< ירמיה 5 >

שׁוֹטְטוּ בְּחוּצוֹת יְרוּשָׁלִַם וּרְאוּ־נָא וּדְעוּ וּבַקְשׁוּ בִרְחוֹבוֹתֶיהָ אִם־תִּמְצְאוּ אִישׁ אִם־יֵשׁ עֹשֶׂה מִשְׁפָּט מְבַקֵּשׁ אֱמוּנָה וְאֶסְלַח לָֽהּ׃ 1
“Pitani uku ndi uku mʼmisewu ya Yerusalemu, mudzionere nokha, funafunani mʼmabwalo ake. Ngati mungapeze munthu mmodzi amene amachita zachilungamo ndi kufunafuna choonadi, ndipo ndidzakhululukira mzinda uno.
וְאִם חַי־יְהֹוָה יֹאמֵרוּ לָכֵן לַשֶּׁקֶר יִשָּׁבֵֽעוּ׃ 2
Ngakhale anthu akulumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ komabe akungolumbira mwachinyengo.”
יְהֹוָה עֵינֶיךָ הֲלוֹא לֶאֱמוּנָה הִכִּיתָה אֹתָם וְֽלֹא־חָלוּ כִּלִּיתָם מֵאֲנוּ קַחַת מוּסָר חִזְּקוּ פְנֵיהֶם מִסֶּלַע מֵאֲנוּ לָשֽׁוּב׃ 3
Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona? Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka; munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro. Anawumitsa mitima yawo ngati mwala ndipo anakaniratu kulapa.
וַאֲנִי אָמַרְתִּי אַךְ־דַּלִּים הֵם נוֹאֲלוּ כִּי לֹא יָדְעוּ דֶּרֶךְ יְהוָה מִשְׁפַּט אֱלֹהֵיהֶֽם׃ 4
Ndiye ndinati, “Awa ndi amphawi chabe; anthu ochita zopusa. Sadziwa njira ya Yehova, sazindikira zimene Mulungu wawo amafuna.
אֵֽלֲכָה־לִּי אֶל־הַגְּדֹלִים וַאֲדַבְּרָה אוֹתָם כִּי הֵמָּה יָדְעוּ דֶּרֶךְ יְהוָה מִשְׁפַּט אֱלֹהֵיהֶם אַךְ הֵמָּה יַחְדָּו שָׁבְרוּ עֹל נִתְּקוּ מוֹסֵרֽוֹת׃ 5
Tsono ndidzapita kwa atsogoleri ndi kukayankhula nawo; ndithu iwo amadziwa njira ya Yehova, amadziwa zomwe Mulungu wawo amafuna.” Koma ayi, iwonso anathyola goli la Yehova ndipo anadula msinga zawo.
עַל־כֵּן הִכָּם אַרְיֵה מִיַּעַר זְאֵב עֲרָבוֹת יְשָׁדְדֵם נָמֵר שֹׁקֵד עַל־עָרֵיהֶם כָּל־הַיּוֹצֵא מֵהֵנָּה יִטָּרֵף כִּי רַבּוּ פִּשְׁעֵיהֶם עָצְמוּ משבותיהם מְשׁוּבוֹתֵיהֶֽם׃ 6
Choncho mkango wochokera ku nkhalango udzawapha, mmbulu wochokera ku thengo udzawawononga, kambuku adzawabisalira pafupi ndi mizinda yawo kuti akhadzule aliyense amene adzayesera kutuluka mʼmizindamo pakuti kuwukira kwawo ndi kwakukulu ndipo abwerera mʼmbuyo kwambiri.
אֵי לָזֹאת אסלוח־אֶֽסְלַֽח־לָךְ בָּנַיִךְ עֲזָבוּנִי וַיִּשָּׁבְעוּ בְּלֹא אֱלֹהִים וָאַשְׂבִּעַ אוֹתָם וַיִּנְאָפוּ וּבֵית זוֹנָה יִתְגֹּדָֽדוּ׃ 7
Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita? Ana anu andisiya Ine ndipo amapembedza milungu imene si milungu konse. Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa, komabe iwo anachita chigololo namasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere.
סוּסִים מְיֻזָּנִים מַשְׁכִּים הָיוּ אִישׁ אֶל־אֵשֶׁת רֵעֵהוּ יִצְהָֽלוּ׃ 8
Monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa, aliyense wa iwo ankathamangira mkazi wa mnzake.
הַֽעַל־אֵלֶּה לוֹא־אֶפְקֹד נְאֻם־יְהֹוָה וְאִם בְּגוֹי אֲשֶׁר־כָּזֶה לֹא תִתְנַקֵּם נַפְשִֽׁי׃ 9
Tsono ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?” akutero Yehova. “Kodi nʼkuleka kuwulipsira mtundu woterewu?
