< איכה 4 >

אֵיכָה יוּעַם זָהָב יִשְׁנֶא הַכֶּתֶם הַטּוֹב תִּשְׁתַּפֵּכְנָה אַבְנֵי־קֹדֶשׁ בְּרֹאשׁ כָּל־חוּצֽוֹת׃ 1
Haa! Golide wathimbirira, golide wosalala wasinthikiratu! Amwazamwaza miyala yokongola ya kumalo opatulika pamphambano ponse pa mzinda.
בְּנֵי צִיּוֹן הַיְקָרִים הַמְסֻלָּאִים בַּפָּז אֵיכָה נֶחְשְׁבוּ לְנִבְלֵי־חֶרֶשׂ מַעֲשֵׂה יְדֵי יוֹצֵֽר׃ 2
Haa! Ana a Ziyoni amtengowapatali amene kale anali ngati golide, tsopano ali ngati miphika ya dothi, ntchito ya owumba mbiya!
גַּם־תנין תַּנִּים חָלְצוּ שַׁד הֵינִיקוּ גּוּרֵיהֶן בַּת־עַמִּי לְאַכְזָר כי ענים כַּיְעֵנִים בַּמִּדְבָּֽר׃ 3
Ngakhale nkhandwe zimapereka bere kuyamwitsa ana ake, koma anthu anga asanduka ankhanza ngati nthiwatiwa mʼchipululu.
דָּבַק לְשׁוֹן יוֹנֵק אֶל־חִכּוֹ בַּצָּמָא עֽוֹלָלִים שָׁאֲלוּ לֶחֶם פֹּרֵשׂ אֵין לָהֶֽם׃ 4
Lilime la mwana lakangamira kukhosi chifukwa cha ludzu, ana akupempha chakudya, koma palibe amene akuwapatsa.
הָאֹֽכְלִים לְמַעֲדַנִּים נָשַׁמּוּ בַּחוּצוֹת הָאֱמֻנִים עֲלֵי תוֹלָע חִבְּקוּ אַשְׁפַּתּֽוֹת׃ 5
Iwo amene kale ankadya zonona akupemphetsa mʼmisewu ya mu mzinda. Iwo amene kale ankavala zokongola tsopano akugona pa phulusa.
וַיִּגְדַּל עֲוֺן בַּת־עַמִּי מֵֽחַטַּאת סְדֹם הַֽהֲפוּכָה כְמוֹ־רָגַע וְלֹא־חָלוּ בָהּ יָדָֽיִם׃ 6
Kuyipa kwa anthu anga kunali kwakukulu kuposa anthu a ku Sodomu, amene anawonongedwa mʼkamphindi kochepa popanda owathandiza.
זַכּוּ נְזִירֶיהָ מִשֶּׁלֶג צַחוּ מֵחָלָב אָדְמוּ עֶצֶם מִפְּנִינִים סַפִּיר גִּזְרָתָֽם׃ 7
Akalonga ake anali owala koposa chisanu chowundana ndi oyera kuposa mkaka. Matupi awo anali ofiira kuposa miyala ya rubi, maonekedwe awo ngati miyala ya safiro.
חָשַׁךְ מִשְּׁחוֹר תָּֽאֳרָם לֹא נִכְּרוּ בַּחוּצוֹת צָפַד עוֹרָם עַל־עַצְמָם יָבֵשׁ הָיָה כָעֵֽץ׃ 8
Koma tsopano maonekedwe awo ndi akuda kuposa mwaye; palibe angawazindikire mʼmisewu ya mu mzinda. Khungu lawo lachita makwinyamakwinya pa mafupa awo; lawuma gwaa ngati nkhuni.
טוֹבִים הָיוּ חַלְלֵי־חֶרֶב מֵֽחַלְלֵי רָעָב שֶׁהֵם יָזוּבוּ מְדֻקָּרִים מִתְּנוּבֹת שָׂדָֽי׃ 9
Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kuposa amene anafa ndi njala; chifukwa chosowa chakudya cha mʼmunda iwowa ankafowoka ndi njala mpaka kufa.
יְדֵי נָשִׁים רַחֲמָנִיּוֹת בִּשְּׁלוּ יַלְדֵיהֶן הָיוּ לְבָרוֹת לָמוֹ בְּשֶׁבֶר בַּת־עַמִּֽי׃ 10
Amayi achifundo afika pophika ana awo enieni, ndiwo anali chakudya chawo pamene anthu anga anali kuwonongeka.
כִּלָּה יְהוָה אֶת־חֲמָתוֹ שָׁפַךְ חֲרוֹן אַפּוֹ וַיַּצֶּת־אֵשׁ בְּצִיּוֹן וַתֹּאכַל יְסוֹדֹתֶֽיהָ׃ 11
Yehova wakwaniritsa ukali wake; wagwetsa pansi mkwiyo wake woopsa. Ndipo wayatsa moto mʼZiyoni kuti uwononge maziko ake.
