< איוב 14 >
אָדָם יְלוּד אִשָּׁה קְצַר יָמִים וּֽשְׂבַֽע־רֹֽגֶז׃ | 1 |
“Munthu wobadwa mwa amayi amakhala masiku owerengeka ndipo ndi odzaza ndi mavuto okhaokha.
כְּצִיץ יָצָא וַיִּמָּל וַיִּבְרַח כַּצֵּל וְלֹא יַעֲמֽוֹד׃ | 2 |
Amaphuka ngati duwa ndipo kenaka amafota; amathawa ngati mthunzi ndipo sakhalitsa.
אַף־עַל־זֶה פָּקַחְתָּ עֵינֶךָ וְאֹתִי תָבִיא בְמִשְׁפָּט עִמָּֽךְ׃ | 3 |
Kodi munthu wotereyo nʼkumuyangʼanitsitsa? Kodi mungamubweretse pamaso panu kuti mumuzenge mlandu?
מִֽי־יִתֵּן טָהוֹר מִטָּמֵא לֹא אֶחָֽד׃ | 4 |
Ndani angatulutse chabwino mʼchoyipa? Palibe ndi mmodzi yemwe!
אִם חֲרוּצִים ׀ יָמָיו מִֽסְפַּר־חֳדָשָׁיו אִתָּךְ חקו חֻקָּיו עָשִׂיתָ וְלֹא יַעֲבֽוֹר׃ | 5 |
Masiku a munthu ndi odziwikiratu; munakhazikitsa chiwerengero cha miyezi yake ndipo munamulembera malire amene sangathe kuwalumpha.
שְׁעֵה מֵעָלָיו וְיֶחְדָּל עַד־יִרְצֶה כְּשָׂכִיר יוֹמֽוֹ׃ | 6 |
Choncho Inu mumufulatire ndipo mumuleke apumule kufikira atakondwera nawo moyo ngati munthu waganyu.
כִּי יֵשׁ לָעֵץ תִּקְוָה אִֽם־יִכָּרֵת וְעוֹד יַחֲלִיף וְיֹֽנַקְתּוֹ לֹא תֶחְדָּֽל׃ | 7 |
“Mtengo uli nacho chiyembekezo: ngati wadulidwa, udzaphukiranso ndipo nthambi zake sizidzaleka kuphukira.
אִם־יַזְקִין בָּאָרֶץ שָׁרְשׁוֹ וּבֶעָפָר יָמוּת גִּזְעֽוֹ׃ | 8 |
Mizu yake ingathe kukalamba mʼnthaka ndipo chitsa chake nʼkuwola pa dothi,
מֵרֵיחַ מַיִם יַפְרִחַ וְעָשָׂה קָצִיר כְּמוֹ־נָֽטַע׃ | 9 |
koma pamene chinyontho chafika udzaphukira ndipo udzaphuka nthambi ngati mtengo wanthete.
וְגֶבֶר יָמוּת וַֽיֶּחֱלָשׁ וַיִּגְוַע אָדָם וְאַיּֽוֹ׃ | 10 |
Koma munthu amafa nayikidwa mʼmanda, amapuma mpweya wotsiriza ndipo kutha kwake nʼkomweko.
אָֽזְלוּ־מַיִם מִנִּי־יָם וְנָהָר יֶחֱרַב וְיָבֵֽשׁ׃ | 11 |
Monga madzi amaphwera mʼnyanja kapena monga mtsinje umaphwera nuwuma,
וְאִישׁ שָׁכַב וְֽלֹא־יָקוּם עַד־בִּלְתִּי שָׁמַיִם לֹא יָקִיצוּ וְלֹֽא־יֵעֹרוּ מִשְּׁנָתָֽם׃ | 12 |
momwemonso munthu amagona ndipo sadzukanso; mpaka zamlengalenga zidzathe, anthu sadzauka kapena kudzutsidwa ku tulo tawo.
מִי יִתֵּן ׀ בִּשְׁאוֹל תַּצְפִּנֵנִי תַּסְתִּירֵנִי עַד־שׁוּב אַפֶּךָ תָּשִׁית לִי חֹק וְתִזְכְּרֵֽנִי׃ (Sheol ) | 13 |
“Aa, Inu mukanangondibisa mʼmanda ndi kundiphimba kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita! Achikhala munandiyikira nthawi, kuti pambuyo pake mundikumbukirenso. (Sheol )
אִם־יָמוּת גֶּבֶר הֲיִחְיֶה כָּל־יְמֵי צְבָאִי אֲיַחֵל עַד־בּוֹא חֲלִיפָתִֽי׃ | 14 |
Munthu akafa, kodi adzakhalanso ndi moyo? Masiku anga onse a moyo wovutikawu ndidzadikira mpaka itafika nthawi yomasulidwa.
תִּקְרָא וְאָנֹכִי אֶֽעֱנֶךָּ לְֽמַעֲשֵׂה יָדֶיךָ תִכְסֹֽף׃ | 15 |
Inu mudzandiyitane ndipo ndidzakuyankhani; inu mudzafunitsitsa kuona cholengedwa chimene munachipanga ndi manja anu.
כִּֽי־עַתָּה צְעָדַי תִּסְפּוֹר לֹֽא־תִשְׁמוֹר עַל־חַטָּאתִֽי׃ | 16 |
Ndithudi pamenepo mudzayangʼana mayendedwe anga koma simudzalondola tchimo langa.
חָתֻם בִּצְרוֹר פִּשְׁעִי וַתִּטְפֹּל עַל־עֲוֺנִֽי׃ | 17 |
Zolakwa zanga zidzakulungidwa mʼthumba; inu mudzaphimba tchimo langa.
וְאוּלָם הַר־נוֹפֵל יִבּוֹל וְצוּר יֶעְתַּק מִמְּקֹמֽוֹ׃ | 18 |
“Koma monga phiri limakokolokera ndi kuswekasweka ndipo monga thanthwe limasunthira kuchoka pa malo ake,
אֲבָנִים ׀ שָׁחֲקוּ מַיִם תִּשְׁטֹֽף־סְפִיחֶיהָ עֲפַר־אָרֶץ וְתִקְוַת אֱנוֹשׁ הֶאֱבַֽדְתָּ׃ | 19 |
monganso madzi oyenda amaperesera miyala ndipo madzi othamanga amakokololera nthaka, momwemonso Inu mumawononga chiyembekezo cha munthu.
תִּתְקְפֵהוּ לָנֶצַח וַֽיַּהֲלֹךְ מְשַׁנֶּה פָנָיו וַֽתְּשַׁלְּחֵֽהוּ׃ | 20 |
Inu mumamugonjetsa kamodzinʼkamodzi ndipo munthuyo nʼkutheratu; Inu mumasintha maonekedwe a nkhope yake ndipo mumamutaya kutali.
יִכְבְּדוּ בָנָיו וְלֹא יֵדָע וְיִצְעֲרוּ וְֽלֹא־יָבִין לָֽמוֹ׃ | 21 |
Ana ake akamalemekezedwa, iyeyo sazidziwa zimenezo; akamachititsidwa manyazi iye saziona zimenezo.
אַךְ־בְּשָׂרוֹ עָלָיו יִכְאָב וְנַפְשׁוֹ עָלָיו תֶּאֱבָֽל׃ | 22 |
Iye amangomva zowawa za mʼthupi lake ndipo amangodzilirira yekha mwini wakeyo.”