עֲלוּ בְשָׁרוֹתֶיהָ וְשַׁחֵתוּ וְכָלָה אַֽל־תַּעֲשׂוּ הָסִירוּ נְטִישׁוֹתֶיהָ כִּי לוֹא לַיהוָה הֵֽמָּה׃ 10
“Pitani ku minda yake ya mipesa ndi kukayiwononga, koma musakayiwononge kotheratu. Sadzani nthambi zake pakuti anthu amenewa si a Yehova.
כִּי בָגוֹד בָּגְדוּ בִּי בֵּית יִשְׂרָאֵל וּבֵית יְהוּדָה נְאֻם־יְהוָֽה׃ 11
Nyumba ya Israeli ndi nyumba ya Yuda onse akhala osakhulupirika kotheratu kwa Ine.”
כִּֽחֲשׁוּ בַּיהוָה וַיֹּאמְרוּ לֹא־הוּא וְלֹא־תָבוֹא עָלֵינוּ רָעָה וְחֶרֶב וְרָעָב לוֹא נִרְאֶֽה׃ 12
Iwowa ankanama ponena za Yehova kuti, “Yehova sangachite zimenezi! Choyipa sichidzatigwera; sitidzaona nkhondo kapena njala.
וְהַנְּבִיאִים יִֽהְיוּ לְרוּחַ וְהַדִּבֵּר אֵין בָּהֶם כֹּה יֵעָשֶׂה לָהֶֽם׃ 13
Mawu a aneneri azidzangopita ngati mphepo; ndipo mwa iwo mulibe uthenga wa Yehova. Choncho zimene amanena zidzawachitikira okha.”
לָכֵן כֹּֽה־אָמַר יְהוָה אֱלֹהֵי צְבָאוֹת יַעַן דַּבֶּרְכֶם אֶת־הַדָּבָר הַזֶּה הִנְנִי נֹתֵן דְּבָרַי בְּפִיךָ לְאֵשׁ וְהָעָם הַזֶּה עֵצִים וַאֲכָלָֽתַם׃ 14
Chifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akuti, “Popeza kuti anthu awa ayankhula mawu amenewa, tsono mawu anga ndidzawasandutsa moto mʼkamwa mwako ndipo anthu awa ndidzawasandutsa nkhuni zimene moto udzapserezeretu.
הִנְנִי מֵבִיא עֲלֵיכֶם גּוֹי מִמֶּרְחָק בֵּית יִשְׂרָאֵל נְאֻם־יְהֹוָה גּוֹי ׀ אֵיתָן הוּא גּוֹי מֵעוֹלָם הוּא גּוֹי לֹא־תֵדַע לְשֹׁנוֹ וְלֹא תִשְׁמַע מַה־יְדַבֵּֽר׃ 15
Inu Aisraeli,” Yehova akuti, “Ndikukubweretserani mtundu wa anthu ochokera kutali, ndi mtundu umene sunagonjetsedwepo, mtundu wakalekale umene chiyankhulo chawo inu simuchidziwa, zimene akunena inu simungazimvetse.
אַשְׁפָּתוֹ כְּקֶבֶר פָּתוּחַ כֻּלָּם גִּבּוֹרִֽים׃ 16
Zida zawo za nkhondo zapha anthu ambirimbiri; onsewo ndi ankhondo amphamvu okhaokha.
וְאָכַל קְצִֽירְךָ וְלַחְמֶךָ יֹאכְלוּ בָּנֶיךָ וּבְנוֹתֶיךָ יֹאכַל צֹאנְךָ וּבְקָרֶךָ יֹאכַל גַּפְנְךָ וּתְאֵנָתֶךָ יְרֹשֵׁשׁ עָרֵי מִבְצָרֶיךָ אֲשֶׁר אַתָּה בּוֹטֵחַ בָּהֵנָּה בֶּחָֽרֶב׃ 17
Adzakudyerani zokolola zanu ndi chakudya chanu, adzapha ana anu aamuna ndi aakazi; adzakupherani nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu, adzawononga mpesa wanu ndi mikuyu yanu. Ndi malupanga awo adzagwetsa mizinda yanu yotetezedwa imene mumayidalira.
וְגַם בַּיָּמִים הָהֵמָּה נְאֻם־יְהֹוָה לֹֽא־אֶעֱשֶׂה אִתְּכֶם כָּלָֽה׃ 18
“Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova.
וְהָיָה כִּי תֹאמְרוּ תַּחַת מֶה עָשָׂה יְהֹוָה אֱלֹהֵינוּ לָנוּ אֶת־כָּל־אֵלֶּה וְאָמַרְתָּ אֲלֵיהֶם כַּאֲשֶׁר עֲזַבְתֶּם אוֹתִי וַתַּעַבְדוּ אֱלֹהֵי נֵכָר בְּאַרְצְכֶם כֵּן תַּעַבְדוּ זָרִים בְּאֶרֶץ לֹא לָכֶֽם׃ 19
Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.”