לֹא הֶאֱמִינוּ מַלְכֵי־אֶרֶץ וכל כֹּל יֹשְׁבֵי תֵבֵל כִּי יָבֹא צַר וְאוֹיֵב בְּשַׁעֲרֵי יְרוּשָׁלָֽ͏ִם׃ 12
Mafumu a pa dziko lapansi sanakhulupirire, kapena wina aliyense wokhala pa dziko lonse, kuti adani kapena ankhondo akhoza kulowa pa zipata za Yerusalemu.
מֵֽחַטֹּאת נְבִיאֶיהָ עֲוֺנוֹת כֹּהֲנֶיהָ הַשֹּׁפְכִים בְּקִרְבָּהּ דַּם צַדִּיקִֽים׃ 13
Koma izi zinachitika chifukwa cha kuchimwa kwa aneneri ake ndi mphulupulu za ansembe ake, amene ankapha anthu osalakwa pakati pawo.
נָעוּ עִוְרִים בַּֽחוּצוֹת נְגֹֽאֲלוּ בַּדָּם בְּלֹא יֽוּכְלוּ יִגְּעוּ בִּלְבֻשֵׁיהֶֽם׃ 14
Tsopano akungoyendayenda mʼmisewu ya mu mzinda ngati anthu osaona. Iwo ndi odetsedwa kwambiri ndi magazi palibe yemwe angayerekeze nʼkukhudza komwe chovala chawo.
סוּרוּ טָמֵא קָרְאוּ לָמוֹ סוּרוּ סוּרוּ אַל־תִּגָּעוּ כִּי נָצוּ גַּם־נָעוּ אָֽמְרוּ בַּגּוֹיִם לֹא יוֹסִיפוּ לָגֽוּר׃ 15
Anthu akuwafuwulira kuti, “Chokani! Inu anthu odetsedwa!” “Chokani! Chokani! Musatikhudze ife!” Akamathawa ndi kumangoyendayenda, pakati pa anthu a mitundu yonse amati, “Asakhalenso ndi ife.”
פְּנֵי יְהוָה חִלְּקָם לֹא יוֹסִיף לְהַבִּיטָם פְּנֵי כֹהֲנִים לֹא נָשָׂאוּ זקנים וּזְקֵנִים לֹא חָנָֽנוּ׃ 16
Yehova mwini wake wawabalalitsa; Iye sakuwalabadiranso. Ansembe sakulandira ulemu, akuluakulu sakuwachitira chifundo.
עודינה עוֹדֵינוּ תִּכְלֶינָה עֵינֵינוּ אֶל־עֶזְרָתֵנוּ הָבֶל בְּצִפִּיָּתֵנוּ צִפִּינוּ אֶל־גּוֹי לֹא יוֹשִֽׁעַ׃ 17
Ndiponso maso athu atopa nʼkuyangʼana, chithandizo chosabwera nʼkomwe, kuchokera pa nsanja zathu tinadikirira mtundu wa anthu umene sukanatipulumutsa.
צָדוּ צְעָדֵינוּ מִלֶּכֶת בִּרְחֹבֹתֵינוּ קָרַב קִצֵּינוּ מָלְאוּ יָמֵינוּ כִּי־בָא קִצֵּֽינוּ׃ 18
Anthu ankalondola mapazi athu, choncho sitikanayenda mʼmisewu yathu mu mzinda. Chimaliziro chathu chinali pafupi, masiku athu anali owerengeka, chifukwa chimaliziro chathu chinali chitafika.
קַלִּים הָיוּ רֹדְפֵינוּ מִנִּשְׁרֵי שָׁמָיִם עַל־הֶהָרִים דְּלָקֻנוּ בַּמִּדְבָּר אָרְבוּ לָֽנוּ׃ 19
Otilondola akuthamanga kwambiri kuposa ziwombankhanga mu mlengalenga; anatithamangitsa mpaka ku mapiri ndi kutibisalira mʼchipululu.
רוּחַ אַפֵּינוּ מְשִׁיחַ יְהוָה נִלְכַּד בִּשְׁחִיתוֹתָם אֲשֶׁר אָמַרְנוּ בְּצִלּוֹ נִֽחְיֶה בַגּוֹיִֽם׃ 20
Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo, anakodwa mʼmisampha yawo. Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wake pakati pa mitundu ya anthu.
שִׂישִׂי וְשִׂמְחִי בַּת־אֱדוֹם יושבתי יוֹשֶׁבֶת בְּאֶרֶץ עוּץ גַּם־עָלַיִךְ תַּעֲבָר־כּוֹס תִּשְׁכְּרִי וְתִתְעָרִֽי׃ 21
Kondwera ndi kusangalala, mwana wamkazi wa Edomu. Iwe amene umakhala mʼdziko la Uzi. Koma iwenso chikho chidzakupeza; udzaledzera mpaka kukhala maliseche.
תַּם־עֲוֺנֵךְ בַּת־צִיּוֹן לֹא יוֹסִיף לְהַגְלוֹתֵךְ פָּקַד עֲוֺנֵךְ בַּת־אֱדוֹם גִּלָּה עַל־חַטֹּאתָֽיִךְ׃ 22
Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chako chidzatha; Iye sadzatalikitsa nthawi yako ya ukapolo. Koma Yehova adzalanga machimo ako, iwe mwana wamkazi wa Edomu, ndi kuyika poyera mphulupulu zako.

< איכה 4 >