< איוב 21 >

וַיַּעַן אִיּוֹב וַיֹּאמַֽר׃ 1
Pamenepo Yobu anayankha kuti,
שִׁמְעוּ שָׁמוֹעַ מִלָּתִי וּתְהִי־זֹאת תַּנְחוּמֹֽתֵיכֶֽם׃ 2
“Mvetserani bwino mawu anga; ichi chikhale chitonthozo changa chochokera kwa inu.
שָׂאוּנִי וְאָנֹכִי אֲדַבֵּר וְאַחַר דַּבְּרִי תַלְעִֽיג׃ 3
Ndiloleni ndiyankhule ndipo ndikatha kuyankhula munditonzetonze.
הֶאָנֹכִי לְאָדָם שִׂיחִי וְאִם־מַדּוּעַ לֹא־תִקְצַר רוּחִֽי׃ 4
“Kodi ine ndikudandaulira munthu? Tsono ndilekerenji kupsa mtima?
פְּנוּ־אֵלַי וְהָשַׁמּוּ וְשִׂימוּ יָד עַל־פֶּֽה׃ 5
Ndipenyeni ndipo mudabwe; mugwire dzanja pakamwa.
וְאִם־זָכַרְתִּי וְנִבְהָלְתִּי וְאָחַז בְּשָׂרִי פַּלָּצֽוּת׃ 6
Ndikamaganiza zimenezi ndimachita mantha kwambiri; thupi langa limanjenjemera.
מַדּוּעַ רְשָׁעִים יִחְיוּ עָתְקוּ גַּם־גָּבְרוּ חָֽיִל׃ 7
Chifukwa chiyani anthu oyipa amakhalabe ndi moyo, amakalamba ndi kusanduka amphamvu?
זַרְעָם נָכוֹן לִפְנֵיהֶם עִמָּם וְצֶאֱצָאֵיהֶם לְעֵינֵיהֶֽם׃ 8
Amaona ana awo akukhazikika pamodzi nawo, zidzukulu zawo zikukula bwino iwo akuona.
בָּתֵּיהֶם שָׁלוֹם מִפָּחַד וְלֹא שֵׁבֶט אֱלוֹהַּ עֲלֵיהֶֽם׃ 9
Mabanja awo amakhala pa mtendere ndipo sakhala ndi mantha; mkwapulo wa Mulungu suwakhudza nʼkomwe.
שׁוֹרוֹ עִבַּר וְלֹא יַגְעִל תְּפַלֵּט פָּרָתוֹ וְלֹא תְשַׁכֵּֽל׃ 10
Ngʼombe zawo zazimuna sizilephera kubereketsa; ngʼombe zawo zazikazi sizipoloza.
יְשַׁלְּחוּ כַצֹּאן עֲוִילֵיהֶם וְיַלְדֵיהֶם יְרַקֵּדֽוּן׃ 11
Amatulutsa ana awo ngati gulu la nkhosa; makanda awo amavinavina pabwalo.
יִשְׂאוּ כְּתֹף וְכִנּוֹר וְיִשְׂמְחוּ לְקוֹל עוּגָֽב׃ 12
Amayimba nyimbo pogwiritsa ntchito matambolini ndi azeze; amakondwa pakumva kulira kwa chitoliro.
יבלו יְכַלּוּ בַטּוֹב יְמֵיהֶם וּבְרֶגַע שְׁאוֹל יֵחָֽתּוּ׃ (Sheol h7585) 13
Zaka zawo zimatha ali mu ulemerero ndipo amatsikira ku manda mwamtendere. (Sheol h7585)
וַיֹּאמְרוּ לָאֵל סוּר מִמֶּנּוּ וְדַעַת דְּרָכֶיךָ לֹא חָפָֽצְנוּ׃ 14
Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’ Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu.
מַה־שַׁדַּי כִּֽי־נַֽעַבְדֶנּוּ וּמַה־נּוֹעִיל כִּי נִפְגַּע־בּֽוֹ׃ 15
Kodi Wamphamvuzonseyo ndani kuti timutumikire? Ife tipindula chiyani tikamapemphera kwa Iyeyo?
הֵן לֹא בְיָדָם טוּבָם עֲצַת רְשָׁעִים רָחֲקָה מֶֽנִּי׃ 16
Komatu ulemerero wawo suli mʼmanja mwawo, koma ine ndimakhala patali ndi uphungu wa anthu oyipa.
כַּמָּה ׀ נֵר־רְשָׁעִים יִדְעָךְ וְיָבֹא עָלֵימוֹ אֵידָם חֲבָלִים יְחַלֵּק בְּאַפּֽוֹ׃ 17
“Koma nʼkangati kamene nyale ya anthu oyipa imazimitsidwa? Nʼkangati kamene tsoka limawagwera? Nʼkangati kamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga?
יִהְיוּ כְּתֶבֶן לִפְנֵי־רוּחַ וּכְמֹץ גְּנָבַתּוּ סוּפָֽה׃ 18
Nʼkangati kamene iwo amakhala ngati phesi lowuluka ndi mphepo, ngati mungu wowuluzika ndi kamvuluvulu?