הַגִּידוּ זֹאת בְּבֵית יַעֲקֹב וְהַשְׁמִיעוּהָ בִיהוּדָה לֵאמֹֽר׃ 20
“Lengeza izi kwa ana a Yakobo ndipo mulalikire kwa anthu a ku Yuda kuti,
שִׁמְעוּ־נָא זֹאת עַם סָכָל וְאֵין לֵב עֵינַיִם לָהֶם וְלֹא יִרְאוּ אָזְנַיִם לָהֶם וְלֹא יִשְׁמָֽעוּ׃ 21
Imvani izi, inu anthu opusa ndi opanda nzeru, inu amene maso muli nawo koma simupenya, amene makutu muli nawo koma simumva.
הַאוֹתִי לֹא־תִירָאוּ נְאֻם־יְהֹוָה אִם מִפָּנַי לֹא תָחִילוּ אֲשֶׁר־שַׂמְתִּי חוֹל גְּבוּל לַיָּם חָק־עוֹלָם וְלֹא יַעַבְרֶנְהוּ וַיִּֽתְגָּעֲשׁוּ וְלֹא יוּכָלוּ וְהָמוּ גַלָּיו וְלֹא יַעַבְרֻֽנְהוּ׃ 22
Kodi simuyenera kuchita nane mantha?” Akutero Yehova. “Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga? Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja, malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo. Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo; mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.
וְלָעָם הַזֶּה הָיָה לֵב סוֹרֵר וּמוֹרֶה סָרוּ וַיֵּלֵֽכוּ׃ 23
Koma anthu awa ndi nkhutukumve ndiponso a mitima yowukira; andifulatira ndipo andisiyiratu.
וְלֹֽא־אָמְרוּ בִלְבָבָם נִירָא נָא אֶת־יְהוָה אֱלֹהֵינוּ הַנֹּתֵן גֶּשֶׁם וירה יוֹרֶה וּמַלְקוֹשׁ בְּעִתּוֹ שְׁבֻעוֹת חֻקּוֹת קָצִיר יִשְׁמָר־לָֽנוּ׃ 24
Sananenepo mʼmitima mwawo kuti, ‘Tiyeni tizipembedza Yehova Mulungu wathu. Kodi suja amatipatsa pa nthawi yake mvula yachizimalupsa ndi yamasika. Iye salephera konse kutipatsa nyengo ya kholola.’
עֲוֺנוֹתֵיכֶם הִטּוּ־אֵלֶּה וְחַטֹּאותֵיכֶם מָנְעוּ הַטּוֹב מִכֶּֽם׃ 25
Koma zolakwa zanu zalepheretsa zonsezi; ndipo machimo anu akumanitsani zabwino.
כִּי־נִמְצְאוּ בְעַמִּי רְשָׁעִים יָשׁוּר כְּשַׁךְ יְקוּשִׁים הִצִּיבוּ מַשְׁחִית אֲנָשִׁים יִלְכֹּֽדוּ׃ 26
“Pakati pa anthu anga pali anthu ena oyipa amene amabisalira anzawo monga amachitira mlenje mbalame ndiponso ngati amene amatchera misampha kuti akole anthu anzawo.
כִּכְלוּב מָלֵא עוֹף כֵּן בָּתֵּיהֶם מְלֵאִים מִרְמָה עַל־כֵּן גָּדְלוּ וַֽיַּעֲשִֽׁירוּ׃ 27
Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengo ngati zikwere zodzaza ndi mbalame. Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera.
שָׁמְנוּ עָשְׁתוּ גַּם עָֽבְרוּ דִבְרֵי־רָע דִּין לֹא־דָנוּ דִּין יָתוֹם וְיַצְלִיחוּ וּמִשְׁפַּט אֶבְיוֹנִים לֹא שָׁפָֽטוּ׃ 28
Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala. Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire; saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino, sateteza ufulu wa anthu osauka.
הַֽעַל־אֵלֶּה לֹֽא־אֶפְקֹד נְאֻם־יְהֹוָה אִם בְּגוֹי אֲשֶׁר־כָּזֶה לֹא תִתְנַקֵּם נַפְשִֽׁי׃ 29
Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi? Kodi ndisawulipsire mtundu woterewu? Akutero Yehova.
שַׁמָּה וְשַׁעֲרוּרָה נִהְיְתָה בָּאָֽרֶץ׃ 30
“Chinthu chothetsa nzeru ndi choopsa kwambiri chachitika mʼdzikomo:
הַנְּבִיאִים נִבְּאוּ־בַשֶּׁקֶר וְהַכֹּהֲנִים יִרְדּוּ עַל־יְדֵיהֶם וְעַמִּי אָהֲבוּ כֵן וּמַֽה־תַּעֲשׂוּ לְאַחֲרִיתָֽהּ׃ 31
Aneneri akunenera zabodza, ndipo ansembe akuvomerezana nawo, ndipo anthu anga akukonda zimenezi. Koma mudzatani potsiriza?

< ירמיה 5 >