מִרְמָה לֹא־טֽוֹב׃ | 23 |
Miyeso yosintha imamunyansa Yehova; ndipo masikelo onyenga si abwino.
מֵיהוָה מִצְעֲדֵי־גָבֶר וְאָדָם מַה־יָּבִין דַּרְכּֽוֹ׃ | 24 |
Mayendedwe a munthu amawalamulira ndi Yehova, tsono munthu angadziwe bwanji njira yake?
מוֹקֵשׁ אָדָם יָלַע קֹדֶשׁ וְאַחַר נְדָרִים לְבַקֵּֽר׃ | 25 |
Ndi msampha kwa munthu kuyankhula mofulumira kuti “Chinthu ichi nʼchopatulika kwa Yehova,” popeza mwina atha kusintha maganizo utalumbira kale.
מְזָרֶה רְשָׁעִים מֶלֶךְ חָכָם וַיָּשֶׁב עֲלֵיהֶם אוֹפָֽן׃ | 26 |
Mfumu ya nzeru imapeta kwathunthu anthu oyipa.
נֵר יְהוָה נִשְׁמַת אָדָם חֹפֵשׂ כָּל־חַדְרֵי־בָֽטֶן׃ | 27 |
Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Yehova; imafufuza ziwalo zake zonse zamʼkati.
חֶסֶד וֶאֱמֶת יִצְּרוּ־מֶלֶךְ וְסָעַד בַּחֶסֶד כִּסְאֽוֹ׃ | 28 |
Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu; chilungamo chimalimbikitsa mpando wake waufumu.
תִּפְאֶרֶת בַּחוּרִים כֹּחָם וַהֲדַר זְקֵנִים שֵׂיבָֽה׃ | 29 |
Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo, imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba.
חַבֻּרוֹת פֶּצַע תמריק תַּמְרוּק בְּרָע וּמַכּוֹת חַדְרֵי־בָֽטֶן׃ | 30 |
Mikwingwirima yopweteka ndiyo imachotsa zoyipa, ndipo mikwapulo ndiyo imachotsa zamʼkatikati mwa munthu.