אֱלוֹהַּ יִצְפֹּן־לְבָנָיו אוֹנוֹ יְשַׁלֵּם אֵלָיו וְיֵדָֽע׃ 19
Paja amati, ‘Mulungu amalanga ana chifukwa cha machimo abambo awo.’ Koma Mulungu amabwezera chilango munthuyo, kuti adziwe kuti Mulungu amalangadi.
יִרְאוּ עינו עֵינָיו כִּידוֹ וּמֵחֲמַת שַׁדַּי יִשְׁתֶּֽה׃ 20
Mulole kuti adzionere yekha chilango chake, kuti alawe ukali wa Wamphamvuzonse.
כִּי מַה־חֶפְצוֹ בְּבֵיתוֹ אַחֲרָיו וּמִסְפַּר חֳדָשָׁיו חֻצָּֽצוּ׃ 21
Nanga kodi amalabadira chiyani zabanja lake limene walisiya mʼmbuyo, pamene chiwerengero cha masiku ake chatha?
הַלְאֵל יְלַמֶּד־דָּעַת וְהוּא רָמִים יִשְׁפּֽוֹט׃ 22
“Kodi alipo wina amene angaphunzitse Mulungu nzeru, poti Iye amaweruza ngakhale anthu apamwamba?
זֶה יָמוּת בְּעֶצֶם תֻּמּוֹ כֻּלּוֹ שַׁלְאֲנַן וְשָׁלֵֽיו׃ 23
Munthu wina amamwalira ali ndi mphamvu zonse, ali pa mtendere ndi pa mpumulo,
עֲטִינָיו מָלְאוּ חָלָב וּמֹחַ עַצְמוֹתָיו יְשֻׁקֶּֽה׃ 24
thupi lake lili lonenepa, mafupa ake ali odzaza ndi mafuta.
וְזֶה יָמוּת בְּנֶפֶשׁ מָרָה וְלֹֽא־אָכַל בַּטּוֹבָֽה׃ 25
Munthu wina amamwalira ali wowawidwa mtima, wosalawapo chinthu chabwino chilichonse.
יַחַד עַל־עָפָר יִשְׁכָּבוּ וְרִמָּה תְּכַסֶּה עֲלֵיהֶֽם׃ 26
Olemera ndi osauka omwe amamwalira ndi kuyikidwa mʼmanda ndipo onse amatuluka mphutsi.
הֵן יָדַעְתִּי מַחְשְׁבֽוֹתֵיכֶם וּמְזִמּוֹת עָלַי תַּחְמֹֽסוּ׃ 27
“Ndikudziwa bwino zimene mukuganiza, ziwembu zanu zomwe mukuti mundichitire.
כִּי תֹֽאמְרוּ אַיֵּה בֵית־נָדִיב וְאַיֵּה אֹהֶל ׀ מִשְׁכְּנוֹת רְשָׁעִֽים׃ 28
Inu mukuti, ‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti, matenti amene munkakhala anthu oyipa aja ali kuti?’
הֲלֹא שְׁאֶלְתֶּם עוֹבְרֵי דָרֶךְ וְאֹתֹתָם לֹא תְנַכֵּֽרוּ׃ 29
Kodi munawafunsapo anthu amene ali pa ulendo? Kodi munaganizirapo zimene iwo amanena?
כִּי לְיוֹם אֵיד יֵחָשֶׂךְ רָע לְיוֹם עֲבָרוֹת יוּבָֽלוּ׃ 30
Zakuti munthu woyipa amasungidwa chifukwa cha tsiku la tsoka, kuti amapulumutsidwa chifukwa cha tsiku la ukali wa Mulungu?
מִֽי־יַגִּיד עַל־פָּנָיו דַּרְכּוֹ וְהֽוּא־עָשָׂה מִי יְשַׁלֶּם־לֽוֹ׃ 31
Kodi ndani amadzudzula munthu wochimwayo? Ndani amamubwezera zoyipa zimene anachita?
וְהוּא לִקְבָרוֹת יוּבָל וְֽעַל־גָּדִישׁ יִשְׁקֽוֹד׃ 32
Iye amanyamulidwa kupita ku manda ndipo anthu amachezera pa manda ake.
מָֽתְקוּ־לוֹ רִגְבֵי נָחַל וְאַחֲרָיו כָּל־אָדָם יִמְשׁוֹךְ וּלְפָנָיו אֵין מִסְפָּֽר׃ 33
Dothi la ku chigwa limamukomera; anthu onse amatsatira mtembo wake, ndipo anthu osawerengeka amakhala patsogolo pa chitanda chakecho.
וְאֵיךְ תְּנַחֲמוּנִי הָבֶל וּתְשֽׁוּבֹתֵיכֶם נִשְׁאַר־מָֽעַל׃ 34
“Nanga inu mudzanditonthoza bwanji ine ndi mawu anu opandapakewo palibe chimene chatsala kuti muyankhe koma mabodza basi!”

< איוב 21 >